Chichewa

Alimi samalani pososa

Mlimi weniweni ndiye amasamalitsa kalendala yake ya ulimi. Kuyambira mwezi watha mpaka uno, alimi amalangizidwa kuti akuyenera kuyamba kusosa.

Mlangizi wamkulu m’boma la Chiradzulu, Sheila Kang’ombe wati alimiwa ayenera asamalitse pamene akusosa chifukwa chiyambi chosakolola zochuluka ndi nthawi yososa.

Kang’ombe adati alimi akuyenera kudziwa kuti mitengo ya thonje ndi fodya siyiyenera kukwiriridwa chifukwa nthawi zambiri imakhala ndi matenda.

Pofotokozapo njira zabwino za kasosedwe, Kang’ombe adati kukwirira mapesi ndi ndondomeko yabwino ya kasosedwe chifukwa kumasunga manyowa.

Alimi angathe kukwirira mapesi ngati awa
Alimi angathe kukwirira mapesi ngati awa

“Mapesi a chimanga mtedza ndi mbewu zina ayenera akwiriridwe, iyi ndi njira yabwino ya kasosedwe chifukwa zikaolerana zimapanga manyowa.

“Ena amakonda kuotcha mapesi, izi siziloledwa koma mitengo ya fodya ndi thonje ndi zomwe ziyenera kuotchedwa. Mapesi achimanga komanso mbewu zina amabweretsa manyowa ngati akwiriridwa,” adatero iye.

Madera ambiri alimi ayamba kale kukwirira koma ena sadayambe monga zilili ku Dedza komwe alimi ali otangwanika ndi kukumba kachewere ndi mbatata ya kholowa.

Sylvester Chitini wa m’mudzi mwa Salile kwa T/A Kasumbu m’boma la Dedza akuti kumeneko alimi sadayambe kusosa komabe mwezi ukudzawu ayambapo.

“Pano ndife otangwanika ndi kukumba mbatata ya kholowa komanso kachewere. Nthawi zonse timayamba mochedwa kusosa kuno. Kumapeto kwa September aliyense akhala wayambapo kusosa,” adatero iye.

M’boma la Blantyre ndi maboma ena alimi ena akumaliza kusosa pamene ena akuyamba kumene. Tomasi Kandodo wa ku Chilomoni akuti sabata ikubwerayi akhala atamaliza kusosa munda wake.

“Kwakukulu ndiye tasosa kale, panopa tangotsala ndi ndime yochepa yomwe sabata ziwiri zikubwerazi tikhala tamaliza,” adatero

Related Articles

Back to top button