Chichewa

Anatchereza

Listen to this article

Mkazi wanga koma mkonono

Agogo,

Langa ndi dandaulo pa mkazi wanga wokondeka. Iyetu mwano alibe ndiponso ntchito amagwira molimbika. Abale anga amawalemekeza ndipo ana athu akuloledwa bwino. Koma chimodzi, mkazi wanga mkonono. Ndichite chiyani?

YH,

Zomba.

 

YH,

Zoonadi mkonono nthawi zina umasokoneza anthu ena. Komatu ichi si chifukwa choti n’kudana nawo.

Muziwalimbikitsa akazi anuwo kuti azigona chambali kapena kuti champeni, osati chagada.  Mudziwe kuti nthawi zina mkonono umadza chifukwa munthu ndi wonenepa kwambiri. Choncho alimbikitseni akazi anuwo azichita masewera olimbitsa thupi kuti mwina thupi n’kuchepako komanso kusamala zimene amadya kuti zisakhale zonenepetsa kwambiri.

Nthawi zinanso, kumwa mowa kwambiri ngakhalenso kusuta kumakuza mkonono. Kusiya izi kukhonza kuthandiza.

Koma ngati zikupitirira, mukhonza kumatchinga makutu anu ndi zinthu zina monga thonje. Ngati nyumba yanu ndi ya zipinda zingapo, mukhonza kumakagona chipinda china. Machitidwe a m’banja muziona nokha.

 

Mwamuna wanga ulesi

Zikomo Anatchereza,

Ndidakwatirana ndi mwamuna wanga chaka chatha koma ndiwaulesi osati masewera. Ndimagwira ntchito masiku ochuluka ndine ndipo ndikabwera amayembekezera kuti ndiphike ndine komanso kukonza m’nyumba. Nthawi zonse ndimakhala otopa moti sabata iliyonse ndimapita kwa makolo anga kuti ndikapumeko. Ndichite naye chiyani?

AB,

Lilongwe.

 

AB,

N’zomvetsa chisoni kuti amuna ena akadali ndi moyo woti ntchito zonse azigwira ndi amayi. Kukakhala kumudzi, mupeza amayi ndi abambo apita limodzi kumunda kukalima. Pobwera uko, amayi asenza nkhuni kumbuyo atabereka mwana.

Kufika pakhomo, amayiwo amapita kumadzi, kenako kuphika nsima ndi ndiwo. Chonsecho abambo akusewera bawo.

Khalidwe ili ndi lachikale. Zoti ntchito zonse zapakhomo azigwira ndi mayi zidapita. Mukuyenera kulankhula naye mwamuna wanuyo chifukwa izi sizikuthandizani.

Komanso mopempha, zothawira kwa makolo anu sizikuthandizani. Kumeneko sikuthana ndi vuto koma kungolikankhira kaye pambali.

 

Adakwatiwa ndi ndale?

Anatchereza,

Ndimanyadira ndi malangizo anu. Kale, ndinkaona ngati sindingakhale ndi vuto mpaka kukuuzani. Koma izi zandikulira.

Mkazi wanga koma ndale. Chingasinthe chipani cholamula, iye amapezeka nsalu ya chipanicho ali nacho. Ndipo kukangoti kuli msonkhano, timayembekezera kuti tidya mochedwa.

Ndikamufunsa, amayankha kuti akukonza kapansi, tilemera chifukwa anzake ena apita patsogolo poimbira ndi kuvinira andale. Ndimusiye?

Dennis M,

Zomba.

 

Bambo Dennis,

Kuimbira andale kumayenera kutha kalekale. N’zomvetsa chisoni kuti amayi, asungwana komanso abambo ndi achinyamata ena akusiya ntchito zawo kukaimbira andale. Ili si vuto la amayi okha, mwaonapo inu achinyamata akudzipenta makaka a chipani.

Sindikudziwa kuti amapindula chiyani. Koma chomwe ndikudziwa uku n’kutaya nthawi.

Kungoganiza. Kodi andalewo angalole kuti ana awo akaswedwe maola ochuluka padzuwa kuimbira wandale amene si mbale wawo kuti apeze K1 000? Mwinanso ndachulutsa. K200?

Ayi ndithu, kupita patsogolo pandale poyambira kuimbira andalewo kuli ndi kena kobisika. Tidamvapo za amayi omwe ankamangitsa amuna awo chifukwa amalephera kuwagulira nsalu yachipani. Ali kuti lero? n

Related Articles

Back to top button