Chichewa

Anatchezera

Listen to this article

Akundimana

Anatchereza,

Ndakhala pabanja ndi mkazi wanga kuyambira mu 2011. Poyamba zonse zimayenda koma masiku ano ndikamufuna masiku ambiri amanena kuti watopa kapena akudwala.

Ndithu mpaka kumaliza mkonono wabodza. Ndikuganiza kuti ali ndi chibwenzi. Nditani?

PB,

Phalombe.

 

PB,

Malembo Oyera amaneneratu kuipa kokanizana. Malangizo ambiri a mipingo ina komanso a chikhalidwe amakhala a kuipa kokanizana ngati anthu alowa m’banja. Koma nkhani imeneyi kuthana nayo kwake ndi inu anthu awiri chifukwa zochitika kuchipinda zimathera komweko moti ngakhale ankhoswe sayenera kumalowerera pokhapokha zitafika povutitsitsa. Choncho, muyenera kukambirana pauwiri wanu kuti muone chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga.

 

Ali kale pabanja

Zikomo gogo,

Ndili ndi zaka 25 ndipo ndakhala pachibwenzi ndi bambo wina kwa zaka zitatu. Mnzangayo ali pabanja koma amandilipirira lendi nyumba imene ndimakhala ndi mwana wanga yemwe adandipatsa. Vuto ndi lakuti ndikamuuza kuti akaonekere kwathu amakana, komanso kwathu sagona. Nditani poti ndikukula tsopano?

NM,

Nsanje.

 

NM,

Cholinga cha ubwenzi chachikulu n’chakuti Mulungu atalola mudzalowe m’banja. Kodi inuyo pochita chibwenzi ndi munthu wokwatira, cholinga chanu nchiyani? Ngati pali chibwenzi pakati pa munthu wokwatira ndi wina wosakwatira kapena ali ndi mwamuna kwina ndipo akugonana, chomenecho ndi chigololo ndipo ndi tchimo pamaso pa Mulungu; palibe za banja.

Mukanena kuti akukana kukaonekera kwanu, inu mumafuna kuti akadzabwera kudzaonekera kwanu abale anu adzati chiyani? Mudziwe kuti chongobwera kudzaonekera kwanu, ndiye kuti mwamunayo akhoza kukhala ngati wavomereza zodzakukwatirani. Kodi mwamunayo ngakhalenso akwanu angalole izi? Fupa lokakamiza silichedwa kuswa mphika, chimodzimodzinso chikondi sakakamiza. Mwamunayo akuonetsa zizindikiro zoti ngakhale anakuchimwitsa pokupatsa mwana ndipo akukulipirira lendi, za banja ndi iwe sakulingalirapo ata! Udakali wam’ngono, yang’ana wina woti ungamange naye banja!

 

Kodi apite?

Gogo wanga,

Ndatha miyezi iwiri ndi mnyamata amene tikugwirizana zodzamanga banja. Komatu ine ndikadali pasukulu ndipo zatsala zaka zinayi kuti ndimalize. Iyeyo wati andidikira koma wanena kuti zingamuvute kudikira ali kuno ndipo wandipempha kuti abapita ku South Africa. Nkhawa yanga ndi yakuti, nanga atati wapita nkukapeza mkazi wina, zidzatha bwanji? Ndamukondatu kotheratu. Ndimulole apite?

JM,

Lilongwe.

 

JM,

Kodi ukuganiza kuti atapeza mkazi wina ngakhale ali konkuno sangatengane naye poona kuchedwa? Izi ndanena chifukwa zomwe akunena kuti apite ku South Africa kaye likhoza kukhala ganizo labwino. Iyeyo utamulola kuti apite ku Joni iwe n’kumaliza sukulu ndiye n’kupezeka kuti wakutaya m’njirayi ungadandaule chiyani? Zikhozatu kutheka kuti iyeyo akhoza kukhala konkuno, molephera kupirira iwe n’kupezeka wapatsidwa mimba tsono zidzakuthandiza chiyani? Mulole apite, chifukwatu zikhozanso kuthandiza kumanga maziko a banja lanu ngati muli oganiza bwino. Chachikulu n’chakuti inu nonse muyenera kudziwa kuti sakupita ku Joniko kukatayitsa nthawi koma kukakonza maziko a banja lanu, monga iwenso ukuchitira popita kusukulu.

 

Amandizunguza

Anatchereza,

Ndidamangitsa ukwati mu 1997 ndipo ndili ndi ana atatu koma mwamuna wanga amandizunza. Ngakhale ndidwale, palibe chimene amachitapo. Komatu ine kwawo ndiye ndimapita pakakhala kalikonse. Mwamuna wangayo ali ndi ana awiri kuchibwenzi. Ndikathetse ukwati kukhoti kapena?

MJT,

Lilongwe.

 

MJT,

Mwamuna wanuyo ngwankhanza komanso wosowa chikondi. Zikuoneka kuti thandizo lalikulu likupita kwa akazi ndi ana a kuchibwenziwo. Itengereni nkhaniyi kwa ankhoswe anu. Ndikhulupirira kuti mudaitengerako kumeneko nkhaniyi, chifukwa pofika munthu kukhala ndi ana awiri apambali inu nkumadziwa simudangokhala chete. Chetechete sautsa nyama, koma suyosuyo.n

Related Articles

Back to top button