Nkhani

Aletsa zionetsero za madzi

Listen to this article

Mkulu wa bungwe loona za ufulu wa ogula la CAMA John Kapito Lachinayi adalepheretsa zionetsero ngakhale mpaka lero anthu ozungulira Blantyre akusaukirabe madzi.

Chionetserochi chidakonzedwa ndi mkulu wa pamene amati ayende kukadandaulira kampani yogulitsa madzi ya Blantyre Water Board (BWB).

Zionetserozi zimadza pamene kwatha mpaka miyezi iwiri madzi m’madera ena amumzindawu asakutuluka mumzindawu. Koma Kapito adati: “Tidakumana ndi akuluakulu a bungweli ndipo atitsimikizira kuti ayamba kupereka madzi. Taona kuti palibenso chifukwa chochitira zionetsero pamene atilonjeza kuti ayamba kupereka madzi,” Kapito adauza atolankhani.

Koma pofika Lachinayi, madera ambiri mumzinda wa Blantyre madzi adali akuvutabe zomwe zidachititsa anthu ena kukwiya nazo.

Mmodzi mwa anthuwo, Rawjazz Siula akuti ndi bwino tsiku lina kudzachita zionetsero zosagwirizana ndi bungwe la Cama popusitsa Amalawi.

“Basi bwana Kapito akatinamize pamene tikunena kuti patha sabata zambiri madzi asakutuluka? Bwanji sadayitane anthu omwe amawauza kuti ayende pamsewu kuti zionetsero zalephereka?” sakumvetsa Siula.

Mwayi Mbwelera akuti nkhani ya madzi yavuta kotero zionetsero si bwenzi zitalephereka. “Kuno ku Mbayani anthu tikusaukira madzi, nthawi yonseyi bwanji samatibweretsera madziwo? Zalakwika,” adatero.

Related Articles

Back to top button