Chichewa

Alosera mvula kugwa mochuluka

 

Nthambi yoona za nyengo ya Department of Climate Change and Meteorological Services (DCCMS) yati mvula yamphamvu ikhala ikugwa kwa masiku angapo motsatizana.

Uwu ungakhale mpumulo polingalira momwe mbewu zafotera m’minda komanso lingakhale tsoka polingalira ngati mvulayo ingachulukitse monga zidalili chaka chatha m’madera ena.

M’chikalata chosonyeza momwe nyengo ikhalire masiku angapo akudzawa, nthambiyo idati mvula yamphamvuyi ikhala ikugwa dziko lonse pafupifupi sabata yatuthu kuyambira lachinayi lapitali.

Kaamba ka ng’amba, chimanga china chidanyala
Kaamba ka ng’amba, chimanga china chidanyala

“Mphepo yomwe ikuomba kuchokera m’madera osiyanasiyana, ipangitsa kuti mvula yamphamvu kwambiri izigwa makamaka kuyambira Lamulungu pa 17 January, 2016. M’madera ambiri, anthu ayembekezere nyengo yotentha masana panthawiyi,” idatero nthambiyi mchikalatacho.

Mkulu wa nthambiyo Jolam Nkhokwe adati mmasiku angapo apitawa, mvula adayeserako m’madera a m’chigawo chapakati ndi kumpoto pomwe m’madera a kumwera, mvulayi imagwa monyentchera.

Mneneri wa nthambiyo, Ellen Kululanga, adati izi nzosadabwitsa chifukwa ndimo zimakhalira kukakhala mphepo ya El Nino monga momwe azanyengowa adalengezera kumayambiriro a mvula.

“Malawi ali mmphepete mwa zigawo ziwiri za Africa kumwera ndi kummawa zomwe zimapangitsa kuti kabweredwe ka mvula kazisiyana. Mvula imavutirako m’chigawo cha kumwera kaamba kakuti chili mbali ya kumwera kwa Africa.

“Chigawo cha kumpoto chomwe chili kumbali ya kumawa kwa Africa, mvula imachulukirapo moti ndi mphepo imeneyi ya El Nino, madera a kumwera mvula ivutirapo pomwe kumpoto ndi madera ena pakati zinthu zikhalako bwino,” adatero Kululanga.

Ogwira ntchito zotukula ulimi m’maboma osiyanasiyana adatsimikizira nyuzipepala ya The Nation kuti ng’amba yomwe idagwayi yaononga mbewu zambiri m’madera osiyanasiyana.

Ena mwa omwe adatsimikizira izi ndi wachiwiri kwa oyendetsa ntchito za Blantyre ADD Aggrey Kamanga komanso otukula ntchito zaulimi m’boma la Machinga Palichi Munyenyembe omwe adati mvula idadula ndipo alimi ali ndi nkhawa.

Kudula kwa mvulaku kudakhudza magulu osiyanasiyana mpaka a bungwe loyendetsa ntchito za fodya mmalawi la Tobacco Control Commission (TCC) lidaganiza zochita kauniuni wa tsogolo la fodya yemwe wambiri adafota. n

Related Articles

Back to top button