Chichewa

Anatchezera

Listen to this article

Amandikakamiza

Agogo,

Ndine mtsikana wa zaka 16 ndipo ndili ndi bwenzi langa la zaka 19. Iyeyu amandikakamiza kugonana naye. Ine zimenezo sindimafuna koma ndimalola kupanga naye zimenezo chifukwa ndimamukonda kwambiri ndipo kukana ndimaopa kumukhumudwitsa. Ndiyeno ndipange chiyani kuti mchitidwewu uthe? Zikomo.

 

Wandikhumudwitsa kwambiri, mwana iwe. Pamsinkhu wakowo wayamba kale zogonana ndi anyamata? Zoona? Ndithu, sukula bwino, mwana iwe. Uli pasukulu kodi? Ayi ndithu, siya mchitidwe umenewo ndipo limbikira sukulu ngati uli pasukulu kuti udzakhale ndi moyo wansangala kutsogolo.

Tsono ndikuuze za kuipa kwa zomwe ukuchitazo. Poyamba wati bwenzi lakolo limakukakamiza zogonana, ine ndikuti iweyo ndi amene umafuna! Si wanena wekha kuti umamukonda kwambiri ndipo umaopa kumukhumudwitsa. Zopusa basi! Adakuuza ndani kuti mukakhala pachibwenzi muyenera kugonana poonetsa chikondi chanu? Mathero ake mupatsanapo mimba kapena matenda ndipo zikatero adzangokutaya uko, osakulabadiranso!

Ukatenga mimba usanakhwime pamchombo ndi vuto lalikulu limenelo. Mwina pobereka ukhoza kufa, kapena kung’ambika moti udzakhala ndi matenda aja odzionongera—mikodzo ndi chimbudzi kumatuluka nthawi imodzi usakufuna.

Samala, mwana wanga, kunja kuno kwaopsa ndi matenda a Edzi. Ndiye chimene ungachite apa ungolimba mtima n’kumuuza bwenzi lakolo kuti sukufunanso zogonana chifukwa ino si nthawi yake. Ukamuuza zimenezo mpamene udzadziwe kwenikweni ngati amakukondadi. Ine ndakuuza, koma zonse zili ndi iwe mwini. Ukapanda kumvera usadzati ena sadakuuze!

 

Ali ndi mkazi

Zikomo Anatchereza,

Ine ndi mayi wa zaka 36 ndipo ndili paubwenzi ndi bambo wa zaka 43. Chibwenzi chathu chinayamba mu November chaka chatha ndipo anakaonekera kwathu ngakhale ali ndi mkazi. Akapita kwa mkazi wake pena sayankha ndikamuimbira foni, pena amadula. Ndikamufunsa amati ‘sindinakutsanzike kuti ndikupita kwathu?’. Pano akuti watopa nane. Ndithandizeni, chibwenzichi chipitirire?

Ine GK,

Mulanje

 

GK,

Apa tisatayepo nthawi. Inu, monga mayi wa zaka 36, ndinu wamkulu ndithu ndipo mukudziwa bwino lomwe mmene chibwenzi chimakhalira. Kunena zoona, bambo ameneyo ali pabanja kale ndipo ngati akuti watopa nanu ndiye kuti wathana nanu basi. Chikondi sachita kukakamiza, musiyeni ayende zake ameneyo, akungokuchedwetsani mayi.

Penapake amayi mumaonjeza. Chokhalira paubwenzi ndi munthu woti ali ndi banja lake n’chiyani? Anthu otere nthawi zambiri ndi akamberembere, ongofuna kunjoya ndi akazi ena pozembera akazi awo. Kudzaonekera kwanu amangofuna kukuphakani phula m’maso kuti aoneke ngati ali siliyasi, pamene cholinga chake n’chongofuna kuchita nanu chipako. Mukachita tsoka kuti mwakwatirana nawo amuna otere, si kuti mchitidwe umenewo adzausiya—adzakhala akushashalikabe ndi akazi ena, mathero ake amalowetsa matenda opatsirana kapena Edzi m’yumba!

 

Ofuna mabanja

 

Ndikufuna mkazi womanga naye banja. Akhale wa zaka 19-30 koma akhale wapantchito. 0991 011 933

 

Ndikufuna mkazi wa zaka 21-30 woti ndimange naye banja. Ngati ali ndi ana asapose atatu, akhale wopemphera komanso wapatchito.

0881 836 632

 

Ndine graduate ndipo ndili ndi zaka 25. Ndikufuna mkazi wa zaka 18-24 woti ndimange naye banja. 0885 237 984

 

Ndine mwamuna wa zaka 30 ndikufuna mkazi womanga naye banja. 0884 566 5614

 

Related Articles

Back to top button