Nkhani

Amabungwe akukonzanso zogwirira ntchito limodzi

Listen to this article

Pozindikira kuti mutu umodzi susenza denga, mabungwe omwe si aboma omwe akugwira ntchito zosiyanasiyana m’dziko muno, kuphatikizapo za maufulu a anthu komanso kayendetsedwe ka boma, ati ali ndi cholinga chokhazikitsa ndi kulimbikitsa mgwirizano pakati pawo kuti azitha kugwira ntchito limodzi pofuna kutumikira mtundu wa Amalawi pa zofuna zawo.

Mmodzi mwa akuluakulu a mabungwe omenyera ufulu wa anthu ndi kudzudzula zolakwika pakayendetsedwe ka zinthu, McDonald Sembereka, adatsimikizira Tamvani kuti mabungwe angapo avomera kale kulowa nawo mumgwirizanowu ndipo posachedwapa uyamba kugwira ntchito yake.

“Cholinga chathu n’chimodzi basi monga oyimirira Amalawi kuonetsetsa kuti zinthu zikuyenda bwino ndipo Amalawi sakuvutika kapena kuphwanyiridwa maufulu awo osiyanasiyana. Taganiza izi poona momwe zinthu zayamba kuyendera m’dziko muno,” adatero Sembereka.

Koma katswiri wa zamalamulo ndi ndale Blessings Chinsinga wati zomwe akulingalira mabungwewa zingatheke pokhapo atasintha khalidwe ndi magwiridwe a ntchito zawo kuti athe kuongolera ndi kudzudzula kayendetsedwe ka zinthu m’dziko muno.

Tamvani itamufunsa maganizo ake pa lingaliro la mabungwewa, Chinsinga adati ngakhale ganizoli ndi labwino pachitukuko ndi tsogolo la dziko lino, mabungwewa ali ndi ntchito yaikulu yomema Amalawi kuti awakhulupirirenso potengera momwe zinthu zakhala zikuyendera mmbuyomu.

“Ndi ganizo labwino koma lovuta kukwaniritsa chifukwa kuyamba n’kuyamba, pali kusagwirizana pakati pa mabungwe eni ake. Izi mukhoza kutsimikiza potengera momwe ntchito za mabungwewa zakhala zikuyendera, makamaka pokonza zionetsero,” adatero Chinsinga.

Iye adati Amalawi ambiri adataya chikhulupiriro kuchokera m’chaka cha 2011 pomwe atsogoleri a mabungwe adamema zionetsero za dziko lonse koma mapeto ake anthu ena adaphedwapo ndipo patangopita nthawi pang’ono mabungwewa adakhala chete.

“Zionetsero za 2011 ndizo zidali nsanamira yaikulu ya mabungwe yosonyeza mphamvu, kugwirizana ndi mtima wofunadi kuthandiza, koma zomwe zidachitika zija zidagwetsa anthu ulesi waukulu moti pano ambiri alibenso nazo chidwi [zochita za amabungwewa],” adatero Chinsinga.

Iye adati chofunika apa n’kuyamba apanga mfundo imodzi yomwe ingaonetse kuti cholinga chawodi n’chimodzi, apo ayi, palibe chomwe angapindulepo.

Koma Sembereka wanenetsa kuti mgwirizano wa ulendo uno ukhala wosiyana ndi migwirizano ina yonse mmbuyomu kaamba koti mfundo zake zikhala zakupsa ndi zomanga komanso zotengera maganizo a anthu ndi kudalira zokambirana mmalo mongolozana zala.

Amalawi ena omwe alankhula ndi Tamvani ati chimawagwetsa ulesi kwambiri n’chakuti atsogoleri a mabungwewa sachedwa kutembenuka akalonjezedwa kapena kupatsidwa maudindo m’boma lolamula.

Lameck Silungwe wa ku Chitipa adati n’zokhumudwitsa kuti amabungwe amakokomeza kuti iwo ndi omenyera ufulu anthu ndi kudzudzula pomwe boma likulakwitsa koma mapeto ake amaoneka ngati iyi ndi njira yopemphera maudindo m’boma.

“Ndi atsogoleri angati a mabungwe omwe adapereka chiyembekezo mwa Amalawi kenako n’kutseka pakamwa Amalawiwo akuwafuna kwambiri?

Ndi ochuluka oti mwina enafe sitingathe kuwalakatula onse. Zimenezi ndizo zimagwetsa ulesi,” adatero Silungwe.

Masozi Banda wa m’boma la Nkhata Bay naye adati adali ndi chiyembekezo chachikulu kuchokera kwa amabungwe pa zomwe adachita m’chaka cha 2011, koma kenako adaona ngati wagwiritsidwa ntchito nkutayidwa ngati wopanda phindu.

“Anthu ambiri tidalolera kupita kukapanga zionetsero m’mizinda chifukwa cha chikhulupiriro koma patangotha miyezi yochepa chabe, atsogoleri ambiri adayamba kulowera kosiyanasiyana kutisiya manja ali m’khosi,” adatero Banda.

Naye Manuel Sajiwa wa m’boma la Lilongwe adati akhoza kutsatira mabungwewa pokhapokha ataonadi kuti pali cholinga chenicheni osati kufuna kupanga phokoso longolambulirapo njira yopezera maudindo.

“Zimayamba chonchi, amabwera pang’onopang’ono n’kumatitsimikizira kuti akudzatitsogolera kuti timenye nkhondo ya ufulu wathu koma posakhalitsa umangomva kuti anthu ochepa, makamaka iwowo, ali m’maudindo kenako zii,” adatero Sajiwa.

Zitachitika zionetsero za 2011 zomwe adatsogolera akuluakulu a mabungwe oima paokhawa, anthu ambiri adaphedwa pazipolowe zomwe zidabuka pakati pa apolisi ndi anthu pomwe apolisi adaletsa anthu kuononga katundu wa eni.

Patangotha miyezi yochepa chichitikireni izi, atsogoleri ena a mabungwe adapatsidwa maudindo m’boma latsopano la PP ndipo izi zidakhalangati zasokoneza mgwirizano wa mabungwewa omwe adayamba kugwira ntchito paokhapaokha.

Ena mwa akuluakulu a mabungwe omwe adalandira maudindo kuchoka mchaka cha 2011 ndi Sembereka, yemwe adapatsidwa udindo wa mlangizi wa pulezidenti pankhani za mabungwe m’boma la Joyce Banda wa chipani PP; Dorothy Ngoma, womenyera ufulu yemwe adapatsidwa udindo woyang’anira za uchembere wabwino m’boma lomwelo la PP; ndipo m’boma latsopano la DPP, mmodzi mwa amabungwe omwe adakhala chete atapatsidwa udindo ndi Mabvuto Bamusi, yemwe ndi mlangizi wa Pulezidenti pa zamabungwe omwe si aboma.

Koma Sembereka adati maudindo ngati awa sakhala chitseka pakamwa koma njira yofuna kuthandizira boma pakayendetsedwe ka zinthu uli mkati momwemo kusiyana n’kukhala kunja komwe umaoneka ngati ukupangira zipsodo. n

Related Articles

Back to top button