Chichewa

Aliza abale pa Khrisimasi chifukwa cha mowa

Listen to this article

 

Chaka chilichonse, 25 December ndi tsiku lachisangalalo koma chaka changopitachi lidali lachisoni m’banja la a Moses a kwa Chinthambwe mfumu yaikulu Chilowoko m’boma la Ntchisi.

Patsikulo, mmodzi mwa a pabanjalo, Steven Moses wa zaka 47,  adamwalira atamwa mkalabongo wochuluka komanso osadyera.

Mng’ono wa malemuyo yemwe amakhala kufupi naye ku Area 25 mumzinda wa Lilongwe, Amos Moses, adati mbale wakeyo adavomereza za nkhaniyo ndipo adati adamva kuchokera kwa wina kuti mbale wakeyo sanali bwino.

Amos: Idali imfa yowawa

Iye adati mmbuyomo sadalandireko lipoti lilironse loti mbale wakeyo samamva bwino ndipo atamva uthengawo adathamangira kunyumba ya malemuyo komwe adakapeza atauma kale.

“Tidamupeza atauma pamphepete pake pali mabotolo a mkalabongo, ena mulibe kanthu ena osayamba. Idali imfa yowawa,” adatero Amos.

Mneneri wapolisi ya Kanengo, Alfred Chimthere, adatsimikiza kuti bamboyo adamwalira kaamba ka mowa.

“Titalandira uthenga wa imfayo, tidathamangirako ndipo titatengera mtembowo kuchipatala cha Kamuzu Central, madotolo adatsimikiza kuti imfayo idachitika kaamba ka mowa oposa mlingo,” adatero Chimthere.

Aaron Tsokwe, yemwe amagulitsa kanyenya mumsika wa Nsungwi komwe malemuyo amakonda kumwera mowa adati mkuluyu amakonda mowa wa kachasu ndi wa m’masacheti ndipo ngakhale amakonda mowa choncho, adalibe mbiri ya ndewu.

“Anthu ambiri tidamuzolowera kuti amakhala chiledzerere. Iye kwake kudali kulongolola, osati ndewu,” adatero Tsokwe.

Mkulu wa bungwe lolimbana ndi mchitidwe ogwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo la Drug Fight Malawi yemwenso amayendetsa mgwirizano wolimbikitsa kuti pakhale ndondomeko zoyendetsera kagwiritsidwe ntchito ka mankhwala wa Malawi Alcohol Policy Alliance, Nelson Zakeyu, adati imfa zotere zikunka patsogolo kaamba kosowa ndondomeko zoyenera.

Iye adati izi zikadatha boma likadakhala ndi ndondomeko zoyenera komanso njira zamphamvu zoonetsetsa kuti ndondomekozo zikugwiradi ntchito.

“Timatsogoza kunena kuti anthu azidyera akafuna kumwa mowa mmalo mongoletsa kuti anthuwo asamamwe,” adatero Zakeyu.

Mneneri wa polisi m’dziko muno James Kadadzera adauza Msangulutso Lachinayi kuti ali mkati mosonkhanitsa ngozi zomwe zachitika mkatikati mwa nyengo ya zisangalalo ntchito yomwe ikukhudza kusonkhanitsa chiwerengero cha imfa zokhala ngati ya Steven.

Iye adati apolisi amagwira ntchito usana ndi usiku kuwonetsetsa kuti anthu akutsatira malamulo ndi cholinga chopewa zinthu zosakhala bwino monga imfa zopeweka ngati za uchidakwa.

“Malamulotu alipo monga pamlingo wa zaka zovomerezeka kumwa mowa, nthawi yomwera mowa komanso mamwedwe oyenera. Ichi nchifukwa chake nthawi zina apolisi amayendera malo omwera kufuna kuona ngati ndondomeko zikutsatidwa,” adatero Kadadzera.

Iye adalonjeza kuti apolisi akamaliza kusonkhanitsa za chiwerengero cha ngozi, imfa ndi zochitika zina pa nyengo ya zisangalalo, adzadziwitsa mtundu wa aMalawi kudzera m’njira zoyenera. n

Related Articles

Back to top button