Anatchezera

Listen to this article

Akukana

banja

Gogo,

Ndidapalana ubwenzi ndi mtsikana wina chaka chatha.

Ndimtsikana wokongola, komanso waulemu.

Chomwe chimandidabwita n’choti ndikamuuza zabanja amakana.

Nditani gogo popeza ndimamukonda kwambiri.

TJK

Zomba

TJK,

Zikomo chifukwa cha funso lako.

Kodi bwenzi lanuyo mudamufunsa kuti afotokoze chifukwa chomwe amakanira banja?

Ndikadakonda mukadafunsa.

Koma akakanitsitsa musamukakamize.

Banja sakakamizani. Musaiwale kuti fupa lokakamiza silichedwa kuswa mphika.

Gogo Natchereza

Ndili ndi zaka 40 ndipo ndikufuna mkazi womanga naye banja.

Ndimagwira ntchito yaulonda, komanso ndili ndi mwana m’modzi.

Amene akufuna ayimbe foni iyi 0887711079.

Ndine mkazi wa zaka 25 ndipo ndikufuna mwamuna womanga naye banja.

Mwamuna amene wasangalasidwa ayimbe foni iyi 0880 315 180.

Ndine mayi wa zaka 26. Ndili ndi ana awiri. Ndimafuna mwamuna womanga naye banja ndipo akhale wa zaka 35.

Wofuna ayimbe pa 0996676261. n

Related Articles

Back to top button
Translate »