Nkhani

Akwenya woganiziridwa kusowetsa anthu pa KCH

Tsoka sasimba. Mayi wina wa ku Area 25 mumzinda wa Lilongwe adaona zakuda Lolemba lapitali atapita kuchipatala chachikulu cha Kamuzu Central (KCH) mumzindawu kukaona mwana wa mnzake woyandikana naye nyumba.

Mnzakeyu adagonekedwa m’chipinda cha ana pachipatalachi.

Mayiyu, yemwe apolisi sadatitchulire dzina, akuti atafika muchipindacho Lamulungu lapitali adapempherera mwana wina modabwitsa ndipo kuti pochoka, adachoka ndi mwana wodwala mmodzi pamodzi ndi womuyang’anira. Awiriwo sadabwererenso m’chipatalamo.

Ndipo Lolemba mayiyu atafikanso m’chipindacho, anthu adamuzindikira ndipo adamukwenya kwinaku akuti ndi wa Sataniki ndipo alongosole bwino za kusowa kwa awiriwo.

Malinga ndi mneneri wa polisi ya Lilongwe, Kingsley Dandaula, anthu okwiyawo adatengera mayiyo kupolisi ya Area 33 yomwe ili pafupi ndi chipatalacho komwe mwatsoka kudalibe maofesala ndipo adaperekedwa m’manja mwa alonda apachipatalapo kuti amusunge.

Malinga ndi zithunzi zomwe taona, gulu lina la anthu lidasonkhana panja pa ofesi ya alondawo.

Dandaula adati apa mpomwe galimoto ya polisi ya Lingadzi idabwera kudzamutenga mayiyo pomuteteza ku anthu olusawo.

Koma Dandaula adatsutsa kwa mtu wa galu zoti mayiyo ngwa Sataniki.

“Mayiyu ngwabwinobwino ndipo adapita kuchipatala monga zimakhalira, koma kuti adangomunamizira. N’zabodza, si Wasataniki monga anthu akunenera,” adatero Dandaula.

Iye adati chifukwa cha nkhaniyi wapolisi mnzawo wa pa Area 33, adaitanidwa kukakumana ndi mmodzi mwa akuluakulu apachipatalachi Lachitatu lapitali kuti akauzidwe mvemvemve pa zomwe zidachitika patsikulo.

Polankhula ndi mkulu woyendetsa chipatalachi, Jonathan Ngoma, adati oyang’anira mbali ya ana sadamuuze tsatanetsatane wa momwe nkhaniyi idayendera.

“Sadandiuze momwe zidayendera patsikulo,” adatero Ngoma.

Koma mmodzi mwa odikirira odwala m’chipinda cha ana pachipatalachi, Jessica Phiri, yemwe mwana wake adali pabedi limodzi ndi mwana wopemphereredwayo, adati tsiku la Sabatalo, m’chipindamo mudachitika zoopsa.

Phiri adati munthuyo adauza amayi onse kuti atsinzine kenako adayamba kupemphera koma pasadathe nthawi, namwino yemwe adali m’chipindacho adabwera n’kuuza amayiwo kuti ayang’ane aone zomwe amachita mayi wopempherayo.

“Tidali odabwa kuona mmene amadinira pamimba pa mwanayo uku akupemphera kenako namwino uja adamuuza kuti aonetse kalata ya chilolezo chodzapempherera odwala koma adalibe ndipo adamuthamangitsa,” adatero Phiri.

Iye adati posakhalitsa mayiyo adabwerera n’kuyamba kukambirana ndi wodikirira mwana uja kenako adatengana ponena kuti akukadya chakudya kukhitchini, koma onse sadabwererenso.

Phiri adati mmawa mwa tsiku linzakelo mayi uja adabweranso ndipo mwamwayi adakumananso ndi namwino yemweuja koma atamufunsa za anthu omwe adatenga dzulo lake adayankha kuti sakudziwapo kanthu ndipo yankholi lidakwiyitsa anthu omwe adali m’chipindamo.

“Tonse tidali odabwa kuti yankho lake lidali limeneli moti anthu adayamba manong’onong’o kenako achitetezo adabwera n’kumuuza kuti atuluke azipita koma anthu adamuthamangira akumuwowoza mpaka kumsewu,” adatero mayiyo.

Namwino yemwe amanenedwayo adatsimikiza kuti iye adadabwa ndi pemphero lomwe mayiyo amachita pamwanayo nkuona adauza amayiwo kuti ayang’ane ndipo adati palibe wachipatala aliyense yemwe adadziwa zoti mayiyo wabwereranso atathamangitsidwa.

“Tidadzadabwa kuona kuti wodwala mmodzi ndi womudikirira sakuoneka ndipo titafunsa, otsalawo adatiuza kuti munthu wopephera uja adabwerera kudzawatenga. Tidadikira koma kudali zii mpaka lero,” adatero namwinoyo Lachinayi lapitali.

Iye adati pambuyo pake adangomva kuti mayi uja ali m’manja mwa apolisi a ku Area 33 ndipo pomwe amacheza ndi Msangulutso, adati sakudziwa kuti nkhaniyi yafika potani.

Related Articles

Back to top button