Nkhani

Akuganizira mwana kupha bambo ake

Listen to this article

Kudalembedwa m’Baibulo kuti masiku otsiriza mitundu idzaukirana ndipo ana nawo adzaukira makolo awo koma osati momwe zafikira Mponda T/A Nyoka m’boma la Mchinji.

Mwana wina kumeneko akumusunga m’chitokosi pomuganizira kuti adapha bambo ake pankhani ya malo.death

Mneneri wapolisi m’bomalo, Moses Nyirenda, watsimikiza kuti apolisi akusunga Christopher Chirwa wa zaka 56 pomuganizira kuti adapha bambo ake Pataleo Chirwa wa zaka 90, powanyonga pakhosi malingana nzotsatira za kuchipatala.

“Ndi mmene nkhani yonse ilili, tikukaikira mwana wa malemuyu pa zifukwa zingapo. Choyamba, adali limodzi tsiku lomwe malemuyo adakapezeka atafa. Chachiwiri, malemuyo adapezeka ali ndi chingwe m’khosi koma pamalo oti munthu sangadzimangilire ndipo chomaliza, achipatala adatsimikiza kuti malemuyo adafa kaamba kokhinyika,” adatero Nyirenda.

Nthawi zambiri, anthu omwalira kaamba kodzimangilira, amapezeka akulendewera, kutanthauza kuti sikelo ya thupi lonse imathera pakhosi pomwe padina chingwe chodzimangiliriracho.

Chomwe chidazizwitsa anthu pa imfa ya bamboyu nchakuti adapezeka atakoledwa chingwe m’khosi ngati adadzimangirira koma thupi lonse lili pansi ngati wakhala tsonga ndipo nthambi yomwe idagwira chingweyo ili yowetezeka.

Patsikulo, lomwe ndi pa 16 July, 2016 mmawa, Nyirenda adati mwanayo adauza bambo ake kuti  apite kudimbako akaunikirane za malire koma bamboyo sadabwerere mpaka pomwe adapezeka atafa m’munda wina wa mphepete mwa njira.

Nyirenda adati apolisi atafika pamalopo adatenga mtembo wa bamboyo nkupita nawo kuchipatala kuti akaupime pomwe mwanayo adapita naye kupolisi kuti afufuze nkhani yonse mwaufulu.

Iye adati mpaka pano apolisi akadachita kafukufuku pankhaniyo kuti apeze umboni okwanira asadapite ndi oganiziridwayo ku bwalo la milandu komwe akuyembekezeka kukayankha mlandu wakupha. n

Related Articles

Back to top button