Chichewa

Anatchezera

Listen to this article

Sabata zingapo zapitazi, takhala tikulengeza kuti patsamba lino tizikupatsirani Anatchereza ndi malangizo pamavuto amene mumakumana nawo. Mavutowa akhoza kukhala a m’banja, maphunziro, chipembedzo komanso momwe mumakhalira ndi ena. Anzanu ayamba kale kutitumizira madandaulo awo ndi awa ali mmunsimu.

Anatchereza

Ndili ndi zaka 20 ndipo amuna anga sagona m’numba ndiye chonde, ndithandizeni. Akuti ndikawauza ankhonswe banja langa litha. Ukwati tapanga August wapiyu.

Ndine A

 

Zikomo A,

Mwamuna wakoyo ngwachibwana cha mchombolende! Mwangokwatirana kumene ndipo ukuti sagona m’nyumba, ndiye amakagona kuti? Ukapanda kusamala naye ameneyo akubweretsera m’mavuto aakulu—ndikunenatu matenda oopsa, kuphatikizapo HIV/Edzi. Ngati wayamba kale kunena kuti ukakanena kwa ankhoswe banja lithapo ndiye kuti iye za banja alibe nazi ntchito koma kusangalatsa chilakolako cha thupi lake basi. Ndiye usazengerezepo apa, pita kaitule nkhaniyi kwa ankhoswe. Ngati akufuna kuti banjali lithe, lithe basi. Mwamuna wachimasomaso ndi woopsa kwambiri ndipo safunika kumusekerera.

 

Anatchereza,

Mwamuna wanga anandisiya ndili ndi mimba palendi. Ndikaimba foni amayankha ndi mkazi amene akufuna kukwatirana naye. Ndipange bwanji pamenepa?

Choyamba, kuti mwamunayo azichoka pakhomo n’kukusiyani palendi, chidachitika n’chiyani? Eetu, amati umanena chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga! Mukamafuna kuti tikuthandizeni, nkhani yanu muziiyala bwinobwino kuti tidziwe gwero la mavuto anu. Koma kungokalakala pamwamba, munena kuti agogo sanandithandize. Poti ine ndikusowa poyambira kuti ndikuthandizeni, ndingonena kuti pitani kwa ankhoswe anu mukawafotokozere zomwe amuna anu achita, mwina atha kukuthandizani. Komanso njira ina ndi yopita kukadandaula kubwalo la milandu kuti mwamuna wanu ngati akufuna kukwatira mkazi wina akusudzuleni mwadongosolo, nanga ukwati umatha choncho? Akapezeka kuti mwamunayo ngolakwa, akhoti amatha kumulamula kuti mwana akadzabadwa azidzamupatsa chithandizo chakutichakuti kufikira atakula. Tayesani njira ziwirizi, mwina mutha kuthandizika pa vuto lanu.

 

Anatchereza,

Zikomo ngati muli bwino. Ine dzina langa ndine Anthony P Nyirongo, ndavutika transport ndiye ndinasiya foni pababa shopu kuonjezera moto ndiye ndinawerenga nyuzi ya pa 27 September ndiye ndinawerenga pena pake kuti amene ali ndi vuto angathe kulemba text pa nambala yanu. Thanks.

 

A Nyirongo,

Chonde tamakulani. Vuto lanu ndi chiyani? Munaiwala foni pababa shopu ndipo mukuti mulibe transport, ndiye nkhalamba ngati ine mukuti nditani? Zinazi abale! Muli bwinobwino koma?

 

Ofuna Mabanja

Ndine mnyamata wa zaka 25, ndikufuna mkazi woti ndimange naye banja koma asakhale wa zaka zoposera 30. Wondifuna aimbe pa 0881 123 064

 

Ndine mnyamata wa zaka 21 ndipo ndikufuna mkazi wamankhalidwe abwino, woopa Mulungu, komanso wachikondi. Tithe kulumikizana pa 0884 442 417/0881 466 378

 

Ndine mwamuna wa zaka 36 ndipo ndimakhala ku Lilongwe. Ndikufuna mkazi wa zaka pakati pa 27-40 woti ndimange naye banja. Akhale wa mwana mmodzi kapena awiri, wachuma chake komanso akhale wa ku Lilongwe konkuno. Amene akufuna aimbe pa 0883 705 299

 

Ndili ndi zaka 36, ndikufuna mwamuna wa zaka za pakati pa 40 ndi 50. Aimbe pa 0885 221 111

Related Articles

Back to top button