Chichewa

Alimi konzekani kukolola madzi

Mvula ya masiku ano ndi yanjomba. Zikatere mlimi amayenera kuchenjera kuti aphulepo kanthu ngakhale mvula itadula msanga. Ichi nchifukwa chake akatswiri pa zamalimidwe amalimbikitsa alimi kuti ayambe kukolola madzi a mvula.

Nthawi yokonzeka kukolola madziwatu ndi ino pamene mvula yayamba kale kugunda ndi madera ena m’dziko muno ayamba kale kulandira mvula.

Mkonzi wa pulogalamu ya ‘Ulimi Walero’ pawailesi ya MBC, Excello Zidana adati ngati alimi sachangamuka ndi ulimi wawo poyamba kukolola madzi, ndiye kuti ulimi uwavuta.

Madzi a mvula sayenera kumangotaika
Madzi a mvula sayenera kumangotaika

“Mvula ya masiku ano mwaiona kale kuti ikugwa mwa njomba. Koma kwa alimi amene akukolola madzi, amathandizikabe chifukwa amagwiritsira ntchito madzi amene akolola pamene mvula yadula,” adatero Zidana.

Pa momwe alimi angakololere madzi, Zidana adati pali njira zambiri zokololera madzi monga kupanga migula (akalozera) komanso kupanga mabokosi.

“Ukapanga kalozera, mizere yonse yomwe ulime m’mundamo imatsatana ndi kalozerayo, kusonyeza kuti mvula ikagwa madzi sathamanga. Komanso mukapanga mabokosi, madzi amaima ndi kudikha koma mukapanda kupanga izi, mvula ikagwa, madzi amathamanga kwambiri ndipo salowanso pansi,” adatero Zidana.

Iye adati mgula kuti ulimbe uyenera kuti mlimi abzalemo udzu wa vetiva kuti madzi angachuluke bwanji sungagumuke.

Zidana adatinso kukumba dzenje kuti madzi azilowapo mvula ikamagwa ndi njira inanso yomwe alimi angakololele madzi.

“Madzi amene asungidwa padzenjepo, mungathe kuwagwiritsira ntchito pamene mvula yadula. Komanso pakhomo panu muyenera kuika migolo yomwe mungasungire madzi.

“Komanso kuthira manyowa ndi njira ina yokolorera madzi chifukwa chifukwa manyowa amasunga chinyezi chomwe chingakhale m’mundamo kwa masiku pamene mvula yadula,” adatero Zidana.

Related Articles

Back to top button