Chichewa

Anatchezera

Listen to this article

Takulandiraninso mu 2021

Ndikufuna ndikulandireni m’chaka cha 2021. Chaka chatha lidali thumba la zambiri. M’chakachi zina zidali zokoma, koma zina zokhetsa misonzi.

Tsamba lino lidakambirana nkhani zosiyanasiyana makamaka zokhudza mabanja ndi ubwenzi.

N’zosangalatsa kuti awerengi ena adapeza okondedwa awo kudzera patsambali.

Cholinga chathu n’kutumikira zofuna zanu. Choncho timakondwera inunso mukamakondwera ndi ntchito yomwe tikugwirira.

N’zoona chaka chatha chidali chovuta kaamba ka matenda a Covid-19 omwe adasautsa kwambiri miyoyo ya Amalawi.

Chifukwa cha Covid-19 ena adataya okondedwa awo, ena okondedwa awo adagonekedwa m’chipatala.

Tikudziwa zinkhoswe ndi maukwati ena adakhudzidwa kwambiri chifukwa cha malamulo othandiza kupewa matendawa omwe unduna wa zaumoyo udakhazikitsa.

Tikukhulupirira kuti chaka chatsopanochi chikhala chopambana kwambiri kumbali ya maubwenzi ndi mabanja.

Ndiyamikire awerengi athu omwe amatitumizira mafunso, mauthenga ndi ndemanga.

Ndikulimbikitseni kuti mupitirize chifukwa zimenezi zimatipatsa mangolomera kuti tilimbikire kukutumikirani.

Chaka chabwino, moyo wathanzi!

Gogo Natchereza

Ndili pa moto

Ndidapanga ubwenzi ndi mnyamata wina wa bizinesi wa ku Blantyre komwe inenso ndimakhala.

Mnyamatayu ndimamukonda, iyense amandikonda. Koma vuto ndi loti akungopanga zibwenzi ndi akazi ena.

Kodi gogo nditani chifukwa ndikafuna kuthetsa chibwenzi amakana?

TKK

TKK,

Mnyamatayu samakukonda, mutaye usananong’oneze bondo.

Akadakhala amakukonda sibwenzi akuchita zibwenzi ndi akazi ena.

Ukatsimikiza kuti ubwenzi ukufuna uthe, udzatha ndipo palibe chomwe angachite.

Uyu si mwamuna, koma kamberembere.

Natchereza

Ndikufuna mwamuna

Ndine mayi wa mwana mmodzi wa zaka 25 ndikufuna mwamuna wopemphera woti ndimange naye banja. Amene wasangalatsidwa ayimbe foni iyi 0997 575 015.

Ndine mayi wa zaka 40 wa ana anayi ndipo ndikufuna mwamuna womanga naye banja. Amene akufuna ayimbe foni iyi 0887 711 079. n

Related Articles

Back to top button
Translate »