Chichewa

TB imakhudza ziwalo zonse

Listen to this article

 

Kusiyana ndi nthenda zina, nthenda ya chifuwa chachikulu ya TB imakhudza chiwalo china chilichonse, kupatula zikhadabo ndi tsitsi, watero woona za nthendayi ku unduna wa zaumoyo, James Mpunga.

Iye adati izi zili chomwecho chifukwa tizilombo toyambitsa nthendayi totchedwa microbacterium timatha kulowa m’chiwalo china chilichonse cha thupi.

Mpunga: Chofunika n’kusadukiza mankhwala

“Ichi n’chifukwa chake zizindikiro zakenso zimakhala zochuluka. Mwachitsanzo, kukhosomola, kupweteka kwa pachifuwa, nthawi zina kutulutsa makhololo a magazi, kutuluka thukuta makamaka usiku, kutentha kwa thupi, komanso kupweteka kwa msana. Chifukwa cha ichi, kawirikawiri sikelo ya wodwala imatha kutsika mosavuta,” iye adatero.

Mpunga adati ngakhale nthenda ya TB imaika anthu pachiopsezo, ndi nthenda yosavuta kuchiza, chachikulu ndi kuyezetsa mwamsanga kuti munthu ayambe kulandira mankhwala komanso kumamwa mankhwala mosadumphitsa ndi mosalekera panjira kufikira munthu atachira.

Iye adati chifukwa cha ichi, ndi anthu ochepa okha omwe amamwalira ndi nthendayi ndipo nkhani yaikulu imakhala kunyalanyaza chabe.

“ Munthu odumphizadumphiza kumwa mankhwala amakhala pachiopsezo chosadzachira ndi mankhwalawa,” iye adatero.

Mpunga adaonjezanso kuti munthu wodwala nthendayi amayenera kulandira chisamaliro choyenera ngati odwala wina aliyense ndipo kuonjezera apa, amayenera kupatsidwa upangiri wa momwe angamamwere mankhwala komanso pa zomwe akuyenera kuchita kuti asapatsire anzake omwe alibe nthendayi.

Iye adafotokoza kuti wodwala nthendayi amayenera kumaphimba kukamwa pokhosomola komanso sakuyenera kumakhala pamodzi ndi anthu mmalo othinana ndiopanda mazenera chifukwa potero, akhonza kupatsira anthu enawo mosavuta.

“Nthendayi ndi yopeweka ndipo njira yodalirika ndi kusapuma mpweya wa munthu yemwe ali ndi nthendayi chifukwa tizilombo toyambitsa nthendayi timafala mwachangu kudzera mumpweya omwe timapuma,” iye adatero.

Sabata ya mawa tidzafotokozera za zinthu zosiyanasiyana zomwe zimakolezera nthenda ya TB. n

Related Articles

Back to top button
Translate »