Chichewa

Akupha makwacha ndi kuchulukitsa mbuzi za chi ‘boer’

Mmalo mopeza K20 000 ku mbuzi yaikulu bwino yachikuda imene imatenga miyezi yosachepera 6 kuti ikule bwino, Allan Kalimasiya wa ku Chipoka m’boma la Salima amapeza K50 000 kuchokera ku mwana wa mbuzi ya chi ‘boer’ mmodzi wa miyezi itatu yokha powagulitsa alimi anzake kuti azikaweta. Iye adafotokoza mmene amachulukitsira mbuzi za mtunduwu kuti zikhale zosasakanikirana ndi ntundu wina, mmene akupindulira ndi ulimiwu komanso mmene amawetera. ESMIE KOMWA adacheza naye motere:

Kodi kuyamba kuchulukitsa mbuzi za chi ‘boer’ mudayamba liti?

Ndidayamba kuchulukitsa mbuzi za mtunduwu mu 1996.

Nanga chiyambi chake chidali chotani?

Kalimasiya pakati pa mbuzi za chi ‘boer’ zimene akuchulukitsa

Kalero ndimaweta mbuzi za mtunduwu koma zokwatitsa ndi zachikuda.

Nditaweta kwa nthawi yaitali ndidachita mwayi pamene a boma adandisankha kuti ndikhale mmodzi mwa alimi ochulukitsa mbewu ya ntunduwu.

Ndidapereka ndalama yochepa chabe ndipo adandipatsa mbuzi za mtunduwu zosasakaniza zokwana 5 zochokera m’dziko la South Africa.

Ndidayamba kuchulukitsa malingana ndi luso limene adandiphunzitsa kuti zisachepe mphamvu komanso zisasakanikirane ndi za mtundu wina.

Kodi mumachulukitsa mbuzizi motani?

Basi chachikulu ndikuonetsetsa kuti zisamakwerane paubale monga mwana ndi bambo kapena ndi mayi kapena gogo komanso zisasakanikirane ndi za mtundu wina.

Kuti izi zitheke ndimayenera kumabweretsa atonde ochokera m’mabanja ena koma a mtunduwu mukhola ndikumakweretsa zazikazizo.

Nanga atonde atsopanowa mumawapeza motani?

Amandipezera a boma ndipo ndimagula pa mtengo wa K80 000 tonde mmodzi.

Kodi ubwino wa mbuzi zimenezi ndi wotani?

Zimakula mwachangu chifukwa masiku 90 okha zimakhala zafika poti ikhoza kupereka nyama yogwirika ndithu ndipo mlimi akhoza kugulitsa pa mtengo wabwino, zimakula kwambiri pafupifupi makilogalamu 70, zimaswa kawiri pachaka ndipo zimaswa mapasa choncho mbuzi yaikazi imodzi imanditulutsira ana 4 pachaka.

Ndikawagulitsa ngati mbewu kwa alimi kuti azikaweta pa mtengo wa K50 000 ndiye kuti mbuzi imodzi imanditulutsira K200 000 pa chaka.

Nanga misika mumaipeza motani?

Ndinene zoona sindisowa misika ndipo anthu ogula akundichulukira.

Anthu m’zigawo zonse za m’dziko muno ngakhale maiko ozungulira monga Tanzania amadzagula. Ndimatumiza m’maboma onse a m’dziko muno pamene ena amachita kubwera pakhomo pompano kudzagula ndipo dzana lomweli ena amakanganirana kuti agule ndipo ena atenga ana osaleka kuyamwa.

Kodi chiyambireni ulimiwu mwapindula motani?

Ndagwira ntchito kwa zaka zochuluka mmbuyomu koma nditasiya ndi kuyamba kulimbikira ulimiwu ndidabwa kuona kuti ndayamba kugwira ndalama zochuluka zimene pamene ndidali pa ntchito sindidazigwirepo.

Ndagula famu ya mahekitala okwana 10 pamene ndaikapo zipangizo za mthirira monga zitsime zakuya, mathanki ndi makina oyendera mphamvu ya dzuwa ndipo ndikuchitirapo ulimi wa zipatso monga mango a chizungu.

Kuonjezera apo, nyumba imene ndikukhalayi ndamanga kuchokera mu mbuzi zomwezi.

Nanga chinsinsi chanu chagona pati?

Chinsinsi ndi kulondoloza ndondomeko kuti ndizitulutsa mbewu yabwino alimi akatenga asakhumudwe nayo.

Ndidazimangira makola abwino a m’mwamba ndi ofolera bwino kuti zizitetezeka ku matenda, ndimazipatsa chakudya chakasakaniza, nthawi iliyonse ndimaziyang’anitsitsa kuti ndione ngati zonse zili bwino ndipo ndikapeza kuti ina siyikupeza bwino ndimaithandiza mwachangu.

Pali mankhwala monga opha nyongolotsi ndi ena amene mlimi wa ziwetozi amayenera kukhala nawo ndi kumamwetsa mbuzi zake motsatira ndondomeko chifukwa kupanda kutero umadzangozindikira ina yafa.

Ngakhale alimi anga ndimawalangiza zonse zofunika ku ulimiwu asadatenge mwachitsanzo mmene angadziwire kuti mbuzi ikudwala ndi zimene akuyenera kuchita akaona izi.

Nanga ndi zakudya zanji zimene mumadyetsera mbuzi za mtunduwu?

Timadyetsera zakudya zopezeka kwathu konkuno mosavuta bola zikhale zosiyanasiyana chifukwa mbuzi zimasankha chimene zikufuna kudya pa nthawi imeneyo.

Zakudyazi ndi monga kholowa, makoko kapena masamba a mtedza, makoko a soya,udzu, madeya, lukina ndi michere ina yoonjezera.

Nanga masomphenya anu pa ulimiwu ndi otani?

Ndikufuna kutsogoloku ndizichulukitsa kwambiri kuti alimi azipeza mbewuyi mosavuta komanso ndifikire zinthu zina zimene sindidazifikire.

Related Articles

Back to top button