Chichewa

ANatchereza

Sakufuna kukaonekera

Gogo Natchereza,

Mnyamata wina adandifunsira chibwenzi ndi cholinga choti tidzakwatirane.

Padakali pano padutsa zaka zinayi tili paubwenzi, koma palibe chomwe amandiuza chokhudza ukwati. Mnzangayu amangofuna tizigonana basi.

Gogo ndithandizeni. Kodi ndimutaye mnyamatayu?

TTK

TTK,

Mutaye! Mnyamatayu zomwe akufuna n’zongogonana basi osati za banja.

Anyamata ambiri amabwatika atsikana powauza kuti adzawakwatira koma akudziwa kuti zaukwati ali nazo kutali.

Chakumtima kwawo chikaphwa, atsikana aja samawawerengeranso.

Nawo atsikana vuto lawo lalikulu n’kutengeka poganiza kuti akakana kugona nawo awasiya n’kukapeza ena.

Apatu ine ndikuona kuti mnyamatayu ndi kamberembere. Mutaye asakutaitse nthawi yako pachabe.

Gogo Natchereza

Bwenzi langa chimasomaso

Gogo Natchereza,

Ndidakumana ndi mtsikana wina mu mzinda wa Mzuzu zaka zitatu zapitazo, tidapatsana nambala za foni ndipo takhala tikuimbirana mpaka ubwenzi udayamba.

Mtsikanayu amagwira ntchito pa ku banki ina mu mzindawo moti ali ndi mnyumba yakeyake yomwe amakhala.

Gogo, mnzangayu ndamupezapo katatu konse ali pa chikondi ndi amuna osiyanasiyana, koma wakhala akundipempha kuti ndimukhululukire ndipo ine ndimakhululukadi.

Gogo, mtima wanga ndiwosweka chifukwa mnzangayu ndimamukonda kwambiri moti maganizo, moyo ndi mphamvu zanga zonse zidali pa iye.

Nditani, gogo? Chonde ndithandizeni!

HKA

HKA

Mtsikanayu ndi njinga simungapitirire kukhala naye paubwenzi.

Mutha kutero mwakufuna kwanu, koma mudzanong’oneza bondo mtsogolo muno chifukwa khalidwe la chimasomaso sindikuona akusiya.

Ngati akuchita ukathyali muli paubwenzi, zidzatha bwanji mukadzamukwatira?

Ndikudziwa kuti n’zopweteka kusiyana ndi wokondedwa wanu, koma limbani mtima.

Mukadekha, Mulungu adzakupatsani mtsikana wina wachikondi, komanso wokhulupirika, koma mtsikana uyu ndi moto. Adzakuotchani!

Gogo Natchereza

Related Articles

Back to top button