Chichewa

‘Amalawi ayenera kuyanjana’

Listen to this article

Sabata ino JAMES CHAVULA akupitiriza kucheza ndi Timothy Mtambo nduna ya zophunzitsa anthu zosiyanasiyana komanso umodzi. Sabata yatha, iye adatambasula nkhani ya amwenye. Adacheza motere:

Timothy Mtambo

Amalawi ena akudandaula kuti mtundu wina wa anthu uli ndi malo ochuluka m’mizinda ya dziko lino. Kodi unduna wanu ukutipo chiyani?

Limeneli ndi vuto lalikulu lomwe taliona m’dziko muno kuti obwera ndiwo akuphangira malo abwinoabwino kulekana ndi Amalawi. Koma funso n’kumati, kodi amawapatsa anthuwa malo ndi ndani? Malowatu samangotola, amakumana ndi Amalawi m’maofesimu, andale, mabwana m’maunduna a boma omwe amati akawanyambititsa, amawapatsa malo abwinoabwino.

Kodi apa vuto ndi ndani? Yemwe akulandira ziphuphu kapena wopereka?

Ngati yemwe akupatsidwa ziphuphuyu angakane kulandira ndiye kuti nkhani za ziphuphu pogulitsana malo zikutha. Choncho pankhani ya malo, tikuyenera kuona momwe malowa tingawagawire kwa aliyense mosakondera.

Kukhala osauka kaya olemera usakhale mlandu. Tikuyenera kupeza njira zothetsera mavutowa, tikuyenera kukambirana komanso tiphunzire kwa anthu ena umo akuchitira.

Tiyeni tikhale osamalitsa kuti izi zisafike pothamangitsa anthu a maiko ena. Si kuti ndi aliyense wobwera yemwe ali kamberembere. Ayi.

Ndiye mukupangapo chiyani?

Boma likuyenera kuika njira zoti anthu ayambe kukambirana za izi. Mabungwe omwe si aboma nawo ali ndi ntchito yopereka chidziwitso ndi kuphunzitsa Amalawi za nkhaniyi.

Kodi unduna wanu ukugwira bwanji ntchito ndi maunduna ena poonetsetsa kuti mwayi ukuperekedwa kwa onse mosakondera pochita bizinesi, pankhani zamalo komanso pogwira ntchito mogwirizana ndi boma?

Boma lathu likufuna kuti tonse tichite bwino ngati momwe mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera amanenera pa imodzi mwa ngodwa zisanu zomanga dziko lino.

Tikuunikanso njira zomwe tingaikire malamulo oyendetsera zinthu ngati zimenezi. Ulamuliro wa Chakwera umalemekeza kwambiri malamulo, choncho

tikuyesetsa kuti lamulo la 60:40 likhazikike pothana ndi mavuto a kusiyanawa komanso tikulimbikitsa kusintha ku malamulo okhudza malo chifukwa ena mwa malamulowa akulimbikitsa kusiyana.

Tikamakonzanso malamulowa, Amalawi adzatenge nawo gawo, adzawamvetse ndi kupereka maganizo awo.

Koma choyambirira ndi kuona gwero la vuto kuti papezekenso njira zabwino zothetsera vutolo.

Kodi unduna wanu wakambiranako ndi maunduna ena?

Eya. Tayamba kale zokambirana ngati boma. Tonse tikudziwa kuti tikuyenera kuchitapo kanthu pothetsa mavuto omwe alipowa akusiyana kwakukulu pakati pa achuma ndi osauka.

Tikuyenera kuthetsa katangale chifukwa amakolezera kuti vuto la kusiyanaku likhale lalikulu.

Yemwe ali n’kuthekera kopereka ziphuphu ndiye alinso ndi kuthekera kwakukulu kopeza malo, kugwira ntchito pa mgwirizano ndi boma.

Kodi chitachitike ndi chiyani kwa Amalawi omwe adagulitsa malo mosatsata malamulo.

Akuyenera kudziwa kuti malo n’chinthu chapamwamba chofunika kusamala osati kubetsa. Chinanso chofunika n’kuwaphunzitsa anthu kuti akhale ndi chidziwitso pa nkhani za malo. Koma a m’boma omwe akukolezera moto pa kusiyanaku, lamulo liwapeza.

Related Articles

Back to top button
Translate »