Chichewa

Anatchezera

Listen to this article

Ndisathandize mwana wanga?

Anatchereza

Ine ndi mkazi wanga tidalekana titakhala pabanja zaka ziwiri. Mkaziyu ndidakukwatira titachimwitsana pasukulu ine ndili Fomu 4 pamene iye adali Fomu 2. Ndidali kuchikamwini. Koma zinthu m’banja zidasintha mosadziwika bwino. Mkazi wanga adayamba makani ndipo ndikamabwera kuchokera kuntchito ndimapeza nsima yosaphika, madzi osamba palibe ndipo izi zitachitika kwa sabata mpamene ndidakawatulira nkhaniyi achimwene ake monga ankhoswe a banja lathu koma padalibe chosintha. Chidatsitsa dzaye ndi ichi: ndidamuuza kuti ngati sanena chimene chikupangitsa kuti azichita mwano sagona m’nyumbamo ndipo adatulikadi kukawauza achimwene ake. Atabwera achiwene akewo adangofikira kunena kuti “ndatopa nawe, uzipita kwanu, siwenso mkamwini pano. Akakhala mchemwaliyu ndimpezera mwamuna, amukwatira”. Ndipo adakatenga makiyi kudzakhoma nyumba yanga nthawi ili cham’ma 11 koloko usiku, mkazi wanga akungoyang’ana osanenapo kanthu. Ndinanyamuka usiku womwewo ulendo wa kwathu ku Nkhula. ndipo mpaka pano palibe kulumikizana. Ndikati ndikamuone mwana wanga wa zaka ziwiri, Prince, mayi a mkazi wangayo amati adapita ndi mayi ake ku Zomba kwa malume ake koma nditafufuza ndidamvetsedwa kuti mkaziyo adayambanso sukulu yogonera konko papasekondale ya Namikase ku Mdeka komwe akubwereza Fomu 2. Ndiye nditani pamenepa? Kodi banja likatha ndiye kutinso mwana wako usamuthandize? Nanga kutula nkhani kwa ankhoswe n’kulakwa? Chonde ndithandizeni. 

BM

Blantyre

 

Okondeka BM,

Choyamba ndikuthokozeni chifukwa choyala nkhani yanuyi bwinobwino kuti ndiimvetsetse ncholinga choti ndikuthandizeni. Ndi mmene mwafotokozeramu zikuoneka kuti ankhoswe a banja lanu sadakuthandizeni chifukwa mmalo molimbikitsa banja lanu iwo ndi amene adali patsogolo kulithetsa. Koma banja lenileni silimatha monga banja lanu lidathera; lanu lidatha mwachibwana zedi, kusonyeza kuti ndondomeko zoyenera zokhudza mmene banja limayambira kapena kutha sizidatsatidwe. Choyamba ndikuona kuti banja lanu lidali lokakamiza chifukwa mudachita kuchimwitsana muli pasukulu ndipo pano mwana wakula. Apa nchachidziwikire kuti makolo a mkazi wanu, achimwene ake omwe mukuti ndi ankhonswe a banja lanu, komanso mkazi wanu iye mwini akufuna kuti apitirize sukulu. Uku, mmene ndikuonera, sikulakwa, komabe adayenera kuzindikira kuti kuthetsa banja la zaka ziwiri mwanjira yotere ndi kulakwa. Masiku ano kuli mwawi woti mayi atha kupitiriza sukulu kuchokera kubanja, bola kugwirizana ndi mwamuna wake. Zimatheka ndithu. Padalibe chifukwa choyambira kuchita mwano kapena kuonetsa mkhalidwe woipa ngati mkazi wanu amafuna sukulu, koma kukhala pansi ndi kukambirana za tsogolo lanu ngati banja. Mkaziyo akadatha kukuuzani za maganizo ake ofuna kupitiriza sukulu ndipo ndikhulupirira mukadatha kugwirizana kuti muchita bwanji, osati mmene zidakhaliramo. Mwachidule, pofuna kukuthandizani chochita, ndikuti ngati mumamukondabe mkazi wanu, muwauze ankhose onse-akuchikazi ndi akuchimuna-za cholinga chanu ndipo ngati ali anzeru akhala pansi n’kukambirana kuti banja lanu, ngati lidalidi lovomerezeka, lipitirirebe ngakhale mkazi wanu ali kusukulu. Mwana wanu, Prince, asavutike inu mulipo, muthandizeni ndithu m’njira iliyonse chifukwa ndi wanu basi, osati wa wina ayi.

Adanditukwana pagulu

Anatchereza,

Mwamuna wanga adachichotsa ulemu ponditukwana za munsalu atandipeza ndikupatsana moni ndi mwamuna wa mnzanga amene ndimakonda kucheza naye. Koma sanasiyire pomwepo, kunyumba adakandimenya ati ndimakonda amuna. Nditani?

NM,

Blantyre

 

NM,

Nkhani yochititsadi manyazi imeneyi. Izi ndiye timati nkhanza kwa amayi. Mwamuna waulemu ndiponso wachikondi sachita zimene mwamuna wanu adachitazo. Ankhoswe anu akuzidziwa zimenezi? Ndi bwino mukhale pansi ndi ankhoswe anuwo kuti amudzudzule mwamuna wanuyo kuti asinthe khalidwe lotukwana ndi kumenya mkazi zinthu zisanafike posauzana. Banja lotere ndi losautsa. n

Related Articles

Back to top button