Nkhani

Amalawi ati boma la PP likusakaza chuma

Listen to this article

Akuluakulu ena ati boma la chipani cha People’s Party (PP) motsogozedwa ndi mtsogoleri wake, Joyce Banda kudzanso wachiwiri wake, Khumbo Kachali lataya chipangano pomwe lasiya kulabada miyoyo ya anthu ake koma kumangoononga chuma cha dziko ngati chiswe.

Mkulu wa Malawi Watch, Billy Banda komanso katswiri wa zandale, Henry Chingaipe, adauza Tamvani m’sabatayi pomwe amawunguza momwe boma likuonongera misonkho ya anthu pofuna kudzikundikira lokha pomwe Amalawi ali pamoto.

Chitsanzo iwo amalankhula momwe misonkho ya anthu yaonongedwera ndi ulendo wa ku United Nations (UN) womwe mtsogoleriyu watenga anthu oposa 40 kuphatikiza mafumu.

Ounikirawa ati pomwe nkhani za chuma zisadakhazikike m’dziko muno, ndikosafunika kuti boma litenge mafumu paulendowo komanso anthu ochuluka amvekere uku ndikuononga chuma posaganizira Amalawi.

‘Kusakaza ngati chiswe’

Malinga ndi malipoti omwe nyuzipepala ya The Nation ya Lachiwiri sabata yatha idapeza, pafupifupi K308 miliyoni ndiyo ionongedwe paulendowo. Ndalamayi ingakwanire kugulira matumba 616 000 a fetereza wotsika mtengo.

Ndalamazi mwazina ndi zolipirira matikiti a ndege komanso ndalama zapadera za omwe wayenda nawo zomwe akuti ndi K84 000 pa munthu mmodzi patsiku.

Koma mneneri wa boma, Moses Kunkuyu, wati sizoona kuti boma akudzikundikira ndipo aiwala Amalawi chifukwa chilichonse chomwe boma likuchita ndichokomera Amalawi.

“Pali maulendo omwe akufunika achitike ndithu ndiye sikuti taiwala. Ndizoonadi kuti paulendowo pali mafumu ena monga Malemia yaku Nsanje koma pali kufunika kwake.

“Mukudziwa kuti bomali likugwira ntchito ndi mafumu pa nkhani ya uchembere wabwino komanso zina ndiye chomwe tikufuna n’kuti akathe kumva momwe mayiko ena zikhalira,” adatero Kunkuyu.

Izi zikuchitika pomwe amabungwe omwe siaboma komanso anthu adzudzula mamulumuzana abomawa kuti achepetse maulendo.

“Bomali likumbuke komwe lachokera, zikuonetsa kuti atsogoleriwa ali pachinyezi ndipo ayiwala Amalawi. Tinkadzudzula boma la DPP zoononga misonkho ndipo ichi sichachilendo kwa iwo koma ife tikudabwa kuti nawonso ayamba zomwezo. Apa asanduka Agalatiya,” adatero Banda.

‘Maulendo achuluka’

Naye Chingaipe wati bomali likulephera kuchepetsa ndalama zogwiritsidwa ntchito maka pamaulendo.

Iye adati ndibwino kuti maulendo ena aboma zizipita nduna zokha kuti ndalama zogwiritsidwa ntchito zichepe.

“Ulendo wa ku UN ndi ulendo wa boma ndipo omwe akuyenera kupita ndi omwe akukhudzidwa ndi nkhani za boma koma zikudabwitsa kuti ulendowo kwapita mafumu ndi ena.

“Kuulendowu kwapita anthu ambiri komanso akukakhala masiku ambiri zomwe ziononge ndalama,” adatero Chingaipe.

Francis Lunga wa m’mudzi mwa Malasa 1 kwa T/A Malengachanzi m’boma la Nkhotakota wati kumeneko zinthu zaipa pomwe anthu akusowa kopezera ndalama chikhalirecho zinthu zikukwera mtengo.

“Tidayamba ntchito yolima msewu ndipo timalandira K300 patsiku koma pano ntchitoyo yayimanso ndipo sitikudziwa mutu wake. Kuno sitikudziwa kuti vuto lenileni kuti zinthu zidzivuta chonchi ndi chani. Izi zili choncho tikungomva kuti alowera uku kapena uko. Maulendo aonjeza,” adatero Lunga.

Abraham Kamanga wa m’mudzi mwa Kandeya kwa T/A Kadewere m’boma la Chiradzulu wati akuganiza kuti boma lidangowanyenga kuti anthu akumudzi salira ndikugwa kwa ndalama ya Kwacha ponena kuti pakhala zowatonthoza. Iye adati n’zodandaulitsa kuti pamene mavuto akula, maulendo akudya ndalama ankitsa.

“Misewu yomwe imakambidwayo sitikulima, palibe chopezera ndalama. Thumba lachimanga lolemera makilogalamu 50 lafika pa K3 600 kuchoka pa K2 500. Chonsecho anthu osafunikira akuyenda nawo m’maulendo osawayanja,” adatero Kamanga.

‘Zinthu ngati madzi zikusowa’

Tifinesi Manjaaluso wa ku Embangweni ku Mzimba ndipo akuchita bizinesi ya zovala wati mavuto sadasiye phazi kumeneko pomwe kuli mavuto amadzi.

“Zinthu zikungokwera mtengo, madzi m’mipope akusiya pena mwina Embangweni yonse zomwe zikutikakamiza kukamwa madzi osatetezedwa. Boma lichitepo kanthu,” adatero.

Mu mwezi wa Meyi chaka chino, boma lidatsitsa mphamvu ya Kwacha ndi K49 pa K100 iliyonse.

Related Articles

Back to top button