Chichewa

Amwalira atathawa m’chipatala

Listen to this article

Mayi wina wa zaka zapafupifupi 60 adamwalira maola anayi,atathawitsidwa m’chipatala cha paboma la Nkhotakota ndi abale ake, atamupeza ndi matenda a Covid 19 Lachiwiri.Malinga ndi mneneri wa pachipatalacho Garry Chilinga, mayiyu adabwera pachipatalapo akubanika komanso kuonetsa zizindikiro zonse za matendawa.

Iye adati mayiyo adatumizidwa kuchokera kuchipatala cha mishoni cha Saint Annes m’bomalo komwe adamuyeza malungo ndipo sadawapeze.

Atamuona kuti akubanika ndipo akufunika oxygen, adamutumiza kuno.Atangofika tidamuika pa oxygen kenako tidamuyeza matenda a Covid-19 ndipo tidamupezadi nawo koma abale ake adakana kuti timugoneke ndipomwatsoka adamwalilira kumudzi kwawo patadutsa maola ochepa,” iyeadalongosola.

Chilinga adati abale ake adakanitsitsa kuti gogoyo sangadwale Covid-19 koma kuti achipatala amangofuna kudyerapo ndalama pa mbale wawo.

“Ife ngati achipatala palibenso chomwe tikadachita koma kuwasiya apite. Nkhawa yathu yagona pakuti anthu a m’mudziwo komanso omwe amasamalira matendawo nawo ali pachiopsezo chachikulu cha matendawa zomwe zikhoza kukweza chiwerengero cha odwala m’boma lino,” adtero Chilinga.

Iye adaonjezera kuti ngati achipatala akukanika kupitanso kumudzi kwamayiyo kuti akayeze anthuwo poopa kukachitidwako chipongwe.

Related Articles

Back to top button
Translate »