Chichewa

Akumanga mvula ndani?

Listen to this article

Tsikulo pa Wenela padali kutentha osati masewera. Zimachita kukhala ngati dziko likutha, Jahena akutsikira pansi pompano.

N’chifukwa khamu lidafika apo lidali kukonkha kummero. Mkulu wina adafika ndi mwana wake amenenso amamwa chakumwa chake. Mwanayo adali kutuluka thukuta ngati mtsinje wa Shire, inde uja wauma kuti magetsi avute chonchi.

art

Nanga magetsi kuzima 5 koloko mmawa, nkuyaka 12 koloko usiku, amenewa akuganiza kuti mfiti nazo zimalira magetsi? Tikudabwa zedi kuti n’chifukwa chiyani kampani imeneyi kukadali ogwira ntchito. Amachitako chiyani?

Mwana adazunzika nalo thukuta, limene limatsikira m’masaya.

Adapukuta thukuta, koma ngati alire.

Amvekere: “Daddy, I am melting!”

Ana amasiku ano Chingerezi! Ndikumbuka masiku amenewo ndisanatulukire pawindo kusukulu kwathu kwa Kanduku, Chingerezi chimene ndinkadziwa ndi ‘please teacher mayi go out basi!

“Ndiye ndikumva kuti Moya Pete anadzibera yekha zikwama paja anagona padepoti!” adayamba milandu ina Abiti Patuma.

Kaya nkhanizi amazitenga kuti? Tonse tidangoti kukamwa yasaaa!

“Moya Pete simukumudziwa, nthuni. Wadzibera yekha zikwama kuti muone ngati akuvutika,” adapitiriza.

Aliyense maganizo adali pakutentha. Adatulukira Moya Pete wa Dizilo Petulo Palibe, Lazalo Chatsika wa Male Chauvinist Pigs komanso Atipatsa Likhweru wa Ukafuna Dilu Fatsa. Amene padalibe ndi Adona Hilida aja adathawa nkhondo ya Angitawo.

Onsewo thukuta lili kamukamu.

“Koma kutentha kumeneku bwanji? Akumanga mvula ndani kwambiri?” adafunsa Moya Pete atakhalira kereti.

“N’zochita kufunsa? Mukumanga mvula ndinu. Tangomva kuti mwaotcha uvuni kuti nanunso mumange nyumba ya manda momwemo muja adachitira Mfumu Mose,” adatero Lazalo.

Moya Pete adakwiya kwambiri.

“Koma udzasiya makani, iwe? Tonse tikudziwa kuti ukumanga mvula ndiwe. Cholinga chako pano pa Wenela anthu asalime, adzavutike ndi njala kenako udzandichotse pampando. Wagwa nayo kwambiri,” adatero iye.

Atipatsa adangoseka: “Zoona iwe, Lazalo, wamanga mvula. Ukufuna ukalawe kumpanda. Ulira. Uli ndi mwayi gogo wanga Che Polamani adapita.”

“Zikugwirizana bwanji?” adafunsa Abiti Patuma.

Enanutu mwina simukuwadziwa Che Polamani. Adali sing’anga wovuta zedi. Amatha kuyala mphasa pamstinje nkumaothera dzuwa koma osamira. Inde, ankatha kuyanika malaya m’malere popanda dzuwa.

Posakhalitsa idatulukira nyakwawa Wenela. Nyakwawayo imasowa kwambiri, tidadabwa kuti idatilemekeza bwanji tsikulo.

“Ndamva mukukangana za mvula. Musadandaule, tikuimanga ndife. Zaka zonsezi mumatipatsa ife nzika zitupa zogulira feteleza, chaka chino mwatimana ndiye tiona kuti mvula yanuyo ichokera kuti,” idatero mfumuyo.

Tonse tidangoti kukamwa kakasi.

“Kapena tipite ku Khuluvi tikathire nsembe kwa Mbona?” ndidafunsa.

Onse adangoseka, kudzimvera chisoni.

Gwira bango, upita ndi madzi mwaiwe!n

Related Articles

Back to top button
Translate »