Nkhani

Andale agundika misonkhano, osapewa Covid-19

Listen to this article

M’sabatayi, anthu ena 5 adapezeka ndi kachirombo ka coronavirus m’dziko muno, kuchititsa kuti chiwerengero cha anthuwo chifike pa 63. Chiopsezo cha nthendayi chikukulirakulira.

Koma zikuoneka kuti andale sakusamala za izi, pomwe akuchititsa misonkhano mosalabadira kuti nkhani ya gulu ndi chinyezi chofalitsa matendawa.

Atangopereka zikalata zawo kwa wapampando wa bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) Jane Ansah, Lazarus Chakwera yemwe akutsatizana ndi Saulos Chilima mumgwirizano wa zipani za Malawi Congress Party (MCP) ndi UTM Party adazungulira mumzinda wa Blantyre komwe chikhamu chimasonkhana, osapereka mpata wokhala mita imodzi.

Ndipo atapereka zikalata zawo, mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika yemwe akuimira zipani za Democratic Progressive Party (DPP) ndi womutsatira wake Atupele Muluzi wa United Democratic Front (UDF) nawo adazungulira mumzindawo mosalabadira za khamu lofikako.

Ndipo Lamulungu, Chakwera ndi Chilima adachititsa msonkhano kubwalo la Mzuzu Upper Stadium, pomwe Muluzi adali pamisonkhano yoimaima kuchoka ku chigawo cha kumwera mpaka pakati. Monsemo, kudalibe kutsata ndondomeko yotalikana.

Koma akadaulo ena pa zaumoyo ndi ndale ati zipanizi zikuika miyoyo ya anthu pachiswe chifukwa matenda a Covid-19 ndi oopsa.

Kadaulo pa zaumoyo Maziko Matemba wati ndale zili apo, atsogoleri a zipani akuyenera kutsatidwa.

“Kampeni imayenera kutha pa 30 June koma chifukwa choti tsiku la chisankho silinaikidwe, onse okhudzidwa ayenera kudziwa kuti kapmeni iyenera kutha masiku kuchokera tsiku la chisankho,” adatero iye.

Koma kadaulo wa malamulo Sunduzwayo Madise adati MEC ili ndi udindo wosankha tsiku la chisankho, monga lichitira posankha tsiku la chisankho chapadera.

“Nyumba ya Malamulo idakhazikitsa tsiku pofuna kutsata malamulo a chisankho kuti psakhale chisokonezo chifukwa nkhani ya chisankho cha patatu chiyenera kutsatidwa. Koma MEC ili ndi mphamvu yokhazikitsa masiku atsopano, monga imachitira pakakhala chisankho chapadera cha aphungu kapena makhansala,” adatero Madise.

Wapampando wa komiti ya zamalamulo ku Nyumba ya Malamulo Kezzie Msukwa adati adzidzimuka ndi nkhaniyi.

“N’zodabwitsa kuti MEC ikufuna kuti chisankho chidzakhaleko pa 23 June,” adatero Msukwa.

Ndipo m’sabatayi, akachenjede a zamalamulo apempha

Mutharika kuti alemekeze chisankhocho pochotsa makomishona a MEC omwe bwalo lamilandu

lidawapeza kuti sadayendetse bwino chisankho cha pa 21 May 2019.

Mmodzi mwa akachenjedewa, Garton Kamchedzera wa ku Chancellor College adati anthu ali tcheru kuyembekeza tsiku lomwe Mutharika adzachotse makomishonala n’kusankha ena.

“N’chifukwa chiyani sakufuna kutula pansi maudindo? Ndikuona kuti zikanakhala bwino akanatula maudindo awo pa okha. Kupanda kutero, anthu okhanza kupanga chiganizo pazosatira za chisankho chomwe chikubwerachi ndipo kupitirira kukhalabe maofesi sikovomerezeka m’malamulo. Ndipo Mutharika akuyenera kuchitapo kanthu pogwiritsa ntchito section 75 ya malamulo.”

Gawo 75 ndime 4 imaperka mphamvu kwa mtsogoleri wa dzko kudzera kubungwe la Public Appointment Committee (PAC) ya ku Nyumba ya Malamulo ikapeza kuti komishoniyo ilibe kuthekera koyendetsa masankho.

Mipando ya makomishonayo itha pa 5 June pomwe iwo akwaniritse ndime yawo.

Related Articles

Back to top button
Translate »