Nkhani

Akugulitsa magazi ku Mangochi

Listen to this article

Kaamba ka kusowa magazi pachipatala cha Mangochi, anthu ena ozungulira chipatalacho akugulitsa magazi awo kwa odwala osoweka mwazi pamtengo wa K7 000 pa lita.

 Izi zidadziwika pamene mayi wina, Hawa Ntila, adabereka mapasa ku Makanjira adatumizidwa kuchipatalacho ndipo Lamulungu adapereka K7 000 ndipo Lolemba adaperekanso ndalama yomweyo kuti apeze magazi.

Mneneri wa unduna wa zaumoyo Henry Chimbali adatsimikza nkhaniyi.

Ntila amagwira ntchito kubungwe lothandiza amayi pa za malamulo la Women and Law in Southern Africa (Wilsa).

Mkulu wabungweli Seodi White adati adakwiya nazo.

“Mpaka K14 000? Ndidafunsa kuti chikuchitika n’chiyani,” adatero iye.

Ena mwa ogulitsa magaziwo ndi anyamata a kabaza pachipatalapo.

Bungwe loona za magazi la Malawi Blood Transfusion lati vutoli lagwa chifukwa anthu sakupereka magazi mokwanira.

Related Articles

Back to top button
Translate »