Chichewa

Akupindula ndi chimanga chachiwisi

Pamene alimi ambiri akugulitsa chimanga chouma pa mtengo wotsika, mlimi wa chimanga chachiwisi ku Area 25 m’boma la Lilongwe Kandida Kalisito akupha makwacha ndi chimanga chachiwisi. Mlimiyu ali ndi malo amene amaotcherapo chimanga chake pa munda pomwepo ndipo akuti nthawi zambiri amagulitsa chootcha chifukwa ndi m’mene muli phindu lochuluka. ESMIE KOMWA adacheza naye motere:

Kodi kulima chimanga chachiwisi mudayamba liti?

Ndidayamba ulimiwu mu 2002.

Nanga chidakuchititsani n’chiyani kuti muyambe ulimiwu?

M’chaka cha 2001 kunali njala kotero a bungwe lina la Katolika mogwirizana ndi la European Union(EU) anabwera kudzaphunzitsa anthu ulimi wothirira ndipo pa nthawiyo pa malo pano panali anthu okwana 14.

Mabungwewa anauza anthu oyambirirawo kuti awonjezere anthu ena omwe akufuna kuyamba ulimiwu ndipo ine ndinali m’gulu la anthu owonjezeredwawo.

Chiyambireni ulimi wa chimanga chachiwisiwu mwapindula motani?

Ulimiwu wandipindulira kwambiri chifukwa ndaphunzitsa ana anga atatu onse pano ali pa ntchito ndipo akudzidalira, ndamanga nyumba za lendi ndipo panopa chilakolako changa n’chogula galimoto.

Nanga chinsinsi chanu kuti muzipindula motere chagona pati?

Chinsinsi changa ndikusamalira bwino mbewuyi kuti ituluke ikuluikulu bwino ndi yapamwamba komanso kugulitsa china chootcha.

N’chifukwa chiyani mumagulitsa chimanga chachiwitsi osati kudikira kuti chiume?

Chimanga chouma chimakhala chotsika mtengo kwambiri kusiyana ndi chachiwitsi kotero kugulitsa chotero n’kungotaya mphamvu zako pachabe.

Tangoganiza panopa makamaka kwa ine ndimagulitsa kwambiri chootcha, chimanga chimodzi ndikumagulitsa pa mtengo wa K200, K150 ndi K100 pamene chouma pa kilogalamu ndi K200.

Kodi pa chaka mumalima kokwana kangati?

Kamakwana katatu koma ndimaonetsetsa kuti malo anga ndiwaike m’magawo ndikubzalanso nthawi zosiyana n’cholinga choti m’chaka chonse ndizikhala ndikugulitsa.

Nanga mumagwiritsa ntchito njira yanji ya mthirira?

Ndimagwiritsa ntchito ya m’makhwawa. Ndili ndi khwawa lalikulu, komanso ma pump amene ndimagwiritsa ntchito petulo kuti ndilize injini. Ndimalumikiza mapiyipi ku pampu ndipo mbali ina ndimalumikiza ingini. Mapayipi ena amatenga madzi mu mtsinje pamene ena amakathira madzi mu khwawa muja ndipo likadzadza ndimapatutsira ku mbewu pokumba timakhwawa ting’onoting’ono.

Kodi si ntchito yolemetsa imeneyi?

Ndiyophweka kusiyana ndiyogwiritsa ntchito ma water cane kapena ma treadle pump n’chifukwa chake tinasiya kugwiritsa ntchito kalekale zinthu zoterezi.

Ndinu munthu wa mayi koma mukuoneka mukuchita zinthu zomwe amayi ambiri sangachite, mungawalangize zotani amayi anzanu?

Ndimakonda kuwauza amayi anzanga kuti sakuyenera kumakhala amanja lende podalira amuna awo okha ndipo pakutero adzachepetsa umphawi m’dziko muno ndipo m’maanja awo. Chinthu china munthu ukakhala wokangalika umakhala ndi masomphenya ndipo umayetsetsa kuwakwaniritsa  pakutero umakhala munthu osangalala pamene ukakhala wa manja lende umakhala otsirira mpaka kalekale.

Nanga ndimavuto anji omwe mumakumana nawo mu ulimiwu?

Vuto limene timakumana nalo ndi la mbozi. Nthawi zina zikachulukitsa timayenera kupopera sabata iliyonse kuti tipulumutse mbewu zathu choncho ndalama yochuluka imalowa ku mankhwala. Vuto lina limene timakumana nalo chaka chilichonse ndi kuphwa kwa madzi mu mtsinje umene timatengako madzi makamaka m’miyezi yotentha.  Aunduna wa zamalimidwe anayamba kutikumbira damu kuti tisamakumane ndi mavuto oterewa, koma sanamalidzitse kotero tinakakonda akanamalizitsa kuti mwina vutoli lichepe.

Related Articles

Back to top button