Saturday, July 2, 2022
  • About Us
  • ImagiNATION
  • Rate Card
  • Contact Us
The Nation Online
Advertisement
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
No Result
View All Result
Home Chichewa

Akufuna mwana

by Staff Writer
23/05/2015
in Chichewa
2 min read
0
Share on FacebookShare on TwitterShare on WhatsAppShare on LinkedinLinkedinShare via Email

Akufuna mwana
Zikomo Gogo
Banja ndi mwamuna wanga lidatha mu 2011. Ndidapeza mwamuna wina yemwe timamvana ndipo tidakayezetsa komwe adatipeza kuti tilibe kachilombo koyambitsa Edzi. Vuto ndi lakuti bwenzi langalo limakonda zogonana komanso limandiletsa kuchita za kulera. Wina adandiuza kuti bwenzi langalo lili ndi mkazi koma nditamufunsa adakana. Tsiku lina ndidaimba foni 5 koloko mbandakucha ndipo ndidamva kulira kwa mwana wakhanda. Nditamufunsa adakana ndipo adati ndi wa khomo loyandikana nalo, nadula foni nthawi yomweyo. Ndizimukondabe?
R,
Chiradzulu

R,
Mwakumana ndi chilombo cha bodza. Wakunamizani kuti akufuna mwana chonsecho pansi pa mtima akudziwa kuti akakupatsani mwana adzakuthawani nkupitiriza kukhala ndi mkazi wake. Wakunamizaninso kuti mwana amalira ndi woyandikana nawo nyumba. Ngati zili zoona, bwanji adadula foni? Asakutayitseni nthawi ameneyo.

Ndimamupitirira
Wawagogo,
Ndili ndi zaka 17 ndipo pali mnyamata wina wa zaka 20 yemwe akundifuna. Ndimamukonda koma vuto ndi lakuti iyeyo ndi wamfupi kuposa ine. Ndimachita manyazi ndikamayenda naye. Ndimulole?
C

C,
Sindikuonapo vuto loti musamulolere! Kutalika kukhale nkhani? Chikondi chimachoka mumtima ndipo sichiyenera kuona ngati wina ndi wamtali kapena wamfupi, woonda kapena wonenepa, woona kapena wosaona ndi zina zotero. Chabwino nchiyani kuti mudzapeze mnyamata wamtali ngati inu kapena kukuposani koma alibe chikondi kapena kukhala ndi mwamuna ameneyu yemwe amakukondani nanunso mukumukonda? Muloleni ameneyo basi.

Amakonda ndalama
Anatchereza,
Ndakhala paubwenzi ndi msungwana wina koma vuto lake akuoneka wokonda ndalama. Tikangokumana, amandipempha ndalama. Timalankhulana nthawi zambiri pafoni koma mwezi ukangotha amati tikumane. Kodi ichi ndi chikondi?
M,
Lilongwe.

M,
Ameneyo sakuthandizani. Mkazi woika ndalama patsogolo si wabwino. Taonani akuonetsa mawanga ake muli pachibwenzi nanga mukadzakwatirana zidzatha bwanji? Mudzaona kuti pakati pa mwezi mavuto okhaokha m’banja. Koma ukangotha mwezi sikusekerera kuchitsakano kwake. Mpeweni.

Mtendere palibe
Kuyambira pomwe tidalowa m’banja, sitinathe mwezi tili pamtendere. Iye amati ine si mwamuna amene iye ankakhumba. Iyetu ndi wobadwanso mwatsopano ndipo akati agwe ndi pemphero, mukhoza kuona kuti ayi, mayi amapemphera uyu. Iye amati zivute zitani tidzasiyana basi. Kodi ndidikire adzandisiye, kapena ndilowere kwanga? Inetu ndimamukonda!
M,
Blantyre.

M,
Mpovuta kukuthandizani chifukwa simukufotokoza ngati banja lanu ndi lomanga kapena mudangolowana. Mwati mkazi wanu ndi wobadwanso mwatsopano, kutanthauza kuti mmene pamene mumakwatirana adali wachikunja. Kodi inu pankhani yopemphera muli pati? Mumapemphera kapena ayi? Mwina inu zochita zanu nzachikunja nkuona mkazi wanu akuti zivute zitani mudzasiyana basi. Ngati banja, khalani pansi nkukambirana kuti vuto m’banja lanu lagona pati ndipo muchitenji kuti banja lanulo libadwenso mwatsopano ndipo liyambenso kuyenda myaaa!

Ofuna mabanja
Ndili ndi zaka 21, ndili ndi mwana mmodzi ndipo ndimafuna mwamuna. 0881838385

Ndili ndi zaka 25 ndipo ndikufuna sugar mummy. 0888496090

Ndili ndi zaka 20, ndikufuna sugar mummy. 0999393177

Ndili ndi zaka 24 ndipo ndikufuna mkazi wa zaka za pakati pa 25 ndi 40. 0888684380

Ndili ndi zaka 25 ndikufuna mkazi wa zaka 20 mpaka 22. 0888494570
Ndili ndi zaka 35 ndikufuna mkazi wa zaka 36 kupita mtsogolo. 0995311249

Ndili ndi zaka 47, ndikufuna mkazi wachilungamo. 0888693022

Ndili ndi zaka 32 ndikufuna mkazi wa zaka 20, woopa Mulungu. 0881182125

Previous Post

Disabled persons demand accessible health services

Next Post

Tame Mwawa: Chiphwanya wa Tikuferanji

Related Posts

Chilima: Change the mindset toward development
Nkhani

A Chilima abwera poyera

July 1, 2022
Nkhani

Achilima awachepetsera mphamvu zaulamuliro

June 24, 2022
Katundu wa a Mtambo adali kuseri kwa ofesi za khonsolo
Nkhani

Agona ku maofesi a khonsolo ya Mzuzu

June 4, 2022
Next Post
Chiphwanya: Mnyamata wazikhakhali pa Tikuferanji

Tame Mwawa: Chiphwanya wa Tikuferanji

Opinions and Columns

My Turn

Following spouse is no crime

July 1, 2022
Rise and Shine

Create your personal brand

June 30, 2022
Business Unpacked

We can do without some levies in fuel price

June 29, 2022
My Turn

US court threatens women’s rights

June 29, 2022

Malawi-Music.com Top10

Trending Stories

  • Entrance to one of the VP’s official residences in Blantyre: Mudi House

    New VP houses draw criticism

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  •  Malawi credit Status at risk

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Britain squeezes Zuneth Sattar

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • 4 DPP MPs disown Nankhumwa injunction

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Ex-MPC boss sues for unfair dismissal

    0 shares
    Share 0 Tweet 0

  • Values
  • Our Philosophy
  • Editorial policy
  • Advertising Policy
  • Code of Conduct
  • Plagiarism disclaimer
  • Disclaimer
  • Privacy Policy
  • Terms of use

© 2022 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation

© 2020 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

This website uses cookies. By continuing to use this website you are giving consent to cookies being used. Visit our Privacy and Cookie Policy.