ChichewaNkhani

ANATCHEZERA

Mkazi wanga asabwere?

Anatchereza,

Ndili ndi zaka 25 ndipo ndili pantchito yokhalira pomwepo. Ndine wokwatira ndipo ndili mwana mmodzi. Abwana anga aakazi ndi achikulire kwambiri ndithu koma ndikati ndiwapemphe kuti ndiitanitse mkazi wanga kuti tizidzakhala limodzi amakana. Ndichite bwanji pamenepa? Chonde, thandizeni maganizo.

I.J.

Mzuzu

Zikomo IJ,

Ndathokoza chifukwa cha kundilembera kuti ndikuthandizeni maganizo pankhani ya banja lanu. Kodi mudayamba mwawafunsa abwana anuwo kuti n’chifukwa chiyani safuna kuti mkazi wanu abwere kuti muzikhala naye pantchitopo? Ndithu payenera kukhala chifukwa. Kodi abwana anuwo ali ndi amuna awo kapena ali okha? Ndafunsa dala mafunsowa chifukwa mwina akhoza kukuthandizani nokha kudziwa chifukwa chomwe safunira kuti mkazi wanu abwere pakhomopo. Mukandiyankha mafunsowa mwina ndidzatha kukuthandizani bwino pa chomwe mungachite chifukwa pano ndinama poti gwero lake lenileni lomwe amakanira kuti mkazi wanu abwere sindikulidziwa n’komwe. Ndisapupulume kupereka chigamulo pomwe nkhani yonse sindikuidziwa bwino lomwe.

Natchereza

 

Sakundifunanso

Gogo wanga,

Ndidakwatiwa chaka chathachi pambuyo popanga chinkhoswe. Tidakhala m’banja mwezi wathuthunthu osandiuza kuti amamwa ma ARV koma tsiku lina ndidatulira nditapeza mankhwalawo m’mabotolo. Nditamufunsa mwamuna wangayu adayankha kuti: “Pepa mkazi wanga, ndimaopa kuti ndikakuuza ukana kuti tikwatirane. Koma usadandaule chifukwa ndisamala ana ako pamodzi ndi iweyo moyo wanga wonse.”

Timakhalabe ngati banja, koma nditadwala ndidapita kuchipatala komwe adandiuza magazi koma amati zotsatira zake samaziona bwino. Nditapitanso adandiuza kuti ndilibe kachilombo ka HIV ndipo nditamuuza mwamuna wanga adati sakundifunanso banja ati chifukwa ndilibe kachilombo. Nditani? Chonde ndithandizeni.

 

Zina zikamachitika kumangothokoza Mulungu! Mwati mwamuna wanu akuti basi sakukufunaninso banja chifukwa mulibe kachilombo? Zoona? Cholinga chake kuchokera pachiyambi chidali chiyani? Kunena zoona, iyeyu adali ndi kampeni kakuthwa kumphasa—amadziwa bwino lomwe kuti ali ndi kachilombo ka HIV ndipo ndikhoza kunena pano popanda mantha kuti cholinga chake chidali kufalitsa dala kachilomboko. Moyo woipa zedi umenewo.

Kufalitsa dala kachilombo ka HIV kapena matenda ena alionse ndi mlandu waukulu ngati sindikulakwa ndipo munthu wotero ayenera kulangidwa. Ndiye inu mwati mwakayezetsa kawiri konse koma sadakupzeni ndi kachilombo, thokozani Chauta! Tsono ngati akuti sakukufunaninso ukwati, inu vuto lanu n’chiyani? Alibe chikondi ameneyo, musiyeni mudakali moyo. Koma osangomusiyasiya ameneyo, mukamusumire kumabungwe kapena kukhoti kuti chilungamo chioneke mwina ena angatengerepo phunziro.

Natchereza

Related Articles

Back to top button