Chichewa

Anatchezera

Listen to this article

 

Akumandiipitsa

Zikomo agogo,

Ndili ndi chibwenzi ndipo makolo akudziwa ngakhale kuti ndi mwamphekesera chabe. Nthawi ina bambo ake (osati omubereka) amafuna kumugwiririra ndiye akumandiipitsa dzina kwa mayi ake, koma iwo sakutekeseka ndi izi. Ndili ndi mantha, nditani pamenepa agogo?

Ine GK, Lilongwe.

 

GK,

Wati uli ndi mantha, mantha ake otani? Sindikuonapo chifukwa choti uzikhala ndi mantha pamene sudalakwire munthu aliyense. Ndiye iwe ukuchita mantha ndi ndani? Ngatidi ukunena zoona kuti bambo omupeza a mtsikanayo adafunadi kumugwiririra, bwenzi lakolo adachitapo chiyani zitachitika zimenezo? Kodi mayi a mtsikanayo nkhaniyi akuidziwa? Ngati akuidziwa adachitapo chiyani? Ndikufunsa mafunso onsewa chifukwa ndi mlandu waukulu kugwiririra kapena kufuna kugwiririra ndipo munthu wopalamula mlandu wotere amayenera kulangidwa kundende malinga ndi malamulo a dziko lino. Munthu wotere ngosafuna kumusekerera. Ndibwerere kunkhani yako yoti uli ndi mantha. Ngati umamukonda zoona mtsikanayo pitiriza kutero chifukwa tsiku lina udzakhala mpulumutsi wake kwa bambo womupezayo mukadzakhala thupi limodzi. Mwina mayi ake sakutekeseka ndi zokuipitsira dzina lako chifukwa akudziwa choona chenicheni, maka pankhani yoti amuna awo amafuna kugwiririra mwana wawo, koma akukhala chete chifukwa akuopa kuti angawasiye banja.

 

Akuti tibwererane

Gogo wanga,

Ndinali pachibwenzi ndi mtsikana wina kwa miyezi isanu ndi umodzi. Pamene timati tipange ukwati mwezi wotsatira iyeyo adathetsa chibwenzi ndi kutengana ndi wina. Patatha miyezi iwiri adabwera ndi kudzandipepesa ati tibwererane koma akwathu akukana. Kodi nditani pamenepa?

NF, Dedza.

 

NF,

Mvera malangizo a makolo ako kapena akwanu amene akuti usayerekeze kubwererana naye chifukwa zimene akukulangizazo ndi zoona. Mawu a akulu amakoma akagonera, ukanyalanyaza udzalirira kuutsi tsiku lina. Iye adathetsa chibwenzi pakati pa iwe ndi iye ndipo adakwatiwa ndi wina kenaka patha miyezi iwiri uyo akubwera poyera ali ‘undikhululukire, tibwererane’. Alibe manyazi! Chavuta komwe adakakwatiwako ndi chiyani? Chilipochilipo. Ndiye iwe ukavomereza zoti mubwererane udzaoneka wombwambwana; wodya masanzi.

 

Ndimukhulupirire?

Agogo,

Ndili pachibwenzi ndi mnyamata wina wake. Ndakhala naye zaka zinayi. Chaka chino adakaonekera kwathu koma ineyo akundikaniza kuti ndikaonekere kwawo. Ndikamufunsa kuti akundikaniza chifukwa chiyani sayankha zogwira mtima koma ndikamufunsa za ukwati amavomera ndi mtima wake wonse. Ndimukhulupirire?

Ine Fannie, Blantyre.

Fannie,

Zikomo kwambiri pondilembera. Funso lako ndalimva ndipo ndiyesetsa kuti ndikuthandize m’maganizo. Wati mnyamatayo adakaonekera kwanu chaka chino kutanthauza kuti walimba mtima za ukwati. Poti miyambo kusiyana, kodi kwanu mtsikana amakaonekeranso kwa makolo a mwamuna? Kwa ine izi n’zachilendo chifukwa kwathu kulibe zotere; mwamuna ndiye amakonekera kwawo kwa mkazi osati mtsikana. Ndiye ngati kwanu kuli mwambo woti mtsikana naye amakaonekera kwawo kwa mwamuna ndipo iye akukuletsa, ndiye kuti chilipo chomwe akubisa, mwina n’kutheka kuti ali ndi mkazi kale ndipo akuopa kuti umutulukira. Koma ngati mwambo umenewo kulibe, palibe chifukwa choti iwe ukaonekere kwawo pokhapokha makolo a mnyamatayo atakhala ndi chidwi choti adzakuone.

Related Articles

Back to top button