Wednesday, March 3, 2021
  • About Us
  • ImagiNATION
  • Adverts
  • Rate Card
  • Contact Us
The Nation Online
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Opinion
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Opinion
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
No Result
View All Result
Home Chichewa

ANATCHEZERA

by ANATCHEZERA
13/09/2015
in Chichewa
2 min read
0
Share on FacebookShare on TwitterShare on WhatsAppShare on LinkedinLinkedinShare via Email

Akundikaikira

Anatchereza,

RelatedHeadlines

Mtsutso pa zoika a Covid-19

Amwalira atathawa m’chipatala

‘Osakondera odya nawo K6.2 biliyoni’

Ndine mtsikana wa zaka 17 ndipo ndili Fomu 4. Ndili ndi chibwenzi chomwe ndakhala nacho miyezi 6 ndipo timakondana kwambiri ngakhale anthu amayesetsa kuti tidane poimba foni ndi kutumiza mauthenga a pafoni zam’manja (SMS) pamene sindili naye limodzi. Mnzangayu adayamba wanenapo zogonana kamodzi koma ndinakana ndiye kuyambira pamenepo amati ndiye kuti ndili ndi chibwenzi china chomwe ndimagonana nacho. Ngakhale zili choncho timakondanabe; sanasinthe chikondi chake pa ine ngakhale amalimbikira kunena kuti ndili wina mpaka timafika poyambana. Agogo, nditani kuti asiye kundiganizira zimenezi?

 

Mwana wanga,

Ndasangalala kwambiri chifukwa chondilembera kupempha nzeru kuti ndikuthandize kuti bwenzi lakolo lisiye kukukaikira za chibwenzi china. Choyamba ndikuthokoz kwambiri kuti bwenzi lakolo litakuuza zogonana iwe udakana kugonjera chilakolako cha thupi. Apo wadya 10 pa 10. Umenewo ndiye umunthu, mwana wanga. Atsikana ambiri amsinkhu wako agwa m’mavuto aakulu chifukwa chovomereza kugonana ali pachibwenzi. Zimachitika ndi zambiri mukamagonana nthawi yoteero isanakwane—kutenga mimba, kutenga matenda opatsirana kuphatikizapo Edzi, kulephera kupitirza sukulu ndi zina zotero. Zitakere ndiye kuti wadzionongera tsogolo lako. Ndiye iwe limbikira sukuluyo mpaka upite nayo patali; usalolere zogonanazo mpaka mutalowa m’banja. Ngati cholinga cha chibwenzi chanu n’choti mudzalowe m’banja, mwamuna wako adzakhala wosangalala kwambiri kuti iwe unali wodzisunga kufikira pomwe walowa m’banja. Ukadzangomuvulira ameneyo muli pachibwenzi sadzakhalanso nawe ndi chidwi, ndikuuze. Adzakhala kuti wathana nawe basi ndipo mathero ake adzakusiya. Ndithudi, mtima umenewo usausiye, mwanawe, ndipo kutsogolo udzasimba lokoma!

 

Akuti Ndimusiye

Anatchereza,

Ndithandizeni. Ndili ndi chibwenzi chomwe chimafunitsitsa banja ndipo ndinavomera zochitenga. Koma poyamba mnzanga ndiye adandifunsirira ndiye pano mnzanga yemweyo akuti mkaziyo ngwachisawawa pomwe poyamba nditamufunsa adati ndi mkazi wabwino. Pano akuti ndimusiye ndipo ndikatenge tanga tonse kwa mkaziyo. Nditani pamenepa?

ABWAM,

Chiradzulu

 

ABWAM,

Chibwenzi sachita kufunsirirana. Inu vuto lanu ndi chiyani kuti mnzanu ndiye azichita kukupezerani mkazi wachibwenzi? Chimene chachitika apa ndi chinyengo basi. Mnzanuyo wakuyendani njomba ndipo sindikukaika kuti wayamba kudyerera maso pa mkaziyo. Naye akumufunanso n’chifukwa chake akuti umusiye ndipo ukatenge katundu wako. Koma mwina nditafunsako, kodi inu ndi mkaziyo mudaonanapo n’kuchezerana? Mwakhala pachibwenzi nthawi yaitali bwanji? Inu maganizo anu pa mpaziyo ndi otani? Mnzanuyo akamati mkaziyo ngwachisawawa, akutanthauza chiyani? Zili ndi inu kufufuza kuti mudziwe zoona zake za mkazi muli naye pachibwenziyu musanathamange zothetsa chibwenzi chanu chifukwa mwina payenda dumbo ndi kaduka pamenepa. Nthawi zambiri vuto lotuma mnzako kuti akufunire mkazi kapena mwamuna limakhala ngati limeneli. Mudziwa bwanji kuti pofunsirana kuseriko akukhuthulanso zakukhosi kwawo? Dziwani kuti fumbi ndiwe mwini.

Previous Post

Agundidwa akuthawitsa katundu wakuba

Next Post

Catholics launch Bible Month, study lessons

Related Posts

covid death | The Nation Online
Nkhani

Mtsutso pa zoika a Covid-19

February 28, 2021
death e1465557792659 | The Nation Online
Chichewa

Amwalira atathawa m’chipatala

February 28, 2021
HRDC pursuing this matter further: Trapence
Nkhani

‘Osakondera odya nawo K6.2 biliyoni’

February 27, 2021
Next Post
Msusa: Political violence is bad.

Catholics launch Bible Month, study lessons

Opinions and Columns

My Turn

Unmasking Covid-19 vaccine

March 3, 2021
My Turn

Tackling global slowdowns

March 1, 2021
People’s Tribunal

Burglary at the hill

February 28, 2021
Search Within

Perseverance landed, is alive and well

February 28, 2021

Trending Stories

  • Under probe: The Reserve Bank building in Mzuzu

    Exclusive: RBM’s Mzuzu branch payment mess exposed

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • K5bn Sunbird Waterfront hotel opens May

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Charcoal traffickers fined K800 000, vehicle forfeited

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Economist warns on teachers’ risk allowance

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Why Kamuzu chose 3rd March as Martyrs’ Day in Malawi

    7 shares
    Share 7 Tweet 0
  • Values
  • Our Philosophy
  • Editorial policy
  • Advertising Policy
  • Code of Conduct
  • Plagiarism disclaimer
  • Disclaimer
  • Privacy Policy
  • Terms of use

© 2021 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Opinion
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation

© 2020 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

This website uses cookies. By continuing to use this website you are giving consent to cookies being used. Visit our Privacy and Cookie Policy.