Chichewa

Ana achoke m’minda—Nduna

 

Mvula yagwa Madera ambiri moti anthu ali kalikiriki m’minda kuthira manyowa, kubzala ndi kuwokera koma nkhawa yaikulu yagona pamchitidwe wogwiritsa ana achichepere ntchito za kumunda pofuna kuzemba mtengo wa anthu aganyu. Chaka chino, boma laneneratu kuti silidzasekerera munthu aliyense wopezeka akugwiritsa ana achichepere ntchito m’munda. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi nduna ya zamalimidwe Dr Allan Chiyembekeza pankhaniyi.

A nduna, tamva mukuchenjeza za mchitidwe wogwiritsa ana achichepere ntchito m’munda, kodi mungatambasulepo bwino pamenepa?

Eya, pamenepa tikutanthauza kuti pali anthu ena omwe amaganiza molakwika, mmalo moti azilimbikitsa ana kupita kusukulu, iwo amalemba ana ochepa msinkhu kwambiri ntchito m’minda makamaka pano pomwe fodya wagundika.

Mayi ndi mwana wake wachichepere kuchita ganyu m’munda wa fodya. Ana sayenera kugwira ntchito zoposa msinkhu wawo
Mayi ndi mwana wake wachichepere kuchita ganyu m’munda wa fodya. Ana sayenera kugwira ntchito zoposa msinkhu wawo

Kodi kumeneku n’kulakwa?

Kulakwa kwambiri moti ngakhale malamulo a dziko lino zimenezi salola, mwana amayenera kuti azipatsidwa nthawi yokwanira bwino yolimbikira maphunziro. Mwana yemwe amakhalira kugwira ntchito zoposa msinkhu wake monga zakumundazo, amakhala wotopa paliponse ndiye sangalimbikire maphunziro.

 

Ndimayesa kumeneku n’kuphunzitsa mwana ntchito?

Ayi kumeneku n’kuzunza mwana osati kumuphunzitsa ntchito, ayi. Munthu aliyense amakhala ndi nthawi komanso msinkhu womwe angagwire ntchito zamtundu wina wake osangoti basi tiyeni watopa azikapumira komweko, ayi, n’kulakwa kwakukulu kumeneku.

Chiyembekeza: Ana azipita kusukulu, osati kumunda
Chiyembekeza: Ana azipita kusukulu, osati kumunda

Kodi vuto limeneli ndi lalikulu bwanji?

Vutoli ndi lalikulu ndithu komabe poti tidayamba kale kudziwitsa anthu za nkhanza zopita kwa ana makamaka pankhani yowagwiritsa ntchito yoposa msinkhu wawo, anthu ena adamvetsetsa ndipo adasintha koma alipo ena omwe amakhulupirira kuti mwana safuna malipiro ambiri akagwira ntchito ndiye amaona ngati chidule kugwiritsa mwana ntchito kusiyana ndi munthu wamkulu.

 

Koma zimakhala bwanji anawo sachita kukafunsira ntchitoyo okha?

Tikudziwa za nkhani ya umphawi mmene ilili. Ana ambiri akhozadi kukafunsira ntchito okha kuti apezeko mwina chakudya komanso ndalama zodzithandizira kumavuto osiyanasiyana. Ambiri amakhala oti mwina alibe makolo kapenanso iwo ndiwo akuyang’anira ana anzawo ndiye palibe chomwe angachite, pogwira alibe. Ambiri mwa ana omwe amakumana ndi nkhanza zamtundu umenewu ali m’gulu limeneli.

 

Nanga munthu utakhala ndi ndalama zolipira aganyu mwana uja n’kukupeza kuti akufuna ganyu kuti athandizike ungatani?

Apa mpamene pamabwerera mtima wa umunthu. Ngati munthu wamkulu uli ndi udindo wongothandiza mwanayo ngati uli ndi thandizo kapena kumuunikira kuti aike maganizo pasukulu osati maganyu. Ambiri mwa anawa amachokera m’madera momwe ifeyo timakhala ndipo mbiri yawo timayitsata tsono chotiletsa n’chiyani kungowathandiza?

 

Nanga poti anthu ena amagwiritsa ntchito ana awo omwe. Anthu oterewa sangadziteteze kuti ndi ufulu wawo poti mwanayo ndi wawo?

Malamulo a dziko lino amaneneratu poyera kuti mwana aliyense apite kusukulu osati azikagwira ntchito m’munda, ayi. Palibe munthu yemwe ali ndi mphamvu zilizonse zosintha malamulo amenewa. Ngati lamulo likuti ichi ayi ndi ayi basi.

 

Ndiye mukungodziwitsa anthu palibe zilango zake?

Lamulo lililonse labwino limakhala ndi zilango zomwe olakwa angalandire ataliphwanya. Tikadzapeza munthu wolemba kapena kugwiritsa ana ntchito, tidzamutengera kubwalo la milandu komwe akagamulidwe potsatira zomwe malamulo akunena ndipo sitidzalola kuti anthu oterewa apatside ufulu wosalandira chilango.

 

Ndi ntchito zanji zomwe ana amagwira m’mindamu?

Pali ntchito zosiyanasiyana. Ena amawanyamulitsa manyowa, kuwaza manyowa, kupanga mizere, kubzala mbewu, kuthena, kuthyola, kunyamula ndi kusoka fodya. Ntchito zina ndi monga kukolola mbewu monga chimanga, nyemba, soya ndi mbewu zina. Ena ndiye amawonjeza mpaka kumathiriritsa ana mbewu kukakhala ng’amba. Nanga choncho mwana ngati ameneyu angakhale ndi maganizo a sukulu?

 

Pomaliza penipeni muwauzanji Amalawi?

Amalawi tiyeni titeteze ana posawalemba kapena kuwagwiritsa ntchito zoposa msinkhu wawo. Ndi ana athu amenewa tiwapangire tsogolo lowala osati kuwakumbira dzenje chifukwa kutero, mawa lino dziko lathu lidzakhala losaukabe

Related Articles

Back to top button