National NewsNkhani

Amalawi aona sabata yakuda

Listen to this article

Pomwe Amalawi akuyembekeza zotsatira za mlandu wa chisankho, sabata ikuthayi kwakhala kuli mpungwepungwe ku Malawi.

Kwa Msundwe ku Lilongwe kudali nkhondo yoopsa pakati pa apolisi ndi anthu mpaka wapolisi mmodzi Usumani Imedi adaphedwa ndi miyala.

Anthuwo amachita zionetsero zokwiya kuti mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika amachititsa msonkhano ku Lilongweko atatsegulira ndondomeko yomanga sukulu zasekondale 250 m’dziko muno.

Mneneri wapolisi James Kadadzera adavomereza kuti wapolisiyo yemwe adali wotsogolera anzake pokakhazikitsa bata, adafera pantchito.

“Amachokera pa C Company ku Lilongwe ndipo adatumidwa kukatsogolera gulu la apolisi okakhazikitsa bata kwa Msundwe koma adangozindikira anthu amuzungulira n’kuyamba kumumenya n’kumamugenda mpaka adafa,” adatero Kadadzera.

Kumeneko kudali kutentha mateyala komanso kuswa magolosale ndi kutseka msewu kuti odutsa azilipira ngati akukhoma msonkho.

Kwa Msundwe zili mkati, kwa Mpingu nako m’boma lomwelo la Lilongwe kudali utsi okhaokha anthu atakwiya ndipo zidatengera asilikali a nkhondo kuti anthuwo abalalike.

Mutharika adapanga msonkhano wachitukuko woyamba m’chigawo pabwalo la Kamuzu Institute chilumbilireni ngati mtsogoleri wa dziko chitachitika chisankho cha pa 21 May 2019.

Kadadzera adati pofika madzulo Lachiwiri pomwe zonsezi zimachitika, apolisi adali atamanga anthu 12 oganiziridwa kuti adatenga nawo mbali pazipolowezo.

Mtsogoleri wachipani cha Malawi Congress Party (MCP) Lazarus Chakwera adati zoti adapanga chiwembu chopha wapolisi ndi ndani kapena wachipani chanji zilibe ntchito koma zomwe zidachitikazo nzolakwika.

Ku Lilongwe kukuyaka choncho, ku Blantyre nako kudali chisokonezo pomwe mavenda a ku Limbe amachita zionetsero zaukali.

Ku Blantyre komweko, ana a sukulu ya Blantyre Secondary School (BSS) nawo adali ndi nthawi yawo yachionetsero posakondwa ndi utsogoleri wapasukulupo, mpaka sukuluyo adaitseka

Katswiri pandale George Phiri wati ichi n’chizindikiro choti zinthu zaonongeka Mmalawi ndipo mpofunika dotolo waluntha kuti dziko lisagwe m’mbuna. n

Related Articles

Back to top button