Nkhani

Akwapula mphunzitsi wochita ‘chisembwere’

Maphunziro a ana a Sitandade 8, adasokonera Lolemba pasukulu ya pulaimale ya Kalira, yomwe ili m’mudzi mwa Kanyera ku Mtakataka m’boma la Dedza.

Izi zidachitika pomwe wachiwiri kwa mphunzitsi wamkulu pasukulupo Owen Kalolo adakwapulidwa pomuganizira kuti amachita chibwenzi ndi mkazi wa mwini.

Zidatengera apolisi ndi aphunzitsi anzake kumuleletsa. Ndipo aphunzitsi anzake adanenetsa kuti saphunzitsanso malire ake chitetezo chawo chibwerere m’chimake chifukwa wokwapula mphunzitsiyo sadanjatidwe.

Mwini mkaziyo Sitivero John, akuti adapita pasukuluyi ndi kukwapula mphunzitsiyo ndi waya yemwe kwinaku akumunena kuti amagona ndi mkazi wake iye ali ku South Africa.

Malinga ndi omwe adatitsina khutu pankhaniyi wa m’mudzimo, mapokosowo adayambika m’mawa wa Lolemba, aphunzitsi ali pa kamsonkhano kawo.

“Tidangoona kwatulukira bambo wolusayo atanyamula waya wa mtundu wa y16 ndi kumukwapula mphunzitsiyo,” adalongosola iye.

Iye adati apa mpomwe aphunzitsi anzake adalowererapo kuopetsa kuti akadamuvulaza kwambiri.

“Kuchoka apa kudabweranso apolisi a ku Mtakataka komanso mkulu woyan’ganira maphunziro kudera la Mankhamba kudzaziziritsa zinthu,” iye adatero.

Polankhulapo, mkulu woona za maphunziro m’bomalo, George Ngaiyaye adatsimikiza za nkhaniyi koma adati pakadalipano ana adayamba kuphunzira zomwe zikusonyeza kuti chitetezo cha aphunzitsi chilli m’malo mwake.

“Nkhaniyi tsopano ili m’manja mwa apolisi ndipo ana akuphunzirano bwino,” adalongosola Ngaiyaye.

Wachiwiri kwa mneneri wa polisi m’bomalo Cassim Manda yemwe adakafikako kusukuluyi adatsimikizira Msangulutso kuti chitetezo cha aphunzitsitsiwo chili m’malo mwake ndipo adayambanso kuphunzitsa.

Manda adati Kalolo ndi John akhala ali pa chinansi kwa zaka 6 ndipo ubale wawo umapitirirabe ngakhale pomwe John adapita m’dziko la South Africa.

“Koma nkhani idakhota pomwe mkazi wa John adampatsa Kalolo munda kuti alimepo zomwe sizidasangalatse abale ndipo adayamba kulankhula zoti awiriwo adali pa ubwenzi wamseri,” adalongosola Manda.

Malinga ndi Manda, John atabwera chaka chino, adayamba kufufuza ndipo adadikira kuti sukulu zitsegulire kuti akamukhape Kalolo nthawi ya sukulu ngakhale adalibe umboni.

“Pakadalipano tikusakasaka komwe kuli John komanso kusukuluko kwapita apolisi chifukwa John-yu adalonjeza kuti sasiyira pomwepa zaupanduzi,” adatero Manda.

Ndipo adanenetsa kuti sukuluyo siyidatsekedwe.

Kalolo yemwe ali ndi zaka 29, amachokera m’mudzi mwa Maliwa, Mfumu Chilikumwendo pomwe John wa zaka 35, amachokera m’mudzi mwa Kanyera, Mfumu Kachindamoto, m’boma la Dedza.

Related Articles

Back to top button