Chichewa

Amalawi valani dzilimbe—Mutharika

Listen to this article

 

 

Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika dzulo watsegulira nkhumano ya aphungu a Nyumba ya Malamulo yokambirana ndondomeko ya chuma choyendetsera boma kuyambira chaka chino mpaka cha mawa mmene ati muli mfundo zokhwima zomwe zithandize kutukula dziko lino, makamaka pantchito zaulimi, mtengatenga, migodi ndi zokopa alendo.

Mutharika adati ngakhale boma lidalephera kukwaniritsa zina mwa zomwe zidali mundondomeko ya chuma ya 2015/2016 kaamba ka zovuta zina, monga ngozi zogwa mwadzidzidzi, ndondomeko yomwe aphungu akambirane pano ikhala yakupsa.

Has he failed the youth? Mutharika
Peter Mutharika

“Ndondomeko ya chaka chatha idakumana ndi zovuta zambiri monga madzi osefukira ndi mvula ya njomba kaamba ka kusintha kwa nyengo ndipo izi zidasokoneza ntchito zambiri,” adatero Mutharika.

Mfundo zina zomwe Mutharika adakambapo ndi kupitiriza pologalamu ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo ya sabuside yomwe adati chaka chatha idapindulira anthu 1.5 miliyoni.

Iye adatiso ndondomekoyi ipitiriza kupititsa patsogolo ntchito za ulimi wamthirira pofuna kuonjezera zokolola  zomwe alimi amapeza paulimi wodalira mvula.

“Ntchito zamthirira zipitirira. Monga mudziwa, nthitozi zidayamba kale m’madera monga kuchigwa cha Shire ndi madera ena kudzera m’ndondomeko ya Green Belt Initiative,” adatero Mutharika.

Iye adati mwa zina boma lidagula ma treadle pump 4 000 othandizira alimi m’madera osiyanasiyana kuti ntchitoyi ipitilire ndi kubereka zipatso.

Mtsogoleriyu adatiso polingalira kuti chaka  chino kuli njala, boma lidapereka kale ndalama kubungwe la Admarc kuti ligule chimanga alimi akakolola komanso kunja kwa dziko lino.

Pa zamtengatenga, Mutharika adati ndondomekoyi ipitiriza ntchito yomanga ndi kukonza misewu m’zigawo zosiyanasiyana komanso ilimbikitsa ubale ndi maiko oyandikana nawo monga Mozambique ndi Zambia kuti agwirizane zotsegula doko la Nsanje.

Patchito zokopa alendo, Mutharika adati nthambi ya zokopa alendo ndi nthambi yomwe ingathandize kutukula dziko lino ngati Amalawi eni ake angakhale oyamba kutukula ntchitozi.

Iye adatinso ndondomekoyi ilimbikitsa kupititsa patsogolo  ntchito za migodi pofuna kuonetsetsa kuti dziko lino likupindula nawo pantchitozi.

Ndondomekoyi akuti ipititsanso patsogolo ntchito za malonda polimbikitsa kukopa makampani akunja ndi a m’dziko mommuno kutsegula mafakitale ndi mabizinesi osiyanasiyana. Iye adatiso akhazikitsa komiti ya anthu 200 oti afufuze chomwe chidayambitsa mchitidwe wopha ndi kuzunza maalubino, mchitidwe womwe wafika poipitsitsa m’dziko muno.

M’sabata zingapo zikudzazi, aphungu a ku Nyumba ya Malamulo akhala akukambirana zomwe walankhula Mutharikazi kuphatikizapo mabilu ena  ndi ndondomeko ya chuma cha 2016/ 2017. n

Related Articles

Back to top button
Translate »