Chichewa

Anatchezera

Banja lavuta

Zikomo Anatchereza,

Ndine mayi wa zaka 30 ndipo ndili ndi ana atatu. Kumbuyo kunseku timakhala bwinobwino ngakhale ndimamva kuti amuna anga akuyenda ndi akazi ena. Zimandiwawa koma ndinalibe nazo ntchito. Mu 2014 anzanga omwe ndimayenda nawo onse adali ndi zibwenzi ngakhale adali pabanja ndipo ankandiuza kuti nane ndipeze chibwenzi chamseri koma ndimakana. Kenaka nanenso ndinapeza chibwenzi chamseri, koma amuna anga atadziwa anandimenya kangapo ndipo ndapitako kwathu kambirimbiri mpakana afika saizi yomawakana ana, ati si awo. Ndayesetsa kuwapepesa kunena chilungamo, koma sizikutheka. Tikangoyambana iwowa amanyoza ana anga. Ndiye nditani?

Ndathedwa nzeru,

Mzuzu

Ku Mzuzuko,

Zikomo pondilembera kundiuza nkhawa zanu. Mayi, mavuto enawa timachita kuwaputa dala ife amayi. Choyamba, kodi inu simunamvepo anthu akunena kuti mamveramvera amapasula banja? Ndi zimenezotu! China, munthu umadziwika ndi abwenzi amene umacheza nawo. Ngati umayenda ndi opemphera, nawe ndiye kuti ndi wopemphera; ukamayenda ndi olongolola, nawenso umakhala wolongolola; ukamakondana ndi wamiseche, nawenso ndiye kuti umakonda miseche; kaya wakuba nawenso wakuba…choncho!

Tsono inu mudasankha kuyenda ndi kucheza ndi anzanu oti ali pabanja koma zibwenzi zamseri bwee! Ndiye inu mumati mutani? Simukadachitira mwina, koma kupeza wanu basi! N’kutheka kuti amakuuzani zoti amuna anu ali ndi zibwenzi zamseri ndi anzanu omwewo, nanga inu munagwira nokha kuti akuyenda ndi uje ndi uje? Misechetu imeneyo. Amafuna kuti mukopeke ndipo nanu muyambe kuyenda njira zomwe amayenda anzanu mukunenawo.

Mukadakhala wozindikira si bwenzi mukunena kuti mutamva zoti amuna anu ali ndi zibwenzi zamseri mudalibe nazo ntchito. Chifukwa chiyani? Mukanawafunsa amuna anuwo kuti “kodi zimene ndikumva zoti mukuyenda ndi amayi oyendayenda ndi zoona?” osati zimene mudachita zotchalenja inunso popeza wanu mwamuna wamseri woyenda naye. Atambwali sametana paja! Lero ndi izo, banja lanu lagwedezeka, chikondi ndi kukhulupirirana zazilala. Taonani, amuna anu tsopano ayamba kukaika ngatidi ana anu atatu mudaberekeranawo ndi awodi. Anawo akula ndi chithunzithunzi chotani cha bamboo awo ngati akuwakana? Kuzunza ana osalakwa kumeneko.

Abwenzi ena ndi olakwitsa. Chonde, azimayi, onetsetsani kuti mukuyenda ndi anzanu oyenera, amakhalidwe abwino, aulemu wawo kuti mabanja anu akhalenso aulemu. Mukakhala m’banja zibwenzinso n’zachiyani, abale? Kunja kuno kwaopsa.

Tsono mongokuthandizani pang’ono, ngati banja lanu lili ndi ankhonswe ndi bwino adziwe mavuto anu ndipo mwina akhoza kukuyanjanitsani kuti banja lanu liyambenso kuyenda bwino. Mwinanso ngati mudamanga kumpingo athanso kukuthandizani kumeneko, koma choyamba kwenikweni awirinu muyenera kukhala pansi ndi kupepesana kuchokera pansi pa mtima, maka inuyo chifukwa anzanu ndiwo adakulakwitsani kuti mupange zinthu zosafunika m’banja.

Natchereza

 

Ofuna mabanja

 

Ndine mwamuna wa zaka 27 ndikufuna mkazi woti ndipange naye chibwenzi. Akhale wa zaka 22 – 25 komanso wa ku Lilongwe. 0888 744 670/0994 447 210

 

Ndine mwamuna wa zaka 26 ndikufuna mkazi wa zaka 18-20 woti ndikwatire. 0884 966 815

 

Ndikufuna womanga naye banja, wapantchito kapena wabizinesi. Wotsimikiza aimbe pa 0882 476 331

Related Articles

Back to top button