Saturday, May 21, 2022
  • About Us
  • ImagiNATION
  • Adverts
  • Rate Card
  • Contact Us
The Nation Online
Advertisement
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
No Result
View All Result
Home Chichewa Nkhani

Akwizinga Mpinganjira

by Steven Pembamoyo
11/09/2021
in Nkhani
4 min read
0
Share on FacebookShare on TwitterShare on WhatsAppShare on LinkedinLinkedinShare via Email

Bwalo lalikulu la High Court mumzinda wa Blantyre dzulo lapeza yemwe anali mkulu wa FDH Holdings a Thomson Mpinganjira wolakwa pa mlandu wonyengerera majaji omwe ankaweruza mlandu wachisankho cha 2019 ndi ziphuphu kuti apotoze chilungamo.

A Mpinganjira adawapeza kuti ankanyengerera majajiwo ndi ndalama zoposa K100 miliyoni kuti agamule mlanduwo mokomera a Peter Mutharika a chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) ndi bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC).

A Mpinganjira (Kumanja) kutuluka kubwalo la milandu ataweluzidwa

Koma woweruza mlanduwo, Dorothy Degrabrielle, alamula mtsogolomu kuti a Mpinganjira akhala nthawi yaitali bwanji kundende.

Mlanduwo umatsatira dandaulo la a Lazarus Chakwera a Malawi Congress Party (MCP) ndi a Saulos Chilima a UTM Party omwe adakadandaula kukhoti kuti bungwe la MEC lidapotoza zotsatira za chisankhocho popambanitsa a Mutharika.

Pogamula mlandu wa a Mpinganjira dzulo, Degabrielle adati pounika umboni omwe boma lidapereka m’khoti, a Mpinganjira ndi wolakwa pa gawo 1 ndi 2 zomwe adapezeka kuti ankafunadi kupereka ziphuphu.

Iwo adatinso a Mpinganjira womwe adali pabelo nthawi yonse ya mlandu awalanda beloyo ndipo abakakhala kundende ya Chichiri komwe azikadikirira tsiku lowapatsa chilango.

“Potsatira umboni onse, khothi oyamba adaberedwa mpaka akuluakulu ena a ku bungwe la Maneb adaimitsidwa ntchito.

Kusokonezeka kwa mayesowo kuphatikizapo zovuta zina ngati zokhudza mliri wa Covid-19 zidachititsa kuti mwa ophunzira 138 310 omwe adalemba mayesowo, 57 293 akhoze

(a Mpinganjira) ndi wolakwa moti belo yawo ilandidwe apite ku alimandi kundende ya Chichiri mpaka tidzapeleke chilango chawo,” adatero a Degabrielle.lapeza kuti woganiziridwa

Koma woimirira a Mpinganjira pa mlanduwo a Patrice Nkhono adapempha kuti khothi liwaganizire a Mpinganjira popereka chilango chifukwa amagwira ntchito zachifundo, ali ndi banja ali ndi antchito ambiri omwe angavutike iwo akapita ku ndende.

A Nkhono adatinso a Mpinganjira ndi wolakwa koyamba komanso umoyo wawo suli wangwiro kwenikweni kuchokera pomwe adadzapezeka ndi Covid-19 mkatikati mwa mlanduwo.

Koma yemwe amaimira boma a Solicitor General a Reyneck Matemba adati a Mpinganjira akadalingalira za mfundo zonsezi asadapange chiganizo chopalamula mlanduwo.

Iwo adapempha khoti kuti liganizirenso zomwe zikadachitika m’dziko muno a Mpinganjira akadakwaniritsa mapulani awo onyengerera majajiwo ndi ndalama zawo.

“Muganizire kuti pomwe amapalamula mlanduwo mitima ya anthu idali itayaka kale moto moti majaji akadawagonjera a Mpinganjirawa sindikudziwa kuti kukadakhala zotani,” adatero a Matemba.

Iwo adati khoti lipereke chilango chokhwima kuti anthu a ndalama, a mphamvu m’ndale ndi maudindo atengerepo phunziro kuti chuma chawo kapena mphamvu ndi udindo sizingawateteze ku lamulo.

A Mpinganjira amayankha mlandu wa ziphuphu omwe amawaganizira kuti ankafuna kupereka ndalama kwa majaji omwe ankaweruza mlandu wokhudza chisankho cha 2019.

Chisankho cha 2019 chomwe chidakomera chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) malingana ndi bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) pansi pa a Jane Ansah chidapezeka ndi zofooka zambiri.

Mtsogoleri wa chipani cha MCP a Lazarus Chakwera ndi mtsogoleri wa chipani cha UTM Party a Saulos Chilima adakasuma kukhoti kuti chisankhocho sichidayende bwino.

Khoti lidasankha majaji asanu kuti amve n’kuweruza mlanduwo koma ntchito ili mkati majajiwo adadandaula kuti a Mpinganjira amawanyengerera ndi ndalama kuti poweruza akondere a Peter Mutharika a DPP.

Mu April 2021, Degabrielle adati umboni omwe boma lidabweretsa omwe wina ndi omvera pomwe wina ndi owerenga unkatsimikiza kwatunthu kuti a Mpinganjira adayeseradi kuchita katangale.

Iwo adakana milanduyo ndipo boma lidabweretsa mboni zisanu ndi imodzi zomwe zina adali majaji omwe a Mpinganjirawo ankaganiziridwa kuti ankafuna kuwapatsa ziphuphuzo.

A Mpinganjira ndi katakwe pa bizinesi ndipo ndi m’Malawi woyamba kukhala ndi banki yomwe idayamba ngati kampani yobwereketsa ndalama koma pakutha kwa zaka 6 idakula n’kukhala imodzi mwa mabanki 12 omwe ali m’dziko muno.

Banki ya a Mpinganjira yomwe imadziwika kuti FDH Bank idagula masheya 75 mwa masheya 100 alionse a banki yomwe idali yaboma ya Malawi Savings Bank (MSB) ndipo ili ndi nthambi zake m’zigawo zonse komanso m’maboma ena ambiri.

A Mpinganjira ndi katakwe wa zachuma ndipo adachita maphunziro awo omwe adamaliza mu 1984 ku Yunivesite ya Malawi.

Atamaliza maphunzirowo, iwo adagwira ntchito zosiyanasiyana zokhudzana ndi zachuma monga ku kampani yolondoloza ndalama ya Deloitte and Touche, Blantyre Print and Publishing Group, kampani yogulitsa galimoto ya Mandala yomwe pano imadziwika kuti CFAO ndipo amatsogolera nthambi ya zachuma ku kampaniko.

Iwo adagwiranso ntchito ngati zosiyanasiyana mumakampani osiyananso kufikira pomwe iwo adapuma paudindo wawo ngati wapampando wa kampani ya FDH pa 1 September 2020 mlandu wawo utayamba kumene.

Previous Post

Time to break fertiliser, drug cartels

Next Post

Chitetezo cha mayeso chakhwima

Related Posts

Nkhani

Dollar yasowa

May 21, 2022
Foni kundende monga ya Zomba n’zoletsedwa
Nkhani

Apezeka ndi foni m’mimba

May 15, 2022
A Kamuzu adali katakwe pandale
Nkhani

‘Kamuzu adali chitsime chakuya’

May 14, 2022
Next Post

Chitetezo cha mayeso chakhwima

Opinions and Columns

Layman's Reflection

New IMF programme pivotal moment for Tonse Alliance

May 21, 2022
Family Table Talk

Historical lessons on the value of forgetting

May 21, 2022
My Diary

Politics of ‘kutola chikwama’

May 21, 2022
Bottom Up

Ukraine war: Sanctions backfire?

May 21, 2022

Trending Stories

  • Left economy in tatters: Muluzi

    Malawi’s public debt now at K5.8 tn

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • CAF accepts FAM’s request on Flames fixture shift

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Gaba comes up with two options

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Onesimus leaves Major One Records

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • UN bets K66bn on LMC’s plan

    0 shares
    Share 0 Tweet 0

Malawi-Music.com Top10

  • Values
  • Our Philosophy
  • Editorial policy
  • Advertising Policy
  • Code of Conduct
  • Plagiarism disclaimer
  • Disclaimer
  • Privacy Policy
  • Terms of use

© 2022 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation

© 2020 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

This website uses cookies. By continuing to use this website you are giving consent to cookies being used. Visit our Privacy and Cookie Policy.