Chichewa

Anatchezera

Listen to this article

Sakuthandiza mwana
Agogo,
Ndine mtsikana wa zaka 19 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Ndidali pabanja koma litatha bambowo samatumiza chithandizo olo sopo. Ndiye nditani poti mwanayu ndimavutika naye ndekha?

Pepa mtsikana,
Ndi zimene ndakhala ndikulangiza atsikana nthawi zonse kuti limbikirani sukulu mudakali anthete, osati kuthamangira kukwatiwa! Tikamanena kuti si bwino kuthamangira banja timadziwa kuti nthawi zambiri zotsatira zake zimakhala ngati zimene wakumana nazo iwezi. Tsono nkovuta kukuthandiza zenizeni chifukwa sukulongosola kuti ukwati wanu udali wotani-wongolowana, wachinkhoswe kapena mudadalitsa kutchalitchi?  Nanga zifukwa zomwe banja lako lidathera n’zotani? Ukwatiwo udathera kuti-kukhoti kapena basi mwamuna adangoti zipita kwanu? Ngati ukwati wanu udali ndi ankhoswe, iwo akutipo chiyani pa kutha kwa ukwati wanu? Banja lenileni silimangotha lero ndi lero popanda zifukwa zenizeni; banja si masanje. Ndiye mmene zikuonekera inu mudangotenganapo popanda ndondomeko yeniyeni ndipo mwamuna adalola zokukwatira pothawa milandu atakupatsa pathupi, si choncho? Ndiye poti amati madzi akatayika saoleka, chomwe ungachite n’choti nkhaniyi upite nayo kwa ankhoswe kapena kubwalo la milandu kuti akakuthandize chifukwa bamboo wa mwana ali ndi udindo woti azithandiza mwana wake ngakhale kuti banja lanu latha. Mwana asavutike chifukwa cha kusemphana Chichewa kwa inu makolo. Kodi, sukulu udalekeza mukalasi yanji? Chonde, ngati pali mwayi woti n’kubwerera kusukulu, chita zomwezo chifukwa udakali mwana wamng’ono.

Ndikhulupirire?
Anatchereza,
Ndidali ndi chibwenzi chomwe tinkakondana kwambiri ndipo tinkamvanadi koma titakhala zaka ziwiri osaonana kaamba ka zovuta zina popeza aliyense ankakhala ndi makolo ake. Koma panopa adakwatiwa ndipo ali ndi mwana mmodzi. Titakumana miyezi yammbuyomu adandiuza kuti amandikondabe. Kodi ndikhulupirire? Kapena ndipange bwanji? Ndithandizeni Anathereza.
Godfrey Richard Sindima,
Thyolo

Okondeka a Sindima,
Tisatayepo nthawi apa. Si mwati adakwatiwa ameneyo ndipo ali ndi mwana mmodzi? Ameneyo si wanunso ayi, ndi mwini wake! Akadakhala kuti amakukondani akadakudikirani, osati kukwatiwa ndi munthu wina, ayi. Kodi mukundiuza kuti kuti kumene adakwatiwako adachita kumukakamiza? Padali chikondi pakati pa mwamunayo ndi mkazi yemwe mukuti adali chibwenzi chanuyo. Tsono inu musapusitsidwe kuti akukukondanibe pamene ali pabanja ndi mwamuna wina. Apa ndiye kuti dzanja silidalembe kuti iye adzakhala nthiti yanu. Funani wina, achimwene, ameneyo ngodanitsa. Mkazi wapabanja amene amadyeranso maso amuna ena timati ndi wachimasomaso ameneyo ndipo si wofunika kutaya naye nthawi. Ndikhulupirira mwamvetsa.

Amamumenya
Zikomo Anatchereza,
Ineyo ndili ndi chibwenzi ndipo timakondana kwambiri koma makolo ake amamumenya chifukwa cha ine. Ndiyeno ndikamuuza kuti chithe amakana, koma ineyo ndimaopa kuti adzamuvulaza. Nditani pamenepa? Ndimusiye?

Pati bii pali munga! Makolo anzeru sangamamenye mwana wawo wamkazi popanda chifukwa. Zimene ukunena kuti amamumenya chifukwa ali m’chikondi ndi iwe si zoona ayi, koma chilipo chifukwa chomwe amamumenyera. Mwina mwana wawoyo adakali pasukulu ndipo sakufuna kuti asokoneze maphunziro chifukwa chochita zibwenzi ali pasukulu; mwina n’kutheka sakuvomereza chibwenzi chanu kaamba ka zifukwa zina ndi zina. Vuto ndi loti sukufotokoza bwinobwino za cholinga cha chibwenzi chanucho, msinkhu wako ndi zina zotero. Ngati chibwenzi chanucho cholinga chake n’choti mudzakhale pabanja, iwe wachitapo chiyani kuonetsa kuti si zachibwana ayi? Iwe udamaliza sukulu ndipo uli pantchito kapena ayi? Pali chitomero kapena ayi? Mwina utandiyankha mafunso amenewa ndingathe kuona kuti ndikuthandize bwanji.

Ofuna Mabanja

Ndine mkazi wa zaka 24 ndipo ndikufuna mwamuna womanga naye banja koma akhale Msilamu. Ndili ndi ana awiri.-0993 519 866

Ndikufuna mkazi wasiriyasi, wamakhalidwe abwino.-0993 173 365
Ndine mwamuna wa zaka 25 ndipo ndikufuna mkazi woti ndikhale naye pachibwenzi koma mapeto ake ndi banja.-0881 309 199
Ine ndikufuna mkazi womanga naye banja koma akhale kuti adayezetsapo magazi ndipo adapezeka ndi kachilombo ka HIV. Wasiriyasi aimbe pa nambala iyi: 0999 522 460 n

Related Articles

Back to top button