Chichewa

Anatchezera

Sagona m’nyumba

Anatchereza,

Ndili ndi zaka 20 ndipo amuna anga sagona m’nyumba ndiye chonde, ndithandizeni. Akuti ndikawauza ankhonswe banja langa litha. Ukwati tapanga chaka chatha.

Ndine A

Blantyre

 

Zikomo A,

Mwamuna wakoyo ngwachibwana zedi! Mwangokwatirana kumene ndipo ukuti sagona m’nyumba, ndiye amakagona kuti? Ukapanda kusamala naye ameneyo akugwetsa m’mavuto aakulu-ndikunenatu matenda oopsa, kuphatikizapo HIV/Edzi. Ngati wayamba kale kunena kuti ukakanena kwa ankhoswe banja lithapo ndiye kuti iye za banja alibe nazo ntchito koma kusangalatsa chilakolako cha thupi lake basi. Ndiye usazengerezepo apa, pita kaitule nkhaniyi kwa ankhoswe, umve zimene anene. Ngati akufuna kuti banjali lithe, lithe basi. Mwamuna wachimasomaso ndi woopsa kwambiri ndipo safunika kumusekerera.

Adandisiya palendi

Anatchereza,

Mwamuna wanga anandisiya ndili ndi mimba palendi. Ndikaimba foni amayankha ndi mkazi amene akuti akufuna kukwatirana naye. Ndipange bwanji pamenepa?

NK,

Balaka

 

Zikomo NK,

Kuti mwamunayo azichoka pakhomo n’kukusiyani palendi, chidachitika n’chiyani? Eetu, amati umanena chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga! Mukamafuna kuti tikuthandizeni, nkhani zanu muziziyala bwinobwino kuti tidziwe gwero la mavuto anu. Koma kungokalakala pamwamba, munena kuti agogo sanandithandize. Poti ine ndikusowa poyambira kuti ndikuthandizeni, ndingonena kuti pitani kwa ankhoswe anu mukawafotokozere zomwe amuna anu achita, mwina atha kukuthandizani. Komanso njira ina ndi yopita kukadandaula kubwalo la milandu kuti mwamuna wanu ngati akufuna kukwatira mkazi wina akusudzuleni mwadongosolo. Nanga ukwati umatha choncho? Akapezeka kuti mwamunayo ngolakwa, akhoti amatha kumulamula kuti mwana akadzabadwa azidzamupatsa chisamaliro chakutichakuti kufikira atakula. Tayesani njira ziwirizi, mwina mutha kuthandizika pa vuto lanu.n

Related Articles

Back to top button