Nkhani

Ampingo avula gule zigoba

Listen to this article

Madzi achita katondo kwa Kansonga m’dera la mfumu Chilowoko, m’boma la Ntchisi komwe Akhristu a mpingo wa CCAP wa Biwi adavula zigoba za gule wamkulu yemwe adakasononeza msonkhano wawo wachitsitsimutso.

Sabata yapitayi, Akhristu a mpingo wa Kanjiwa adali ndi msonkhano wachitsitsimutso pampingo wa Biwi. Msonkhanowo udatenga masiku atatu, kuyambira Lachisanu kufikira Lamulungu.

Anthu ena amayerekeza gulewamkulu akafuna kuchita chiwembu

Malinga ndi omwe atitsina khutu omwe amachita malonda pamsikawo, ulaliki umatsindika kwambiri za gule wamkulu zomwe sizidasangalatse akuluakulu a kumzinda.

Ndipo pofika Lamulungu gule wokwana 7 adatulukira pamalo a chitsitsimutsowo kuti akasokoneze, koma Akhristuwo adagwirapo zirombo ziwiri ndi kuzivula zigoba ndipo zirombo zinazo, zitaona izi zidathawira kudambwe.

Polankhulapo, Mfumu Chilowoko ya m’bomalo yati ikufufuzabe za nkhaniyi kuti idziwe ngati ‘mizimuyo’ idawedzedwa ndi mfumu ya mzinda.

“Nthawi zina anthu ena amangoyeserera gule wamkulu ndipo awa ndi omwe amangotuluka paokha opanda mfumu ya mzinda chifukwa kuti titsimikize kuti uyu adalidi gule, pafunika chitsimikizo chochoka kwa mfumuyi,” adatero Chilowoko.

Iye adatinso pali chikaiko choti guleyo adali wovomerezeka chifukwa mfumu yaikulu ya Achewa Kalonga Gawa Undi adaletsa kuwedza gule malinga ndi mlili wa Covid-19.

“Koma zikapezeka kuti n’zoona kuti guleyu adali wa mzinda ndipo akapezeka wolakwa, timalipiritsa mbuzi kapena kuposera apo chifukwa ife ngati Achewa timafuna mabungwe onse azikhala mwamtendere opanda

chiopsezo,” adatero Chilowoko.

Malinga ndi iye, nkhani yomwe wamvetsedwa ndi yoti nawo a mpingo pachitsitsimutso chawo amangokamba za gule wamkulu zomwe sizidakomere agulewo.

“Pakadalipano tingodikira kuti apolisi atiuze pomwe nkhaniyi ili chifukwa ndauzidwa kuti idakafika m’manja mwawo, monga mukudziwa anthu salowa mabwalo awiri,” adalongosola Chilowoko.

Koma iye adanenetsa kuti apolisiwo akathana nazo za mzinda alekere eni chikhalidwe omwe ndi mafumu omwe amakawedza gule kumanda.

Koma mneneri wa polisi m’boma la Ntchisi, Richard Kaponda adati nkhaniyo siyidafike kupolisi chifukwa mbali zonse zokhudzidwa zidangokambirana pazokha.

Nawo a bungwe losungitsa chikhalidwe la Chewa Heritage Foundation (Chefo) adati atumiza ku maloko mkulu woyang’anira nkhani za mafumu komanso chikhalidwe kuti akafufuze chidatsitsa dzaye kuti njovu itchoke mnyanga.

Wapampando wa bungwelo George Kanyama Phiri adati mpungwepungwe pakati pa mpingo ndi a gulewamkulu wakhala ukusowetsa mtendere kwa kanthawi tsopano.

“Akamati gulewamkulu ndi usatana, tikufuna akonze pomwe pali usatanapo,” adalongosola Phiri. n

Related Articles

Back to top button