Chichewa

Amukwenya ponena olumala kuti ‘agalu’

 

Banja lina lapempha mkulu woyang’anira za maphunziro m’maboma a Phalombe, Mulanje ndi Thyolo (Divisional Education Manager—DEM) kuti athane ndi mphunzitsi wina amene akumuganizira kuti adanena ana olumala pasukulu ya sekondale ya Phalombepo kuti ndi ‘agalu’.

Kalata yomwe tapeza, yatumizidwanso kwa wachiwiri kwa mkulu woyendetsa maphunziro a ana olumala, mkulu wa sukulu ya Phalombe, mkulu wa bungwe la anthu amene ali ndi vuto la kumva la Malawi National Association for the Deaf (Manad), mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a anthu olumala la Federation of Disability Organisations in Malawi (Fedoma) ndi ena.

disability

Malinga ndi kalatayi, mpunzitsiyo akuti adachita izi pa 2 February pamene banjalo lidapita kukaona mwana wawo.

Kalatayo, yomwe walemba ndi mmodzi mwa a pabanjapo, Bettie Chumbu, yati patsikulo iwo atafika pasukulupo adakumana ndi wophun-zirayo ndipo adali ndi ophunzira anzake a mavuto osiyanasiyana achibadwidwe.

Sukuluyi, malinga ndi mphunzitsi wamkulu, James Kamphonje, ili ndi ophunzira azilema zosiyanasiyana monga achialubino, osamva, osalankhula ndi ena. Onse pamodzi akuti alipo 15.

Chumbu adati akucheza ndi ophunzirawo mpamene mphunzitsiyo adatulukira, “botolo la mowa lili m’manja” n’kunena mawu amene adawakwiyitsawo.

“Adati, ‘mukuchita chiyani ndi agaluwa?’,” adatero Chumbu. Akuti adamufunsa mphunzitsiyo zomwe ankatanthauza ponena mawu amenewo, koma iye akuti adabwereza mawuwo, amvekere: “Yes these are dogs [Inde, awa ndi agalu].”

Gwen Mwamondwe, yemwe ankayendetsa galimoto yomwe adakwera Chumbu popita kusukuluko ndi Hussein Chindamba, yemwe adatsagana ndi nawo paulendowo, adatsimikiza za nkhaniyi ponena kuti adayesetsa kuuza mphunzitsiyo kuti zomwe wayankhula zidali zopanda mutu ndipo ayenera kupepesa, koma akuti zidakanika mpaka ana asukulu ena ndiwo adalowererapo n’kumududa pamalopo.

Koma Lachiwiri Msangulutso utafuna kumva mbali ya mphunzitsiyo, adangoti: “Tilankhulane cha m’ma 5 koloko kuti ndiyankhepo.” Koma titamuimbira kangapo, iye sadayankhenso foni.

Kumbali yake, Kamphonje adati nkhaniyi ili pakati pa banja lodandaula ndi mphunzitsiyo ndipo mbali ziwirizi zikukambirana.

“Chomwe ndikudziwa nchakuti banja lodandaulalo likukambirana ndi Malikebu, zomwe agwirizane timva kwa iwo,” adatero mphunzitsi wamkuluyu amene adakana kulankhulapo zambiri.

Titamufunsa Chumbu ngati akukambirana ndi mphunzitsiyo, iye adati: “Nkhani tidaisiya m’manja mwa akuluakulu ndiye palibe chifukwa choti tiyambe kukambirana ndi mphunzitsiyu. Koma wakhala akundiimbira foni kuti tikambirane.

“Mafoni amene akuimba sindikuwayankha ndipo mmalo mwake adanditumizira uthenga wapafoni kuti ‘ndikupepesa kuti mundikhululukire. Ndikukudikirirani kuti ndidzapepese pamaso. Chonde ndikhululukireni, sizidzachitikanso, Mulungu akudalitseni’.”

Mkulu woyang’anira maphunziro m’maboma a Thyolo, Mulanje ndi Phalombe, Christopher Nauje, adati akudikira lipoti kuchokera kwa banja lolakwiridwa. “Ndidalankhuladi palamya ndi abanja lodandaula pankhaniyi ndipo ndidawauza kuti atumize dandaulo lawo kuofesi yathu polemba kalata. Panopa ndikudikirabe kalatayo ndiye sindingayankhepo kanthu,” adatero Nauje.

Mkulu woona za maphunziro a olumala muunduna wa zamaphunziro, David Njaidi, adatsimikiza kuti walandira dandaulo kuchokera kubanja lodandaula ndipo wati akhala pansi kuti aone chomwe angachite.

“Apa chatsala nchakuti tikambirane ndipo tipereke zomwe tapeza komanso zomwe tingachite ndi mphunzitsiyo,” adatero Njaidi.

Kodi ngati mphunzitsiyo atapezeka wolakwa achita naye chiyani?

Njaidi adati: “Aka nkoyamba kumva kuti mphunzitsi akuchita zotere. Komabe tikambirane kaye. Amene timapereka zilango si ife, pali nthambi ina yomwe timaipatsa zomwe tapeza ndipo iwo ndi amene amaona chomwe achite.” n

Related Articles

Back to top button