Chichewa

Aletsa zionetsero ku Nkhata Bay

Gulu la anthu omwe amakonza zionetsero zofuna kukakamiza boma kuti likonze msewu waukulu wopita ku Mzuzu, limange msika komanso malo oimira basi m’boma la Nkhata Bay lidagwetsa ulesi anthu Lachitatu lathali pomwe zionetserozo zidalephereka mwadzidzidzi.

Makomiti atatu a zachitukuko m’madera a ma T/A Timbiri, Mankhambira ndi Mkumbira  ataona kuti zitukuko zikuchedwa kukwaniritsidwa m’bomalo, adagwirizana zochita chionetsero ndi kukapereka chikalata ku ofesi ya DC wa bomalo.

Gululo lidagwiritsa ntchito gawo 30 la malamulo oyendetsera dziko lino omwe amakamba za ufulu wa anthu pachitukuko.

Koma tsiku la zionetserozi litafika, anthu adauzidwa kuti bwanamkubwa (DC) wa bomali sadapereke chilolezo ndipo ngati anthuwa angapitirire ndi zionetserozi zikhala zosaloledwa.

Kaunda: Ngati sakutiuza zomveka tipitirira ndi zionetsero
Kaunda: Ngati sakutiuza zomveka tipitirira ndi zionetsero

Ena mwa anthu omwe amafuna kutenga nawo mbali pazionetserozo adadzidzimuka atauzidwa atafika kale pamalo a nkhumano kuti zionetserozo zalephereka.

Nawo apolisi ovala zamawangawanga omwe adalipo 16 sadalekerere koma kuchoka mumzinda wa Mzuzu kukasonkhana nawo pamalo a nkhumanowo  pa roadblock yaikulu m’bomali. Koma patatha maola awiri opanda chochitika adabwerera ku Mzuzu.

Mneneri wa polisi m’chigawo cha kumpoto, Maurice Chapola, adati apolisiwo adangopita kukakhala tcheru posungitsa bata ngati zionetserozo zikadapitirira.

Msangulutso adalankhula ndi wampando wa komiti yomwe imakonza zionetserozi, Mabvuto Kaunda, yemwe adati bwanamkubwa wa bomali ndi amene adaletsa zionetserozi.

“Monga mwa malamulo a dziko lino zionetsero zimachitika pokhapokha ngati padutsa masiku awiri mutapereka kalata yanu yodziwitsa DC. Ife tidatsatira izi bwino lomwe chifukwa tidapereka kalata yathu Loweruka sabata yatha kuwadziwitsa kuti tichita zionetsero

Lachitatu,”  adatero Kaunda.

Koma Kaunda adati adali odabwa atauzidwa ndi DC Lachiwiri kuti zionetserozo sizikhalako kaamba koti Lolemba lidali latchutchi choncho sangaliwerengere.

“Ifetu zionetsero zathu zikadakhala za bata ndipo timafuna kukapereka kalata kudzera ku ofesi yawo yopita kuofesi ya mtsogoleri wa dziko lino yoti ngati satiyankha zakuspa pamasiku 30, tidzayamba kugona kuofesi ya bwanamkubwayu,” adatero Kaunda.

Iye adati anthuwa atopa ndi kulonjezedwa zitukuko zomwe sizikukwaniritsidwa. Kaunda adati ngakhale boma lidayamba kulonjeza zoti likonza msewuwu ndi ndalama zochokera ku bank ya African Development Bank (AfDB) zaka zapitazo, pamalopa palibe ndi kontilakita yemwe.

“Tidamvetsedwanso kuti kudaperekedwa K368 miliyoni yomangira depoti ndi msika, koma zonsezi kuli zii,” adadandaula Kaunda.

Iye adati bwanamkubwayu wauza komitiyi kuti a unduna wa za mayendedwe komanso bungwe loona za misewu m’dziko muno la Roads Authority (RA) akumana nawo kuti athetse kusamvanaku.

“Koma ife tikuti, ngati sakatiuza zomveka, tipitirira ndi zionetsero,” adatero Kaunda.

DC wa bomali, Alex M’dooko, sadapezeke pa lamya zake zonse ziwiri pomwe timasindikiza nkhaniyi.

Koma mneneri wa bungwe la RA, Portia Kajanga, adavomereza kuti ntchitoyi yachedwadi. Iye adati koma apa nguluwe yalira msampha utaning’a chifukwa ati ntchitoyi iyamba posachedwappa.

“Ntchito yatha kale, inde tachedwa koma anthuwa asade nkhawa, zitheka osati chifukwa atiopseza koma potsatira dongosolo lake,” adatero Kajanga.

Ntchito yomanga msewu idakhazikitsidwa mwezi wa July m’chaka cha 2013 ndipo panthawiyo ntchitoyi imati itenga ndalama zokwana K14.8 biliyoni ndipo imayembekezereka kugwiridwa kwa zaka zinayi mpaka chaka cha 2017.

 

 

 

Related Articles

Back to top button