Nkhani

Amalawi akulira ndi kukwera kwa mafuta

Listen to this article

Mkulu wa bungwe loona za ufulu wa ogula malonda la Consumers Association of Malawi (CAMA), John Kapito, wati boma lichite machawi kubweretsa njira zoombolera anthu pomwe mitengo ya zinthu yakwera potsatira kukweranso kwa mitengo ya mafuta a galimoto apo biii zifika posauzana.

Kapito wanena izi m’sabatayi pophera mphongo kulira kwa Amalawi omwe akuti moyo wafika pothina kaamba ka mavuto a zachuma.

Mkuluyu wati kumudzi n’kumene kwagona moto kaamba koti ogulitsa amakweza zinthu moposera mlingo wake.

Kapito wati posachedwapa zinthu zifika potaya miyoyo chifukwa chakudya chisowa komanso chochepa chopezekacho chikwera mtengo.

“Kumudzi ndiko kuli mavuto osaneneka kaamba koti mitengo yakwera kale moposera m’tawuni. Bungwe lathu lili kalikiliki kuthamanga m’midzimu kuona momwe anthu akukwezera mitengo ya katundu wofunikira,” watero Kapito.

Koma mneneri wa boma, Moses Kunkuyu, wati Amalawi atonthola posachedwapa popeza boma laika kale ndondomeko zowapulumutsira ku ululu wa zachuma.

‘Mafuta akweranso’

Mafuta a galimoto akweranso sabata yatha ndipo aka kadali kachiwiri kukwera m’sabata zinayi zokha.

Pa 10 Ogasiti, petulu adachoka pa K441.10 kufika pa K485.60, dizilo adachoka pa K445.60 kufika pa K475.

Pa 6 Sepitembala, petulo adalumpha kuchoka pa K485.60 kufika pa K539, dizilo adachoka pa K475 kufika pa K521.90.

Izi zikusonyeza kuti m’sabata zinayizi, petulo wakwera ndi pafupifupi K98 pa lita pomwe dizilo wakwera ndi K76.30.

Monse momwe mafutawa akhala akukwera m’sabatazi, nayo mitengo ya katundu wofunikira wakhala akukwera mtengo.

Mwachitsanzo, dzanadzanali, mitengo ya maulendo yakwera ndi ndi K1 pa K10 iliyonse.

Loveness Chinomba wochokera ku Neno koma akukhala ku Chirimba mumzinda wa Blantyre wati moyo wa mtawuni wafika powawa.

Chinomba, yemwe amagulitsa masamba kumsika wa Blantyre, wati malinga ndi kukwera kwa mitengo yogulira mafuta agalimoto, ndiwo za masambanso zakwera.

Masamba anayi a mpiru ali pa K20 kuchoka pa K10, masamba 6 a nkhwani alinso pa K20.

“Ndimakapikula kwa Bvumbe. Kumeneko alimi akuti akweza chifukwa zomwenso iwonso amadalira pantchito yawo zakwera.

“Komansotu ulendo wopita kumeneko wakwera, ndiye ndikuyenera kukweza kuti ndizipezako phindu,” adatero Chinomba.

‘Apaulendo amva kuwawa’

Charles Kabaghe wa m’mudzi mwa Mkombanyama kwa T/A Mwabulambia m’boma la Chitipa wati kumeneko zinthu zaipa, maka pa maulendo.

Iye wati kalelo kuchoka ku Karonga kupita ku Mzuzu pa minibasi ankalipira K2600 koma tsopano akulipira K4 500.

Sopo osambira wa Geisha wamkulu tsopano wafika pa K350 kuchoka pa K220.

“Boma liike ndalama m’makampani kuti mitengo ya zinthu itsike. Pano kumudzi kuno kwaipa; sitikugwira ntchito koma zinthu zakwera—nanga tidzigula n’chani?” adalira Kabaghe, yemwe ndi mlimi.

Sanudi Tambula wa m’mudzi mwa Kalembo kwa T/A Kalembo m’boma la Balaka wati kumenekonso zinthu zakwera, maka zam’golosale.

Iye wati achinyamata akumeneko akusowa chochita chifukwa mwayi wa maganyu ukusowanso.

“Zinthu zikukwera pomwe tilibe pogwira, tikupempha boma litiganizire kuti tikhale ndi kopezera ndalama,” adatero Tambula.

Apa Kapito wati tsopano n’zosapsatiranso kuti boma la chipani cha People’s (PP) lalephera posathana ndi kusakhazikika kwa mitengo ya mafuta.

Iye adaloza chala boma polola kuyamba kutsatira ndondomeko yomwe imati mtengo wa mafuta m’dziko muno uzisintha msangamsanga mitengo ikangosintha pa misika ya chipiku ya kunja.

Pansi pa ndondomekoyi, mitengo ya mafuta ikuyenera kusintha pompopompo m’dziko muno ngati mitengo yasintha kunjako.

“Tikupempha boma libwerere libweze ganizo lake. Kwacha yathu ikungogwa kotero ngati kunja mafuta akukwera mtengo kunonso adzikwera.

“Ngati boma silichita kanthu, n’kutheka mitengo ya mafuta kumakwera sabata iliyonse,” adatero Kapito.

Iye wati kumasulira kwa zonsezi n’koti Amalawi akhala pamoto popeza zinanso zofunikira pamiyoyo yawo zizikwera mtengo .

Koma poyankhulira mbali ya boma, Kunkuyu wati chiyembekezo chilipo kuti ziyenda bwino posachedwapa.

Iye adati boma liri ndi ndondomeko zophulira Amalawi pamoto.

“Pali ndondomeko yomwe akumidzi ogwira ntchito zachitukuko amalandira kangachepe; kale ntchitoyi imakhala ya masiku 12, koma pano taonjezera kufika pa masiku 48 ndipo patsiku azilandira K300.

“Tikukhulupirira kuti anthu akumudzi asangalala,” adatero Kunkuyu yemwe sadanene zomwe boma lakonza kwa anthu okhala mtawuni.

Related Articles

Back to top button