Chichewa

Anatchezera

Listen to this article

Sakuyankhanso foni

Zikomo,

Ndine mtsikana wa zaka 19 ndipo ndidapeza bwenzi langa mu 2012. Poyamba ankalimbikira kuti andikwatire chaka chomwecho koma ndidakana. Kuyambira mu 2014 mpaka 2015 nkhani yake idali yomweyo kuti andikwatire koma ndidamuuza kuti andidikire ndingomaliza kaye sukulu. Koma kuchoka nthawi yomweyo adasiya kundiimbira foni ndipo ineyo ndikati ndimuimbire sayankhanso. Sindikudziwanso ngati ubwenzi wathu ukupitirirabe ndiye mundithandize pamenepa kuti nditani popeza ndinali naye yekhayo.

FR, Zomba.

FR,

Zikomo, mwana wanga, pondilembere. Atsikana a maganizo ngako akowo okonda sukulu ndi ochepa masiku ano; ambiri akangofunsiridwa basi womwewo kukalowa m’banja. Iwe usadandaule kwambiri za chibwenzicho kuti kaya chatha kaya chilipo, koma ingolimbikira sukulu. Ndanena izi chifukwa ngati ukunena zoona kuti atangokufunsira mnyamatayo mu 2012 basi maganizo ake adali poti mukwatirane nthawi yomweyo, osaganizira za tsogolo lako pa nkhani ya maphunziro. Akadakhala mwamuna wachikondi chochokera pansi pa mtima akadamvetsa kuti maphunziro ndi ofunika kwambiri pamoyo wa munthu aliyense wofuna tsogolo lowala. Kuthamangira kukwatira kapena kukwatiwa si chanzeru; palibe phindu kukhala mbuli pamene uli ndi mwawi wa maphunziro. Ndiye ngati mnyamatayo wasiya kuyankha kapena kukuimbira foni, ndi mwayi wako umenewo kuti uike mtima wako wonse pamaphunziro mpaka umalize kenaka mpamene uziganiza za ntchito kapena banja poti maphunziro ndi zibwenzi nthawi zambiri siziyendera limodzi—china chimasokonekera basi. Waonetsa kukhulupirika pokhala ndi bwenzi mmodzi yekhayo ndiye sindikukaika kuti udzatha kupeza mwamuna wokhulupirika womanga naye banja mtsogolomu ukapitiriza ndi mtima umenewo wopanda chimasomaso.

 

Umandiwaza

Anatche,

Gogo wanga ndiwe wanzeru ndipo umandizawaza. Ndidawerenga Msangulutso wa pa 7 February 2016 ndipo nkhani idandigwira mtima ndi yomalizayi yoti mwamuna anakaonekera kwawo kwa mkazi ndipo mkazi naye ati akufunanso kuti akaonekere kwawo kwa mwamuna. Nane mavuto amenewa ndili nawo ati mkazi akaonekere kaye kwathu kenaka ndipite kwawo ati kuti makolo anga akhale ndi chidwi choti adzamuone. Ndiye takhala tikulimbana ndiye pano ndinangozisiya chifukwa [zopanda pake] ndimadana nazo ngati kubanjako ndizikalandira salale…

PS, Blantyre.

 

Hahahahaa! A PS ndinu woseketsa! Ayi, zikomo chifukwa cha maganizo anu, koma ndangoti tikumbutsane kuti nkhani za chikondi nzovuta ndipo zimafuna kufatsa nazo, kupirira ndi kumvetsetsana. Inu simunafumulire kungozisiya? Ndikhulupirira simunathetse chibwenzi ndi wokondeka wanu chifukwa cha nkhani yoti akufuna akaonekere kwanu kuti makolo anu akamuone komanso kuti akamudziwe. Kwa ena izi zilibe vuto malingana ndi kusiyana miyambo ndi zikhalidwe, koma kwa ena zoti mkazi naye akaonekere kwa makolo a mwamuna nzachilendo ndithu! Koma zonse zimatha n’kukambirana basi.

Akuti tibwererane

Gogo wanga,

Ndidali paubwenzi ndi mnyamata wina kwa chaka chimodzi koma anathetsa chibwenzicho popanda chifukwa. Ine ndinapezana ndi wina amene timagwirizana kwambiri. Pano wakale uja akuti tibwererane. Kunena zoona wakale uja ndimamukondabe mpaka lero. Ndithandizeni, nditani pamenepa?

Cyndie, Blantyre.

 

Zikomo Cyndie,

Kodi sudamvepo zoti mapanga awiri avumbwitsa? Kusankha usankha wekha poti wanena wekha kuti wakaleyo umamukondabe komanso watsopanoyo umagwirizana naye kwambiri! Sindidziwa ngati amene ukugwirizana naye kwambiriyo umamukondanso—chifukwatu kugwirizana ndi kukondana ndi zinthu zosiyana. Langizo langa ndi loti amene umamukonda adaonetsa kale mawanga ake oti chikondi chake kwa iwe ndi chochepa chifukwa adathetsapo chibwenzi “popanda chifukwa” pamene watsopanoyu amene wati umagwirizana naye kwambiri sadakulakwirepo. Ndiye pali chifukwa chanji chomusiyira n’kubwererana ndi munthu woti adakuchitapo chipongwe? Uyu watsopanoyu ngati sadakulakwirepo kapena kukukhumudwitsa, iwenso osamukhumudwitsa chifukwa mapeto ake olo mizimu idzakuseka. Koma chisankho chili ndi iwe mwini. n

Related Articles

Back to top button