Chichewa

Alimbana ndi ntchemberezandonda ku Zomba

Unduna wa zamalimidwe wati ntchemberezandonda zomwe zabuka m’boma la Zomba zisatayitse anthu mtima chifukwa akatswiri apita kale m’madera omwe akhudzidwa ndi mbozizo.

Mbozizo zapezeka kale m’madera ena m’boma la Zomba mkulu wa zaulimi kumeneko Patterson Kandoje watsimikiza koma mneneri wa unduna wazamalimidwe Hamilton Chimala adati gulu la akatswiriwo likafikanso m’madera achigwa cha Shire.

“Padakalipano nduna ndi gulu la akatswiri ali kale kalikiliki kulimbana ndi mbozizo ndipo iwo ndi amene angakhale ndi zonena zambiri pammene zinthu zilili,” adatero Chimala.

Ntchemberezandonda zimaononga masamba ofunika pokonza chakudya cha mbewu
Ntchemberezandonda zimaononga masamba ofunika pokonza chakudya cha mbewu

Nduna ya zamalimidwe Dr Allan Chiyembekeza adatsimikiza kuti iye pamodzi ndi akatswiri ali kalikiliki kulimbana ndi vutoli koma adati padakalipano sanganene kuti vutolo ndi lalikulu motani popeza akadali mkati mofufuza.

“Anthu angokhala ndi chikhulupiliro chifukwa akatswiri omwe akugwira ntchitoyo ndiwodziwa kwambiri moti ali ndi chikhulupiliro kuti vutoli silipita patali lisadagonjetsedwe,” adatero Chiyembekeza.

Ndunayo idati chongodandaulitsa chakuti mbozizo zimaononga kwambiri panthawi yochepa komanso vuto lake ndilakuti zimadya masamba omwe mbewu zimadalira popanga chakudya motero kakulidwe ka mbewu kamasokonekera.

“N’tizilombo tachabe kwambiri chifukwa timaononga masamba a mbewu choncho kuchedwa kutigonjetsa kukhoza kukhala ndi zotsatira zowawa kwambiri,” adatero Chiyembekeza.

Kandoje adati pamalo okwana mahekitala 34 omwe akhudzidwa, mahekitala 6 ndiwo adali atapoperedwa pofika Lachiwiri ndipo adapempha anthu kuti akhale tcheru kuti akangoona mbozi zobiriwira zokhala ndi mizere yoyera akauze a zaulimi chifukwa maonekedwe a ntchemberezandonda ndi wotero.

Chiyembekeza:  Tikuthana nazo
Chiyembekeza:
Tikuthana nazo

Madera ozungulira malo a zaulimi a Mpokwa kwa T/A Mwambo makamaka midzi ya Saiti, Masambuka, Kwaitana, Mamphanda, Kabwere, Kumpatsa, Havala, Mlomwa ndi Chaima ndi ena mwa midzi yomwe yakhudzidwa.

Ntchemberezandondazi zabuka panthawi yomwe alimi akudandaula kale ndi ng’amba yomwe ikutha pafupifupi sabata zitatu tsopano ndipo mbewu zambiri zanyala kale m’minda moti pali chiyembekezo choti ng’ambayi itati yapitirira ndiye kuti alimi akhoza kudzabzalanso.

Ng’ambayo yadza kaamba ka mphepo ya El Nino yomwe yasokoneza magwedwe a mvula makamaka m’maiko a kummwera kwa Africa zomwe zapangitsa madera a m’chigawo cha kummwera kwa Malawi akhudzidwe kwambiri.

Malingana ndi a nthambi yoona zanyengo, mvula ikuyembekezeka kusintha chamkatikati mkumapita kumapeto kwa mwezi uno wa January. n

Related Articles

Back to top button