Chichewa

Alimbikitsa chitetezo cha okhala m’malire Covid-19

Bungwe la Farmers Union of Malawi (FUM) lati pakufunika kulimbikitsa chitetezo cha anthu m’madera akumidzi omwe ali m’malire a dziko lino ndi maiko ena pofuna kupewa kufala kwa matenda a Covid-19.

Mlangizi wamkulu wa bungweli m’boma la Mwanza Caswel Kachingwe adanena izi sabata latha pamwambo wopereka mabeseni, ndowa ndi sopo kumidzi ya kwa mfumu Nthache ndi Govati m’bomalo polimbikitsa anthu kusamba m’manja ngati njira yopewera matendawa.

Nthache (Kumanzere) ndi Kwachingwe (Kumanja)
kusamba m’manja pa mwambowo.

Maderawa, omwe ali m’malire a dziko ndi la Mozambique ndi komwe bungwelo likuchitako pulojekiti yolimbikitsa kadyedwe kabwino.

“Nthendayi yavuta m’maiko oyandikana nawo ngati Mozambique. Anthu a kwa Nthache ndi Govati ayandikana ndi dzikoli moti akhonza kugwidwa ndi mliliwu ngati satetezedwa ndi kulimbikitsidwa kutsata njira zopewera. Tathandiza ndi zinthuzi ndipo tionetsetsa kuti zigwire ntchito popeza kupewa kumaposa kuchiza,” adatero Kachingwe.

Iye adati zipangizozi zikaikidwa m’malo omwe anthu amadutsa kwambiri ndi mokumanirana.

Woona za umoyo m’bomalo Ireen Zuze adavomerezana ndi Kachingwe pa zolimbikitsa chitetezo cha anthu m’maderawo.

“Zipangizo zothandiza anthu kupewa makamaka kuti azisamba m’manja ndi sopo pafupifupi zikufunika. Tikuthokoza FUM pothangatira ntchito yathu yolimbikitsa umoyo wabwino m’boma lino,” adatero Zuze.

Mfumu Nthache idali yokondwa ndi kunena kuti ukhondo uyanja dera lake ndipo chitetezo ku Covid-19 chikula.

Related Articles

Back to top button
WordPress › Error

There has been a critical error on this website.

Learn more about troubleshooting WordPress.