Chichewa

Alandira upangiri pa malonda a mbewu

Listen to this article

 

Ochita bizinesi yogulitsa mbewu a m’maboma 7 m’dziko muno alandira upangiri wa momwe angapewere kuononga bizinesi yawo popezeka ndi mbewu yachinyengo yomwe atambwali ena amakonza mwa iwo okha.

Mchitidwe wopanga mbewu zachinyengo ukukula m’dziko muno poti pakadalibe lamulo loletsa munthu kuyamba kukonza ndi kugulitsa mbewu, koma chodandaulitsa n’chakuti atambwali ena amapanga mbewu yabodza n’kuika m’mapaketi a makampani odziwika kuti azinamiza anthu.

Apolisi ku Limbe agwirapo kale akamberembere ena omwe akugulitsa mbewu yachinyengo monga iyi
Apolisi ku Limbe agwirapo kale akamberembere ena omwe akugulitsa mbewu yachinyengo monga iyi

Mmodzi mwa ogulitsa mbewu, Ashraf Botha, yemwe ndi mwini wake wa Jumark Investments m’boma la Machinga, adapereka umboni kuti adalandirako mbewu yachinyengo poyesa kuti ndi mbewu yomwe amagulitsa chaka chilichonse.

Iye adati adadzidzimuka kuona kuti alimi ambiri omwe amamugula mbewu ndi zipangizo zina zaulimi, chaka chino akubwera ndi madandaulo kuti mbewu yawo sikumera ndipo izi akuti zidachititsa kuti iye agule mbewu ina n’kupereka kwa alimiwo mwaulere.

“Alimiwo ndi makasitomala anga ndiye ndidangololera kuti ndiluze ndine ndipo ndidagula mbewu ina kukampani ina n’kuwapatsa ndipo akuti idamera, koma ndikukambirana ndi eni kampani yoyamba aja kuti andithandiza bwanji,” adatero Botha.

Potsatira malipoti akuti anthu ena agwidwapo kale ndi mbewu yachinyengo, bungwe la International Maize and Wheat Improvement Centre (CIMMYT) lidachititsa maphunziro a ogulitsa mbewu kuwaphunzitsa momwe angazindikirire ngati mbewu ili yeniyeni ndi momwe angathandizire alimi kupewa kupusitsidwa.

Msonkhanowu udachitikira mumzinda wa Lilongwe Lachisanu lapitali ndipo oyang’anira ntchito za bungweli, Willie Kalumula, adati cholinga cha maphunzirowo n’chakuti ogulitsa mbewu azitha kuzindikira mbewu yachilungamo ndi yachinyengo komanso azikhala ndi upangiri wokwanira woti akhoza kuunikira alimi.

“Sitikufuna msika wa mbewu woti bola ndagulitsa, ayi, koma ogulitsa azikhala ndi upangiri ndipo azitha kuunikira alimi pa za mbewu zomwe angabzale m’madera mwawo komanso kuti azitha kuzindikira mbewu yachilungamo ndi yachinyengo,” adatero Kalumula.

Mmodzi mwa anthu omwe adachita nawo maphunzirowo, Jessie Mazengela, yemwe ndi mwini wake wa Zilim’nthaka Investments kwa Mkanda ku Mchinji, adati maphunzirowo adawatsegula m’maso powaunikira kuti ndi bwino kudziwa mbewu zomwe akugulitsa.

Iye adati kuzindikirako kuwapangitsa kuti nawonso aziunikira makasitomala awo omwe ndi alimi kuti ulimi upite patsogolo.n

Related Articles

Back to top button
Translate »