Nkhani

‘Amalawi dekhani’

Listen to this article

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wati Amalawi asayembekezere kuti zonse zomwe adalonjeza nthawi ya kampeni zingakwaniritsidwe nyengo yochepa chifukwa pali zambiri zoyenera kuchita malonjezowo asadaoneke.

Chakwera adanena izi Lolemba ku Nyumba ya Boma mumzinda wa Lilongwe pomwe amasanthula zomwe boma lake lachita m’masiku 100 omwe lakhala likulamula.

Chakwera adalumbira kukhala mtsogoleri wa dziko pa 28 June 2020

Iye adati akudziwa kuti Amalawi ali ndi njala yofuna kuona dziko lonyezimira msangamsanga koma adachenjeza kuti changu chimadyetsa nsima yosapsa.

“Zinthu zimachitika pang’onopang’ono. Pali ndondomeko zomwe zimatsatidwa kuti mpaka uphule nsima yoti munthu akamadya azimva kuti akudya nsima,” adatero Chakwera.

Mwa zina zomwe boma la Tonse Alliance lidalonjeza ndi kudya katatu patsiku, mswahara wa K15 000 pa mwezi kwa okalamba, zitupa zoyendera za K14 000, fetereza wotsika mtengo kwa aliyense, ntchito 1 miliyoni kwa achinyamata m’chaka choyamba, feteleza waulele kwa osaukitsitsa ndi sabata yogula katundu kunja popanda msonkho.

Chakwera adasanthula zinthu 35 zomwe akuti boma lake lakwaniritsa pamasiku 100 koma akadaulo ati ngakhale Chakwera akunena zoona kuti n’zosatheka kukwaniritsa malonjezo nthawi yomweyi, sizoona kuti zomwe wasanthulazo n’kukwaniritsa lonjezo lililonse.

Zina mwa zomwe Chakwera adasanthula ndi kutsata malamulo, ulamuliro wabwino, kuthana ndi katangale, kutsata utsogoleri wotumikira, kulimbikitsa kuchita zinthu poyera komanso kukhazikitsa lamulo loti anthu azitha kupeza mauthenga kuchokera ku maofesi a boma mosavuta.

Iye adatinso boma la Tonse Alliance likusintha zinthu zambiri m’boma monga kagwiridwe ntchito ka wailesi ya boma ya MBC komanso kukhazikitsa kuti banki yaikulu iziunikidwa pafupipafupi.

Chakwera adakodwa pomwe atolankhani adamufunsa kuti afotokoze chifukwa chomwe sadasankhire amayi m’maudindo ngati momwe adalonjezera komanso kuti afotokozere achinyamata za ntchito 1 miliyoni zomwe adalonjeza.

M’kuyankha kwake, Chakwera adati pomwe maudindo amasankhidwa iye adalibe maina ambiri aamayi omwe ali n’kuthekera kotsogolera m’mipando yosiyanasiyana. Iye adatinso pali masitepe angapo oyenera kutsata kuti ntchito 1 miliyoni zipezeke.

“Zinazi sizingachitike lero ndi lero, masiku 100 siambiri ayi kotero zomwe zathekako ndi zomwezo zina zizichitika pang’onopang’ono. Chomwe Amalawi achite n’kudekha,” adatero Chakwera.

Koma kadaulo pa kayendetsedwe kabwino ka zinthu Vincent Kondowe wati zomwe adasanthula Chakwera ndi akalozera chabe a momwe angakwaniritsire malonjezo ake osati kuti wakwaniritsa kanthu kalikonse.

“Tikuvomera kuti wayamba bwino, chiyembekezo chilipo chifukwa zomwe adanena zija zikusonyeza momwe wakonzera kukwaniritsa malonjezo ake ndiye timumvetsa kuti timudikire pang’ono,” adatero Kondowe.

Iye adati mpomveka kuti Amalawi adikire pang’ono chifukwa ngakhale bajeti yoyamba ya boma laTonse Alliance siyidadutse ndiye pa masiku 100 adalibe mphamvu zokwanira zopangira matsenga.

“Chachikulu tiziona maziko kuti nyumba iyima apa ndiye kuti tizilimba mtima kuti tikulowera kolondola koma padakalipano sitingadye dowe tisadabzale chimanga n’komwe,” adatero Kondowe.

Kadaulo pa ndale George Phiri adati ngakhale pempho la Chakwera lofuna nthawi lili lomveka, Amalawi akufunika kuzitsata pofuna kudziwa komwe dziko lawo likulowera.

“Nthawi ndi imeneyo koma zisatanthauze kuti Amalawi angokhala chete chifukwa n’zomwe zimaononga utsogoleri, anthu apitirize ndithu kusokosa mpaka tsogolo liyambe kuoneka chifukwa chinthu chilichonse chimaonekera kumayambiriro,” adatero Phiri.

Iye adati boma la Tonse Alliance lidalephera kusonyeza kudzipereka kwake pokwaniritsa malonjezo m’bajeti yake yomwe zambiri zomwe ankalonjeza sizidapatsidwe chidwi chilichonse kapena kungoonetsa kuti atsata njira iti.

“Pali zambiri zomwe adalonjeza zoti sitingayambe kudutsamonso pano ayi koma mubajeti yawo muli zina. Amayenera kungopereka chithunzithunzi choti ngakhale zinthuzo sizikwaniritsidwa m’bajeti iyiyi, koma ayambapo kuswa mphanje zokwaniritsira,” adatero Phiri.

Iye adati pano Amalawi akudikira miyezi isanu yomwe adati ikadzatha adzasanthula momwe nduna zawo zagwirira ntchito zake.

Mkulu wa bungwe loona za chitukuko ndi kayendetsedwe kachuma la CDEDI Silvester Namiwa sadapsatire mawu koma kungokhadzula kuti boma la Tonse lidanyenga Amalawi popereka malonjezo onona omwe likulephera kukwaniritsa.

“Tikuona ndi maso athu kuti adalonjeza zina koma apa tikumva zina, mwachitsanzo ankati fetereza otsika mtengo kwa aliyense koma pano akusankha, ankanena zodya katatu koma sizikuwoneka. Pamenepa akutengera Amalawi kumtoso,” adatero Namiwa.

Koma akadaulo omenyera ufulu wa amayi ati mayankho omwe adapereka Chakwera okhudza kupeleka mipando kwa amayi m’boma ndiwosamveka.

Mkulu wa bungwe la Women Legal Resource Centre (Wolrec) Maggie Kathewera Banda adati Chakwera wakanika kukwaniritsa lonjezo lake lotukula amayi m’maudindo.

“Pulezidenti akuti amayi sadapereke zowayenereza kukhala m’maudindo n’chifukwa chake sadawasankhe, kodi abambo ndiye adapereka zoyenereza zawo,” adatero Kathewera Banda.

Related Articles

Back to top button