Tuesday, March 2, 2021
  • About Us
  • ImagiNATION
  • Adverts
  • Rate Card
  • Contact Us
The Nation Online
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Opinion
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Opinion
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
No Result
View All Result
Home Chichewa

anatchezera

by ANATCHEZERA
08/11/2015
in Chichewa
3 min read
0
Share on FacebookShare on TwitterShare on WhatsAppShare on LinkedinLinkedinShare via Email

 

Akunyengana ndi mnzanga

RelatedHeadlines

Mtsutso pa zoika a Covid-19

Amwalira atathawa m’chipatala

‘Osakondera odya nawo K6.2 biliyoni’

Zikomo Anatchereza,

Ndakhala pabanja zaka 7 ndipo tilinso ndi mwana wa zaka 7. Tsiku lina mwanayo adathyoka mkono ndipo adatigoneka kuchipatala sabata ziwiri ndi masiku 4.

Ndili konko, ndidamva kuti mwamuna wanga akuyenda ndi mnzanga, yemwenso ndi woyandikana naye nyumba. Titatuluka adabwera kudzandiuza kuti mwamuna wanga adamufunsira koma adawakana.

Nditawafunsa amuna anga adakana. Chodabwitsa nchakuti, usiku mwamuna wanga amasowa. Kuyang’ana kuchimbudzi, kubafa ngakhalenso pakhonde osaoneka.

Ntawapanikiza, adaulula kuti amayendadi ndi mnzangayo. Powafunsa ngati ndili ndi vuto adati palibe, koma Satana ndiye adawanyenga. Ndichitenji?

EKM

EKM,

Amuna anuwo alibee chikondi chenicheni. Iwowo povomereza kuti amanyengana ndi mnzanu, aonetseratu ukamberembere wawo. Poyamba ndi kukana ndiye kusowa chikondiko.

Chokaikitsa china nchakuti mnzanuyo adabwera yekha kudzakuuzani kuti amuna anu adamufunsira koma adanama kuti adawakana. Ichi chidali chiphimba m’maso chabe chifukwa amadziwa kuti manong’onong’o a uhule wake akufikani.

Zikatere nkutani? Kunjaku kudaopsa ndipo si bwino kusekerera mwamuna kapena mkazi wosakhulupirika. Nthawi yoimbs nyimbo ya kapirire kunka iweko idatha.

Kaitureni nkhaniyi kwa ankhoswe chifukwa uwu ndi mlandu wachigololo choletsedwa ndi Ambuye.

 

Apachibale akundifuna

Anatchereza,

Pali anyamata awiri a pachibale amene akuoneka kuti amandifuna. Mmodzi mwa anyamatawo ndidamudziwa kalekale ndipo wakhala akundifundira koma ndimamukana.

Ndidadziwana ndi winayo chifukwa cha mbale wakeyo ndipo nsye akunditumizira mauthenga a chikondi, ati akundifuna. Ndichitenji, chifukwatu awiriwo akundisowetsa mtendere.

M.E.

Mponela

ME,

Ngati anyamatawo simukuwafunadi ndi bwino kuwauziratu, mmalo mowapatsa banga kuti aziganiza kuti mwayi ukadalipo.

Mwinatu inuyo simutsindika kukana kwanuko. Komanso nkutheka kuti anyamatawo ndi nkhakamira. Mwinanso ali pampikisano kuti aone angakutengeni ndani.

Muli monsemo, mphamvu zili m’manja mwanu, kulola kapena kukana.

 

Ana owapeza avuta

Zikomo Anatchereza,

Ndakhala pachibwenzi ndi mkazi wina yemwe ndidalowa naye m’banja chaka chatha. Iye adabwera ndi ana ake awiri ndi abale ena ndipo polingalira kuti ndi banja, nanenso ndidakatenga mwana wanga.

Iye akungokhalira kulalatira mwana wangayo ati ndi wamwano. Nthawi zina akumachita izi panja kuti a nyumba zoyandikira amve. Akuti ngakhale nditachoka sangadandaule, chonsecho ali ndi pathupi pa miyezi 7.

Ndapirira mokwanira, ndithandizeni.

WL,

Lilongwe.

WL,

Musanachite chilichonse pabanja mumayenera kukambirana kaye. Momwe zikuonekera apa, mkazi wanuyo adakangotenga ana ndi abale akewo musanakambirane. Nanunso mudangoyendera yanu nkukatenga mwana wanu.

Choncho kusamvana sikungalephere kubwerapo.

Komatu apa palibe chifukwa chokwanira choti nkuthetsera banja.

Khalani pansi nkumanga mfundo imodzi. Ndi ana ndi abale ati amene ayenera kuchoka pakhomopo ndipo ndi angati amene ayenera kuchoka?

Mukuyembekezera mwana wanu, kusonyeza kuti udindo wanu ukukula.

 

Anatchereza

Ndimutsatirebe?

Ine ndidakwatiwa ndi mwamuna wa ku Zimbabwe ndipo takhala limodzi mpaka mu 2012 pomwe adachoka kupita ku Joni. Ndili naye mwana mmodzi. Poyamba ankatumiza chithandizo ndipo timaimbirana foni koma pano olo foni saimba, chithandizonso adasiya kutumiza. Koma adandipangitsira pasipoti kuti ndimtsatire ku Joniko koma abale ake adayankhula mwathamo kuti adakwatira ku Joni komweko. Ndiye nditani pamenepa, ndikwatibwe kapena ndizidikirabe? Nditani ine, gogo wanga, poti ndidakali wachitsikana?

EE,

Blantyre

 

Wokondeka EE,

Ndamva nkhawa zako ndipo ndakhudzidwa kwabasi ndi mmene ukwati wako ndi mwamuna wa ku Zimbabweyo ukuyendera. Koma nanenso ndili ndi funso kuti ndithe kukuthandiza bwino. Kodi ukwati wanuwo ndi womanga bwinobwino ndipo ndi wovomerezeka ndi mbali zonse ziwiri za kuchimuna ndi kuchikazi? Ndatero chifukwa pakuoneka kuti ukwati wanu ulibe ankhoswe n’chifukwa chake abale ake a mwamunayo akukuyankha mwathamo kuti uiwaleko za iye ati chifukwa adakwatira mkazi wina ku Joniko. Maukwati ambiri akhala asakulongosoka chifukwa achinyamata masiku ano amakonda madulira, osafuna kutsata ndondomeko zonse zofunikira asanalowe m’banja. Mnyamata akangoti ‘I love you’ basi msungwana khosi gonekere kenaka wakamulowerera m’nyumba ali basi takwatirana. Posakhalitsa mavuto otere amayamba m’banja lotereli, zinthu osalongosokanso. Tsono apa, mwana wanga, chimene ndikuona n’chakuti mwamuna wakoyo walithawa banja n’chifukwa chake chithandizo olo foni adasiya kukutumizira. Iwe ukamuimbira amakuyankha nanga? Ndikukaika. Likadakhala banja lenileni ndidakati upite kwa ankhoswe akuthandize, koma ndakaika ngati alipo. Ndiye chomwe ungachite apa n’mumuiwala mwamunayo ndi kuyambiranso wani. Si wanena wekha kuti udakali mtsikana! Koma ulendo uno uyesetse kuti utsate ndondomeko zonse zimene zimayenera kutsatidwa munthu ukafuna kulowa m’banja—iwe ndi bwenzi lako mudziwane bwinobwino ndipo lidzaonekere kwanu ndi akwawo kudzatomera ukwati; pakhale chinkhoswe cholongosoka; kenaka ukwati wololedwa. 

Previous Post

Govt cancels 15 suppliers contracts in Malata Subsidy Programme

Next Post

Vitamin K dispenser caught out

Related Posts

covid death | The Nation Online
Nkhani

Mtsutso pa zoika a Covid-19

February 28, 2021
death e1465557792659 | The Nation Online
Chichewa

Amwalira atathawa m’chipatala

February 28, 2021
HRDC pursuing this matter further: Trapence
Nkhani

‘Osakondera odya nawo K6.2 biliyoni’

February 27, 2021
Next Post

Vitamin K dispenser caught out

Opinions and Columns

My Turn

Tackling global slowdowns

March 1, 2021
People’s Tribunal

Burglary at the hill

February 28, 2021
Search Within

Perseverance landed, is alive and well

February 28, 2021
Emily Mkamanga

Tasting your own salt in politics

February 28, 2021

Trending Stories

  • Olela: We are excited

    K5bn Sunbird Waterfront hotel opens May

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Inside Chisale’s seized property

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Exclusive: RBM’s Mzuzu branch payment mess exposed

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Lhomwe chiefs divided on paramount chief

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Experts fault IFMIS roll-out delays

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Values
  • Our Philosophy
  • Editorial policy
  • Advertising Policy
  • Code of Conduct
  • Plagiarism disclaimer
  • Disclaimer
  • Privacy Policy
  • Terms of use

© 2021 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Opinion
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation

© 2020 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

This website uses cookies. By continuing to use this website you are giving consent to cookies being used. Visit our Privacy and Cookie Policy.