Chichewa

Ana avala umasiye Makolo akali moyo

 

Nthawi ya nkhomaliro yakwana, pamsika wa Manje mumzinda wa Blantyre ambiri akudya nsima pamene ena akusaka chakudya.

Kuponya maso patali pali ana atatu, Fakili wa zaka 8, Pemphero, 7, ndi Yamikani 4. Pemphero lawo nkuti apeze chakudya. Anawa aima pafupi ndi mpanda wa mfumu Misesa.

“Tikufuna tipemphe mango, tilibe chakudya,” adatero Fakili, uku akutonthoza Yamikani amene akulira chifukwa chomukaniza kutoleza makoko a mango.

Uwu ndiye umasiye omwe anawa auvala makolo awo ali moyo. Zonsezo zikuchitika chifukwa makolowo sakumwetsana madzi. Kumenyana kwa njobvu, wovutika ndi udzu.

Fakili akulephera kufotokoza bwinobwino chomwe chidachitika kuti ayambe kukhala moyo wovutika choncho.

Fakili (Kumanja) ndi abale ake Yamikani ndi Pemphero

“Amayi sakutifuna…. komanso ababa adachoka koma pena amatisaka,” adatero iye.

Mfumu Misesa ikuti anawa si achilendo m’dera lake.

Gulupuyu akuti patha mwezi anawo akungoyendayenda m’dera lake. “Kunyumba kwanga agona masiku awiri,” adatero iye.

Uko atawathyolera mango kuti azikukuta, Misesa adati banja la makolo a anawo lidatha ndipo kuchokera pa nthawiyo, anawo akhala akuzunzika.

“Ndidawaitana onse kuti tikambirane koma zidakanika. Mkazi akuti iye adapeza banja lina ndipo sangasunge anawa pamene bamboyo ali ndi chidwi chowasunga koma akuti sangathe chifukwa alibe pokhala komanso ntchito idatha,” adatero Misesa.

Lolemba Msangulutso udakumana ndi bambo wa anawa. Bamboyo, Dave Singano adati mtima wosunga anawo ali nawo koma sangathe chifukwa alibe thandizo.

“Zikundiwawa kuti anawa akuzunzika komabe palibe chomwe ndingachite chifukwa ndilibe thandizo. Ndilibenso pogona, ndiye ngakhale ndiwatenge akagona potani?” adatero Singano.

Bamboyu adati patha zaka zitatu chisiyirane ndi mkazi wake. Iye adati adathetsa banja lake pomuganizira mkaziyo kuti akumuyenda njomba.

“Panthawiyo ndinkagwira ntchito ya ulonda. Ndiye anthu ena adanditsina khutu kuti ndikachoka kukumabwera mwamuna m’nyumbamo. Nditakambirana ndi mkazi wanga sitidamvane ndipo banja lidatha,” adatero.

Singano akuti adagwirizana ndi mkazi wake komanso amfumu kuti anawo akakhala ndi mkaziyo ndipo iye azipereka thandizo.

“Panthawiyo zidachitika momwemo, koma kungotha miyezi yochepa adasintha pamene adati sangakwanitse kukhala ndi anawo poti wapeza mwamuna wina.

“Ndidakhala ndi anawo komabe nanenso zidandisokonekera, ntchito idatha, adandichotsa palendi. Ndikadatani?” adatero Singano.

Iye adati patha chaka chimodzi tsopano anawa akukhala wokha, “komabe ndikapeza thandizo ndimawasaka. Monga dzana [Lamulungu] ndidawatenga ndipo ndidakagona nawo ku Chilobwe kwa mnzanga,” adatero iye.

Naye mkazi wa bamboyu akuti adauza bwalo la mfumu Misesa kuti sangatenge anawo chifukwa adakwatiwanso.

“Adauza bwalo kuti anawa sakuwatenga, patsikulo adabwera ndi mwamuna wake watsopanoyo. Nditamuitananso kuti tidzakambirane sadabwere mpaka lero,” adatero Misesa.

Gawo 60 loteteza ana, limati kholo lolephera kusamala ana ake liyenera kunjatidwa.

Misesa akuti nkhaniyi idapita kupolisi ndipo apolisi adanjata bamboyo koma adamutulutsa tsiku lomwelo.

Koma mkulu womenyera ufulu wa ana kubungwe la Centre for Children’s Affairs Malawi, Moses Busher adadzidzimuka ndi nkhaniyo ndipo adati makolowa akuyenera kunjatidwa.

Iye adati bungwe lawo litengera nkhaniyo kukhoti la ana. “Ngati bungwe lomenyera ufulu wa ana, nkhaniyo sitiyisiya mpaka anawa athandizidwe. Mayi akuyenera kusunga anawo mosayang’ana kuti wakwatiwa kapena ayi ndipo bamboyo akuyenera kumawathandiza. Tifufuza ndipo ana amenewa athandizidwa,” adatero Busher.

Atafunsidwa ngati ndikololedwa kuti anawa atengedwe ndi banja lina kukawasunga ngati ana awo, Busher adati ndizotheka pokhapokha ndondomeko itatsatidwa.

“Koma poona kuti makolo awo onse alipo ndipo izi zangochitika chifukwa cholekerera, zifukwa zotenga anawa kukhala ako sizikumveka,” adaonjeza.

Pamene mutu wa nkhaniyi ukufufuzidwa, moyo wa anawo udakali pamavuto adzaoneni.

Kusukulu sapita, pogona ndi kubowo kwa uvuni ya njerwa, m’kalasi, apo ayi apemphe pakhomo pa eni. Chakudya chawo ndi mango, misonga ya mzimbe ndipo akadya bwino ndiye kuti banja lina lawagawira.

Nawo moyo wa Pemphero, yekhayo wamkazi ndiwosokonekera chifukwa adapsa ndi madzi kuyambira m’khosi mpaka kuphazi. n

Related Articles

Back to top button