Chichewa

‘Amatsutsanabe zamakumanidwe awo’

Listen to this article

 

Ambiri akapezana nkukondana nkugwirizana za banja amakhala ndi chikumbumtima cha komwe ndi mmene adakumanirana, koma ndi nkhani yochititsa chidwi kumva za Chiyembekezo Focus Maganga ndi Lydia Kalonde.

Awiriwa akuti mpaka lero sagwirizanabe za malo ndi tsiku lomwe adakumana koyamba ndipo chomwe amakumbukirako nchakuti mudali m’chaka cha 2013 ndipo adapanga chinkhoswe pa 7 June 2013.

“Chomwe ndimakumbuka ine nchakuti ndidakamupeza kuofesi yake nditapita ndi mnzanga Dickson Kashoti pomwe iye amakakamira kuti tidakumana koyamba m’minibasi koma kwa ine uku kudali kukumana kwachiwiri,” adatero Focus.

Focus ndi Linda pachinkhoswe chawo
Focus ndi Linda pachinkhoswe chawo

Panthawiyo nkuti Focus akugwira ntchito ya utolankhani pomwe Lydia adali wothandizira mkulu wa zofalitsa mawu kuunduna wa zofalitsa mawu komwe ali mpaka pano.

Focus adati poti awiriwa alibe tsiku lokhazikika lomwe angati adakumana koyamba, chomwe amakumbukira nchakuti atakumana kuofesi ya Lydia adangopatsana moni polingalira kuti idali nthawi ya ntchito.

Kwinaku akuti amakumbukira kuti atakumana m’minibasi Lydia adali ndi chidwi ndi momwe iye adavalira, suti yapamwamba koma tsitsi losapesa ndipo m’maganizo mwake amangoti mwina wadzuka ndi mowa m’mutu.

“Ngakhale adali ndi maganizo oterewa, macheza adayenda bwino mpaka posiyana tidapatsana nambala za foni n’kumaimbirana mwakathithi mpaka chibwenzi chidayamba,” adatero Focus.

Iye adati chitachitika chinkhoswe iwo adalowana asadapange ukwati pofuna kukonzekera mofatsa ndipo akuti ukwatiwo ukhalako kumapeto kwa chaka chino.

Focus akuti amakonda kwambiri Lydia chifukwa ndi wooneka bwino, wanzeru, wachikondi, woopa Mulungu komanso amamuthandiza nzeru ndi kumulimbikitsa akamafooka.

Naye Lydia akuti amamukonda kwambiri Focus kaamba ka zochitika zake komanso masomphenya ndi kulimbikira pochita zinthu.

“Amapanga zondisangalatsa komanso ali ndi khama ndi luntha pochita zinthu. Tidapezana okonda kupemphera tokhatokha komanso ansangala,” adatero Lydia.

Focus amachokera m’mudzi mwa Chagunda, kwa T/A Changata m’boma la Thyolo, pomwe Lydia amachokera m’mudzi mwa Nsiyaludzu, kwa Inkosi Makwangwala m’boma la Ntcheu. n

Related Articles

Back to top button
Translate »