Chichewa

Anatchezera

Listen to this article

Sakundikwatira

Agogo,

Ndithandizeni. Ndili paubwenzi ndi mwamuna yemwe adakwatirapo koma banja lake lidatha ndi mkaziyo ndipo kuli mwana mmodzi. Inenso ndili ndi mwana mmodzi. Titatha chaka tili pachibwenzi adandiuza kuti andikwatira koma mpaka lero padutsa zaka 4 palibe chimene chkuchitika. Foninso adasiya kundiimbira, komanso pan chikondi chachepa. Nditani?

BH

 

Zikomo BH,

Mwamunayo si wachilungamo ndipo akungokunamiza, za banja alibe nazo ntchito. Ngati ukuti pano zaka 4 zatha chikuuzireni kuti akufuna akukwatire ndipo olo foni sakukuimbiranso, ufuniranji umboni wina woti alibe nawe chikondi? Usataye naye nthawi ameneyo, udzangodikirapo madzi a mphutsi apa. Palibe chako. Akadakhala kuti ali ndi chidwi nawe pano atakaonekera kwa makolo ako ndipo pano bwenzi tikukamba kuti muli pabanja.

 

Ndidalirebe?

Agogo,

Ndifunse nawo. Ine kwathu ndi ku Rumphi ndipo ndakhala ndili pachibwenzi ndi mnyamata wa ku Mzimba kwa zaka ziwiri tsopano. Sitinagonanepo ndipo tinagwirizana zotengana koma mpaka pano chaka chikuthanso. Ndikamufunsa akuti akonzeke kaye. Kodi ndipange bwanji? Ndidalirebe?

 

Zikomo pondilembera kuchoka ku Rumphiko. Funso lovuta kuyankha mwana wanga—kodi udalirebe? Inde ndikuti eee, usataye mtima poti kuona maso a nkhono n’kudekha. Ngati mnyamatayo akuti akonzeke kaye, mwina akunena chilungamo. Ndi anyamata ochepa amene amatha kukhala pachibwenzi ndi mtsikana kwa zaka ziwiri osagonana naye. Sindidziwa, paja amati mtima wa mnzako ndi tsidya lina, koma mmene ndikuonera fatsa, zoona zake zioneka zokha. Iwe ukuthamangira banja chifukwa chiyani? Mwamunayo ngwanzeru n’chifukwa chake akuti akonzekere kaye za ukwati, osangoti lero ndi lero basi tikwatirane uku alibe chilichonse. Ndikudziwa bwino lomwe kuti ku Mzimba ndi ku Rumphi miyambo yokhudza ukwati imafanana, mwamuna akafuna kukwatira amayenera kupereka malobolo, si choncho? Ndiye mwina akusakasaka kaye kuti akamatuma ‘thenga’ kwa asewere akhale ndi kenakake m’manja, osati kungopita chimanjamanja. Chachikulu n’choti simudagonanepo ndipo ngati ukuona kuti akukunamiza ukhoza kumusiya n’kupeza wina amene watsimikiza za ukwati. Nthawi zambiri atsikana ena zikawavuta, tiyese kuti mwatsoka achimwitsidwa ndi wina pamene ali pachibwenzi ndi winanso, amakakamira wachikondiyo kuti akwatirane msangamsanga n’cholinga choti azikati pathupi mpamwamunayo! Ndikhulupirira sizili chonchi ndi iwe.

 

Ofuna Mabanja

 

Ndine mayi wa mwana mmodzi ndipo ndikufuna mwamuna wodziwa mavuto, wachikondi, woopa Mulungu koma wopanda banja. – 0884 437 604

 

Ndili ndi zaka 23 ndipo ndifuna mwamuna woti ndimange naye banja. Akhale woti akufunadi banja osati zoyesana ayi. Wofuna aimbe pa:

0992 673 004

 

Ndine mayi wa ana awiri ndipo ndifuna mwamuna womanga naye banja. Akhale wachilungamo komanso woopa Mulungu.0992 728 276

Related Articles

Back to top button
Translate »